-
1 Samueli 17:25Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
25 Pamenepo amuna a Isiraeli anayamba kunena kuti: “Mukumuona mwamuna amene akubwerayu? Iye akubwera kudzatonza+ Isiraeli. Munthu amene angamukanthe ndi kumupha, mfumu idzam’patsa chuma chochuluka ndi kum’patsanso mwana wake wamkazi.+ Komanso, mfumu idzamasula nyumba ya bambo ake a munthuyo kuti isamapereke chilichonse mwa zinthu zimene Aisiraeli ayenera kupereka kwa mfumu.”+
-
-
1 Samueli 18:27Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
27 Davide pamodzi ndi asilikali ake ananyamuka, ndipo anakapha+ amuna 200 achifilisiti. Ndiyeno Davide anabwerako atatenga makungu awo a kunsonga,+ ndipo makungu onsewo anawapereka kwa mfumu kuti achite naye mgwirizano wa ukwati. Pamenepo Sauli anapereka Mikala, mwana wake wamkazi, kwa Davide kuti akhale mkazi wake.+
-