6 Manase anatentha ana ake aamuna pamoto+ m’chigwa cha mwana wa Hinomu,+ ndipo ankachita zamatsenga,+ ankawombeza,+ ankachita zanyanga,+ ndiponso anaika anthu olankhula ndi mizimu+ ndi olosera zam’tsogolo.+ Iye anachita zinthu zambiri zoipa pamaso pa Yehova ndiponso zomukwiyitsa.+