1 Samueli
31 Afilisiti anayamba kumenyana ndi Aisiraeli+ ndipo asilikali a Isiraeli ankathawa moti ambiri anaphedwa mʼphiri la Giliboa.+ 2 Afilisiti anayandikira kwambiri Sauli ndi ana ake ndipo kenako anapha Yonatani,+ Abinadabu ndi Malikisuwa, ana aamuna a Sauli.+ 3 Nkhondo inamʼkulira kwambiri Sauli, moti oponya mivi ndi uta anamupeza nʼkumuvulaza koopsa.+ 4 Kenako Sauli anauza womunyamulira zida kuti: “Solola lupanga lako undibaye kuti anthu osadulidwawa+ asandipeze nʼkundipha mwankhanza.” Koma womunyamulira zidayo sankafuna chifukwa ankachita mantha kwambiri. Choncho Sauli anatenga lupanga lake nʼkuligwera.+ 5 Womunyamulira zidayo ataona kuti Sauli wafa,+ nayenso anagwera lupanga lake ndipo anafera limodzi. 6 Choncho Sauli, ana ake atatu, womunyamulira zida komanso asilikali ake onse anafera limodzi pa tsikuli.+ 7 Aisiraeli amene ankakhala kuchigwa ndiponso mʼdera la Yorodano ataona kuti asilikali a Isiraeli athawa komanso kuti Sauli ndi ana ake afa, anachoka mʼmizinda yawo nʼkuthawa.+ Kenako Afilisiti anabwera kudzakhala mʼmizindayo.
8 Tsiku lotsatira, Afilisiti atabwera kudzatenga zinthu za anthu amene anaphedwa, anapeza Sauli ndi ana ake atatu atafa paphiri la Giliboa.+ 9 Iwo anadula mutu wa Sauli nʼkumuvula zida zake. Kenako anauza anthu mʼdziko lonse la Afilisiti kuti afalitse uthengawu+ mʼnyumba* za mafano awo+ ndiponso kwa anthu awo. 10 Kenako anakaika zida zakezo mʼnyumba ya zifaniziro za Asitoreti ndipo anapachika mtembo wake pakhoma la mzinda wa Beti-sani.+ 11 Anthu a ku Yabesi-giliyadi+ atamva zimene Afilisiti anamuchita Sauli, 12 asilikali onse ananyamuka nʼkuyenda usiku wonse ndipo anakachotsa mtembo wa Sauli ndi mitembo ya ana ake pakhoma la mzinda wa Beti-sani. Kenako anabwerera ku Yabesi nʼkutentha mitemboyo kumeneko. 13 Atatero, anatenga mafupa awo+ nʼkuwaika mʼmanda pansi pa mtengo wa bwemba ku Yabesi+ ndipo anasala kudya masiku 7.