-
Hoseya 9:10Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
10 “Isiraeli ndinamupeza ali ngati mphesa zam’chipululu.+ Ndinaona makolo a anthu inu ali ngati nkhuyu zoyambirira pamtengo wa mkuyu wongoyamba kumene kubereka.+ Iwo anapita kwa Baala wa ku Peori+ ndipo anadzipereka kwa chinthu chochititsa manyazicho.+ Anakhala onyansa ngati chinthu chimene anali kuchikondacho.+
-