25 Bilidadi+ wa ku Shuwa anayankha kuti:
2 “Ulamuliro komanso mphamvu zochititsa mantha ndi zake.
Iye amakhazikitsa mtendere kumwamba.
3 Kodi nʼzotheka kuwerenga asilikali ake?
Ndipo ndi ndani amene saona kuwala kwake?
4 Choncho, kodi munthu angakhale bwanji wolungama pamaso pa Mulungu,+
Kapena kodi munthu wobadwa kwa mkazi angakhale bwanji wosalakwa?+
5 Ngakhale mwezi si wowala kwa iye
Ndipo nyenyezi si zoyera mʼmaso mwake,
6 Ndiye kuli bwanji munthu yemwe ndi mphutsi,
Komanso mwana wa munthu yemwe ndi nyongolotsi?”