Levitiko
19 Yehova anapitiriza kulankhula ndi Mose kuti: 2 “Uza khamu lonse la ana a Isiraeli kuti, ‘Mukhale oyera,+ chifukwa ine Yehova Mulungu wanu ndine woyera.+
3 “‘Aliyense wa inu aziopa mayi ndi bambo ake,+ ndipo muzisunga masabata anga.+ Ine ndine Yehova Mulungu wanu. 4 Musatembenukire kwa milungu yopanda pake,+ ndipo musadzipangire milungu yachitsulo chosungunula.+ Ine ndine Yehova Mulungu wanu.
5 “‘Mukamapereka nsembe yachiyanjano kwa Yehova,+ muziipereka m’njira yakuti Mulungu akuyanjeni.+ 6 Muzidya nyama yoperekedwa nsembeyo pa tsiku limene mwaipereka ndi tsiku lotsatira, koma yotsala kufikira tsiku lachitatu muziitentha pamoto.+ 7 Ngati munthu wadya nyamayo pa tsiku lachitatu, wadya nyama yonyansa.+ Mulungu sadzalandira nsembe imeneyo.+ 8 Ndipo munthu wodya nyamayo aziyankha mlandu wa cholakwa chakecho,+ chifukwa waipitsa chinthu chopatulika cha Yehova. Munthu wotero aziphedwa kuti asakhalenso pakati pa anthu amtundu wake.
9 “‘Mukamakolola zinthu za m’munda mwanu, musamachotseretu zonse m’mphepete mwa mundawo, ndipo musamachite khunkha m’munda mwanumo.+ 10 Komanso, musamakolole mphesa zotsala+ za m’munda mwanu, ndipo musamatole mphesa zimene zamwazika m’munda mwanu. Zimenezo muzisiyira wovutika ndi mlendo wokhala pakati panu.+ Ine ndine Yehova Mulungu wanu.
11 “‘Musabe,+ musanamizane+ ndipo aliyense asachitire mnzake chinyengo.+ 12 Musamalumbire zabodza m’dzina langa+ ndi kuipitsa dzina la Mulungu wanu. Ine ndine Yehova. 13 Usabere mnzako mwachinyengo+ ndipo usafwambe aliyense.+ Malipiro a munthu waganyu asagone m’nyumba mwako kufikira m’mawa.+
14 “‘Usatemberere munthu wogontha, ndipo usaikire munthu wakhungu chinthu chopunthwitsa.+ Uziopa Mulungu wako.+ Ine ndine Yehova.
15 “‘Musamaweruze mopanda chilungamo. Musamakondere munthu wosauka,+ ndiponso musamakondere munthu wolemera.+ Mnzako uzimuweruza mwachilungamo.
16 “‘Usamayendeyende pakati pa anthu amtundu wako n’kumachita miseche.+ Usachite kanthu kalikonse kuti uphetse mnzako.+ Ine ndine Yehova.
17 “‘Usadane ndi m’bale wako mumtima mwako.+ Mnzako um’dzudzule ndithu+ kuti usasenze naye tchimo.
18 “‘Usabwezere choipa+ kapena kusungira chakukhosi anthu amtundu wako.+ Uzikonda mnzako mmene umadzikondera wekha.+ Ine ndine Yehova.
19 “‘Malamulo angawa muziwasunga: Musakweranitse ziweto zanu zosiyana. Pobzala mbewu m’munda mwanu musasakanize mitundu iwiri yosiyana.+ Ndipo musamavale chovala cha ulusi wa mitundu iwiri yosakaniza.*+
20 “‘Mwamuna akagona ndi mtsikana wantchito wofunsiridwa ndi mwamuna wina, ndipo mkaziyo sanawomboledwe m’njira ina iliyonse kapena kupatsidwa ufulu, pazikhala chilango. Iwo asaphedwe chifukwa mkaziyo anali asanakhale mfulu. 21 Mwamunayo azibweretsa kwa Yehova nkhosa yamphongo ya nsembe ya kupalamula+ pakhomo la chihema chokumanako. 22 Ndiyeno wansembe aziphimba tchimo limene munthuyo wachita. Azitero popereka kwa Yehova nkhosa yamphongo ya nsembe ya kupalamula ija. Pamenepo munthuyo azikhululukidwa tchimo lakelo.+
23 “‘Mukafika m’dziko limene mukupita n’kubzala mtengo uliwonse wa zipatso, muziuona ngati wosadulidwa, ndipo zipatso zake zizikhala zodetsedwa kwa inu. Muziona mtengowo kukhala wosadulidwa kwa zaka zitatu ndipo musamadye zipatso zake. 24 Koma m’chaka chachinayi zipatso zake zonse+ zizikhala zoyera ndipo muzizipereka kwa Yehova+ pa chikondwerero chachikulu. 25 M’chaka chachisanu, muzidya zipatso zake ndipo mtengowo udzakuberekerani zipatso zochuluka.+ Ine ndine Yehova Mulungu wanu.
26 “‘Musadye chilichonse limodzi ndi magazi.+
“‘Musaombeze*+ ndipo musachite zamatsenga.+
27 “‘Musamete ndevu zanu zotsikira m’masaya ndipo musadule nsonga za ndevu zanu.*+
28 “‘Musamadzicheke chifukwa cha munthu wakufa,+ ndipo musamadziteme zizindikiro. Ine ndine Yehova.
29 “‘Musaipitse mwana wanu wamkazi mwa kum’sandutsa hule,+ kuti dziko lingachite uhule ndi kudzaza makhalidwe otayirira.+
30 “‘Muzisunga masabata anga+ ndipo muziopa malo anga opatulika.+ Ine ndine Yehova.
31 “‘Musatembenukire kwa olankhula ndi mizimu+ ndipo musafunsire olosera zam’tsogolo+ ndi kudetsedwa nawo. Ine ndine Yehova Mulungu wanu.
32 “‘Anthu aimvi uziwagwadira,+ munthu wachikulire uzim’patsa ulemu+ ndipo uziopa Mulungu wako.+ Ine ndine Yehova.
33 “‘Munthu wokhala m’dziko lanu monga mlendo musam’chitire zoipa.+ 34 Mlendo wokhala pakati panu muzimuona ngati mbadwa. Muzim’konda mmene mumadzikondera nokha,+ chifukwa inunso munali alendo m’dziko la Iguputo.+ Ine ndine Yehova Mulungu wanu.
35 “‘Musamaweruze mopanda chilungamo.+ Musamachite chinyengo poyeza utali wa chinthu, kulemera kwa chinthu+ kapena poyeza zinthu zamadzi. 36 Muzikhala ndi masikelo olondola,+ miyala yolondola yoyezera kulemera kwa zinthu, muyezo wolondola wa efa ndi muyezo wolondola wa hini.* Ine ndine Yehova Mulungu wanu, amene ndinakutulutsani m’dziko la Iguputo. 37 Muzisunga malangizo anga onse ndi zigamulo zanga zonse, ndipo muzizitsatira.+ Ine ndine Yehova.’”