Zekariya
11 “Iwe Lebanoni,+ tsegula zitseko zako kuti moto utenthe mitengo yako ya mkungudza.+ 2 Lira mofuula, iwe mtengo wofanana ndi mkungudza, chifukwa chakuti mtengo wa mkungudza wagwa, ndiponso mitengo ikuluikulu yawonongedwa.+ Lirani mofuula, inu mitengo ikuluikulu ya ku Basana, chifukwa nkhalango yowirira kwambiri ija yawonongedwa.+ 3 Tamverani! Abusa akulira mofuula+ chifukwa ulemerero wawo watha.+ Tamverani! Mikango yamphamvu ikubangula mofuula chifukwa nkhalango zowirira, za m’mphepete mwa mtsinje wa Yorodano zawonongedwa.+
4 “Yehova Mulungu wanga wanena kuti, ‘Weta nkhosa zanga zimene zinayenera kuphedwa.+ 5 Amene anazigula anazipha+ koma sanaimbidwe mlandu.+ Amene akuzigulitsa+ akunena kuti: “Yehova atamandike pamene ine ndikupeza chuma.”+ Abusa ake sazichitira chifundo ngakhale pang’ono.’+
6 “‘Sindidzachitiranso chifundo anthu okhala m’dzikoli,’+ watero Yehova. ‘Choncho ine ndichititsa aliyense kuti aponderezedwe ndi mnzake+ ndiponso mfumu yake.+ Iwo adzawononga dzikoli, ndipo ine sindidzapulumutsa aliyense m’manja mwawo.’”+
7 Choncho ine ndinayamba kuweta nkhosa+ zimene zinayenera kuphedwa,+ ndipo ndinachita zimenezi chifukwa cha inu, anthu osautsika a m’gulu la nkhosali.+ Chotero ndinatenga ndodo ziwiri.+ Imodzi ndinaipatsa dzina lakuti Wosangalatsa.+ Inayo ndinaipatsa dzina lakuti Mgwirizano,+ ndipo ndinayamba kuweta gulu la nkhosalo. 8 Kenako ndinachotsa abusa atatu m’mwezi umodzi+ chifukwa sindinathenso kuleza nawo mtima,+ ndipo iwonso ananyansidwa nane. 9 Pambuyo pake ndinanena kuti: “Ndileka kukuwetani.+ Amene akufa, afe.+ Amene akuwonongeka, awonongeke. Otsalawo adyane.”+ 10 Choncho ndinatenga ndodo yanga yotchedwa Wosangalatsa+ ija ndi kuithyolathyola.+ Ndinachita izi kuti ndithetse pangano limene ndinapangana ndi anthu a mtundu wanga.+ 11 Panganolo linasweka pa tsiku limenelo. Mwa njira imeneyi, nkhosa zosautsika+ zimene zinali kundiona+ zinadziwa kuti zimene ndachitazo n’zimene Yehova ananena.
12 Kenako ndinawauza kuti: “Ngati mukuona kuti n’zoyenera,+ ndipatseni malipiro anga, koma ngati mukuona kuti n’zosayenera musandipatse.” Pamenepo iwo anandipatsa ndalama 30 zasiliva monga malipiro anga.+
13 Zitatero Yehova anandiuza kuti: “Kaziponye mosungiramo chuma.+ Zimenezi ndi ndalama za mtengo wapatali zimene akuona kuti angandigule nazo.”+ Choncho ndinatenga ndalama 30 zasilivazo n’kukaziponya mosungiramo chuma panyumba ya Yehova.+
14 Kenako ndinathyolathyola ndodo yanga yachiwiri ija yotchedwa Mgwirizano+ kuti ndithetse ubale+ wa Yuda ndi Isiraeli.+
15 Ndiyeno Yehova anandiuza kuti: “Tenga zida za m’busa wopanda pake.+ 16 Pakuti ndilola kuti m’dzikoli mukhale m’busa wina.+ M’busa ameneyu sadzasamala nkhosa zimene zikuwonongeka.+ Nkhosa yaing’ono sadzaifunafuna, ndipo yothyoka sadzaichiritsa.+ Nkhosa yotha kuima yokha sadzaipatsa chakudya, ndipo adzadya nyama ya nkhosa yonenepa.+ Iye adzakupula ziboda za nkhosazo.+ 17 Tsoka m’busa wanga wopanda pake+ amene akusiya nkhosa.+ Lupanga lidzamutema padzanja ndi kuboola diso lake la kudzanja lamanja. Dzanja lake lidzafota,+ ndipo diso lake la kudzanja lamanja lidzachita mdima.”