Salimo
BUKU LA 5
(Masalimo 107-150)
107 Yamikani Yehova, chifukwa iye ndi wabwino.+
Chikondi chake chokhulupirika chidzakhalapobe mpaka kalekale.+
2 Anthu amene Yehova anawawombola anene zimenezi,
Anthu amene anawawombola mʼmanja mwa mdani,*+
3 Anthu amene anawasonkhanitsa pamodzi kuchokera mʼmayiko osiyanasiyana,+
Kuchokera kumʼmawa komanso kumadzulo,*
Kuchokera kumpoto komanso kumʼmwera.+
4 Iwo ankayendayenda mʼchipululu mopanda kanthu.
Sanapeze njira yopita kumzinda woti azikhalamo.
5 Anali ndi njala komanso ludzu.
Anafooka kwambiri chifukwa chotopa.
8 Anthu ayamike Yehova+ chifukwa cha chikondi chake chokhulupirika,
Ndiponso chifukwa cha ntchito zake zodabwitsa zimene wachitira ana a anthu.+
10 Ena ankakhala mumdima wandiweyani,
Anali akaidi amene ankavutika atamangidwa maunyolo.
12 Choncho Mulungu anawagwetsera mavuto kuti akhale ndi mtima wodzichepetsa.+
Iwo anapunthwa ndipo panalibe wowathandiza.
13 Iwo anaitana Yehova kuti awathandize mʼmasautso awo,
Ndipo iye anawapulumutsa ku mavuto awo.
15 Anthu ayamike Yehova chifukwa cha chikondi chake chokhulupirika,+
Ndiponso chifukwa cha ntchito zake zodabwitsa zimene wachitira ana a anthu.
19 Iwo ankaitana Yehova kuti awathandize mʼmasautso awo.
Ndipo iye ankawapulumutsa ku mavuto awo.
21 Anthu ayamike Yehova chifukwa cha chikondi chake chokhulupirika,
Ndiponso chifukwa cha ntchito zake zodabwitsa zimene wachitira ana a anthu.
23 Anthu amene amayenda panyanja mʼsitima,
Amene amachita malonda pamadzi ambiri,+
24 Iwo aona ntchito za Yehova,
Ndiponso ntchito zake zodabwitsa mʼmadzi akuya.+
25 Aona mmene mawu ake amayambitsira mphepo yamkuntho,+
Nʼkuchititsa mafunde panyanja.
26 Mafundewo amakweza anthuwo mʼmwamba
Kenako amawatsitsa pansi pakati pa nyanja.
Kulimba mtima kwawo kumatha chifukwa cha tsoka limene akuliyembekezera.
27 Amayenda peyupeyu ndipo amadzandira ngati munthu woledzera,
Ndipo luso lawo lonse limakhala lopanda ntchito.+
30 Iwo amasangalala mafundewo akatha,
Ndipo Mulungu amawatsogolera kudoko limene iwo akufuna.
31 Anthu ayamike Yehova chifukwa cha chikondi chake chokhulupirika,
Ndiponso chifukwa cha ntchito zake zodabwitsa zimene wachitira ana a anthu.+
33 Amasandutsa mitsinje kukhala chipululu,
Ndiponso akasupe a madzi kukhala malo ouma.+
34 Nthaka yobala zipatso amaisandutsa dziko lopanda chonde,+
Chifukwa cha kuipa kwa anthu okhala mmenemo.
39 Koma iwo anakhala ochepa ndipo anachititsidwa manyazi
Chifukwa choponderezedwa, masoka komanso chisoni.
40 Mulungu amachititsa manyazi anthu olemekezeka
Ndipo amawachititsa kuti azingoyendayenda mʼchipululu mmene mulibe njira.+