9 Iwe mkazi amene ukubweretsa uthenga wabwino wonena za Ziyoni,+ kwera phiri lalitali.+ Lankhula mwamphamvu ndiponso mofuula, iwe mkazi amene ukubweretsa uthenga wabwino wonena za Yerusalemu.+ Fuula! Usachite mantha.+ Uza mizinda ya ku Yuda kuti: “Uyu ndiye Mulungu wanu.”+