Numeri 23:19 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 19 Mulungu si munthu, woti anganene mabodza,+Si mwana wa munthu, woti angadzimve kuti ali ndi mlandu.+Kodi ananenapo kanthu koma osachita,Analankhulapo kanthu kodi koma osakwaniritsa?+ 1 Samueli 2:31 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 31 Tsopano imva izi, masiku adzafika pamene ndidzadula dzanja lako ndi la nyumba ya kholo lako, moti m’nyumba yako simudzakhala munthu wokalamba.+ Yesaya 46:11 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 11 Ine ndi amene ndidzaitane mbalame yodya nyama kuchokera kotulukira dzuwa.+ Ndidzaitana munthu kuti adzachite zolingalira zanga kuchokera kutali.+ Ineyo ndalankhula ndipo ndidzazichita.+ Ndakonza zimenezi ndipo ndidzazichitadi.+ Yesaya 55:11 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 11 ndi mmenenso adzakhalire mawu otuluka pakamwa panga.+ Sadzabwerera kwa ine popanda kukwaniritsa cholinga chake,+ koma adzachitadi zimene ine ndikufuna+ ndipo adzakwaniritsadi zimene ndinawatumizira.+ Zekariya 1:6 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 6 Kodi zimene ndinalamula atumiki anga aneneri+ m’mawu anga ndi m’malangizo anga, sizinawachitikire makolo anu?’+ Chotero iwo anabwerera kwa ine ndi kunena kuti: ‘Yehova wa makamu watichitira zimene anakonza kuti atichitire+ mogwirizana ndi njira zathu ndi zochita zathu.’”+
19 Mulungu si munthu, woti anganene mabodza,+Si mwana wa munthu, woti angadzimve kuti ali ndi mlandu.+Kodi ananenapo kanthu koma osachita,Analankhulapo kanthu kodi koma osakwaniritsa?+
31 Tsopano imva izi, masiku adzafika pamene ndidzadula dzanja lako ndi la nyumba ya kholo lako, moti m’nyumba yako simudzakhala munthu wokalamba.+
11 Ine ndi amene ndidzaitane mbalame yodya nyama kuchokera kotulukira dzuwa.+ Ndidzaitana munthu kuti adzachite zolingalira zanga kuchokera kutali.+ Ineyo ndalankhula ndipo ndidzazichita.+ Ndakonza zimenezi ndipo ndidzazichitadi.+
11 ndi mmenenso adzakhalire mawu otuluka pakamwa panga.+ Sadzabwerera kwa ine popanda kukwaniritsa cholinga chake,+ koma adzachitadi zimene ine ndikufuna+ ndipo adzakwaniritsadi zimene ndinawatumizira.+
6 Kodi zimene ndinalamula atumiki anga aneneri+ m’mawu anga ndi m’malangizo anga, sizinawachitikire makolo anu?’+ Chotero iwo anabwerera kwa ine ndi kunena kuti: ‘Yehova wa makamu watichitira zimene anakonza kuti atichitire+ mogwirizana ndi njira zathu ndi zochita zathu.’”+