Masalimo
BUKU LACHISANU
(Masalimo 107 – 150)
107 Yamikani Yehova anthu inu, pakuti iye ndi wabwino.+
Kukoma mtima kwake kosatha kudzakhalapobe mpaka kalekale.+
2 Anthu owomboledwa a Yehova anene zimenezi,+
Anthu amene iye wawawombola m’manja mwa mdani,+
3 Anthu amene anawasonkhanitsa pamodzi kuchokera m’mayiko osiyanasiyana,+
Kuchokera kotulukira dzuwa kukafika kolowera dzuwa,+
Kuchokera kumpoto kukafika kum’mwera.+
4 Iwo anayendayenda m’chipululu+ mopanda kanthu.+
Sanapeze njira iliyonse yopita kumzinda woti azikhalamo.+
6 Iwo anapitiriza kufuulira Yehova m’masautso awo,+
Ndipo anawalanditsa ku mavuto awo.+
7 Anawayendetsa m’njira yabwino,+
Kuti akafike kumzinda woti azikhalamo.+
8 Anthu ayamike Yehova chifukwa cha kukoma mtima kwake kosatha,+
Ndiponso chifukwa cha ntchito zake zodabwitsa zimene wachitira ana a anthu.+
10 Ena anali kukhala mu mdima, mu mdima wandiweyani,+
Anali akaidi osautsika ndi omangidwa maunyolo,+
11 Chifukwa anachita zinthu mopandukira+ mawu a Mulungu,+
Ndipo ananyoza malangizo a Wam’mwambamwamba.+
12 Choncho mwa kuwadzetsera mavuto, Mulungu anagonjetsa mitima yawo.+
Iwo anapunthwa ndipo panalibe wowathandiza.+
13 Iwo anayamba kuitana Yehova kuti awathandize m’masautso awo,+
Ndipo iye anawapulumutsa ku mavuto awo monga mwa nthawi zonse.+
15 Anthu ayamike Yehova chifukwa cha kukoma mtima kwake kosatha,+
Ndiponso chifukwa cha ntchito zake zodabwitsa zimene wachitira ana a anthu.+
17 Anthu amene anali opusa chifukwa cha njira yawo yophwanya malamulo,+
Komanso chifukwa cha zolakwa zawo, pamapeto pake anadzibweretsera masautso.+
19 Iwo anayamba kuitana Yehova kuti awathandize m’masautso awo.+
Ndipo iye anawapulumutsa ku mavuto awo monga mwa nthawi zonse.+
21 Anthu ayamike Yehova chifukwa cha kukoma mtima kwake kosatha,+
Ndiponso chifukwa cha ntchito zake zodabwitsa zimene wachitira ana a anthu.+
23 Anthu amene amayenda m’zombo panyanja,+
Amene amachita malonda pamadzi ambiri,+
24 Amenewa ndi amene aona ntchito za Yehova,+
Ndiponso ntchito zake zodabwitsa m’madzi akuya.+
25 Aona mmene amautsira mphepo yamkuntho mwa kungonena mawu,+
Moti nyanjayo imachita mafunde.+
27 Amadzandira ndipo amayenda peyupeyu ngati munthu woledzera,+
Ndipo ngakhale nzeru zawo zonse zimasokonezeka.+
30 Iwo amasangalala chifukwa mafundewo atha,
Ndipo Mulungu amawatsogolera kudoko limene iwo akufuna.+
31 Anthu ayamike Yehova chifukwa cha kukoma mtima kwake kosatha,+
Ndiponso chifukwa cha ntchito zake zodabwitsa zimene wachitira ana a anthu.+
33 Amasandutsa mitsinje kukhala chipululu,+
Ndiponso akasupe a madzi kukhala malo opanda madzi.+
34 Nthaka yobala zipatso amaisandutsa dziko lamchere,+
Chifukwa cha kuipa kwa anthu okhala mmenemo.
35 Amasandutsa chipululu kukhala dambo la madzi,+
Ndipo dziko lopanda madzi amalisintha kukhala dera la akasupe amadzi.+
40 Mulungu akutsanulira mnyozo pa anthu olemekezeka,+
Moti iye akuwachititsa kuyendayenda m’chipululu, mmene mulibe njira.+