Akolose
3 Komabe, ngati munaukitsidwa+ limodzi ndi Khristu, pitirizani kufuna zinthu zakumwamba,+ kumene Khristu wakhala kudzanja lamanja la Mulungu.+ 2 Ikani maganizo anu pa zinthu zakumwamba,+ osati pa zinthu zapadziko.+ 3 Pakuti munafa,+ ndipo moyo+ wanu wabisidwa mwa Khristu mogwirizana+ ndi Mulungu. 4 Khristuyo, amene ndiye moyo wathu,+ akadzaonetsedwa,+ inunso mudzaonetsedwa limodzi naye mu ulemerero.+
5 Choncho chititsani ziwalo za thupi+ lanu padziko lapansi kukhala zakufa+ ku dama, zinthu zodetsa, chilakolako cha kugonana,+ chikhumbo choipa, ndi kusirira kwa nsanje,+ kumene ndiko kulambira mafano. 6 Chifukwa cha zinthu zimenezi, mkwiyo wa Mulungu ukubwera.+ 7 Inunso munayendapo m’zinthu zimenezi, pamene munali kukhalira kuchita zomwezo.+ 8 Koma tsopano zonsezo muzitaye kutali ndi inu.+ Mutaye mkwiyo, kupsa mtima, kuipa, ndi mawu achipongwe,+ ndipo pakamwa panu pasatuluke nkhani zotukwana.+ 9 Musamanamizane.+ Vulani umunthu+ wakale pamodzi ndi ntchito zake, 10 ndipo muvale umunthu watsopano+ umene Mulungu amapereka, kutanthauza kuti mwa kudziwa zinthu molondola, muchititse umunthu wanu kukhala watsopano mogwirizana ndi chifaniziro+ cha Mulungu. 11 Mukatero, sipadzakhala Mgiriki kapena Myuda, kudulidwa kapena kusadulidwa, mlendo, Msukuti, kapolo, kapena mfulu,+ koma Khristu ndiye zinthu zonse ndipo ali mwa onse.+
12 Chotero monga ochita kusankhidwa ndi Mulungu,+ oyera ndi okondedwa, valani chifundo+ chachikulu, kukoma mtima, kudzichepetsa,+ kufatsa,+ ndi kuleza mtima.+ 13 Pitirizani kulolerana ndi kukhululukirana ndi mtima wonse,+ ngati wina ali ndi chifukwa chodandaulira+ za mnzake. Monga Yehova* anakukhululukirani+ ndi mtima wonse, inunso teroni. 14 Koma kuwonjezera pa zonsezi, valani chikondi,+ pakuti chimagwirizanitsa anthu mwamphamvu+ kwambiri kuposa chinthu china chilichonse.
15 Komanso, mtendere+ wa Khristu ulamulire m’mitima+ yanu, popeza munaitanidwa ku mtenderewo monga ziwalo za thupi limodzi.+ Ndiponso, sonyezani kuti ndinu oyamikira. 16 Mawu a Khristu akhazikike mwa inu ndipo akupatseni nzeru zonse.+ Pitirizani kuphunzitsana+ ndi kulangizana mwa masalimo,+ nyimbo zotamanda Mulungu, ndi nyimbo zauzimu+ zogwira mtima. Pitirizani kuimbira Yehova+ m’mitima yanu. 17 Ndipo chilichonse chimene mukuchita m’mawu kapena mu ntchito,+ muzichita zonse m’dzina la Ambuye Yesu,+ ndipo muziyamika+ Mulungu Atate kudzera mwa iye.
18 Inu akazi, muzigonjera+ amuna anu, pakuti zimenezi ndiye zoyenera kwa anthu otsatira Ambuye. 19 Inu amuna, musaleke kukonda akazi+ anu ndipo musamawapsere mtima kwambiri.+ 20 Ananu, muzimvera+ makolo anu pa zinthu zonse, pakuti kuchita zimenezi kumakondweretsa Ambuye. 21 Inu abambo, musamakwiyitse ana+ anu, kuti angakhale okhumudwa. 22 Inu akapolo, muzimvera ambuye anu a padziko lapansi+ pa zinthu zonse, osati mwachiphamaso ngati ofuna kukondweretsa+ anthu, koma moona mtima ndiponso moopa Yehova.+ 23 Chilichonse chimene mukuchita, muzichichita ndi moyo wanu wonse+ ngati kuti mukuchitira Yehova,+ osati anthu, 24 chifukwa mukudziwa kuti mudzalandira cholowa+ kuchokera kwa Yehova+ monga mphoto yanu. Tumikirani Ambuye wanu, Khristu, monga akapolo.+ 25 Ndithudi, amene akuchita zolakwa adzalandiranso+ zolakwa zake zimene akuchitazo, chifukwa Mulungu sakondera.+