-
Ekisodo 29:1, 2Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
29 “Uchite izi kuti uwayeretse kuti atumikire monga ansembe anga: Utenge ngʼombe yaingʼono yamphongo ndi nkhosa ziwiri zamphongo zopanda chilema.+ 2 Utengenso mkate wopanda zofufumitsa, mkate wozungulira woboola pakati wopanda zofufumitsa, wothira mafuta komanso timitanda ta mkate topyapyala topanda zofufumitsa, topaka mafuta.+ Uzipange ndi ufa wa tirigu wosalala.
-
-
Ekisodo 29:40, 41Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
40 Popereka mwana wa nkhosa woyamba, uzipereka limodzi ndi ufa wosalala, muyezo wake gawo limodzi mwa magawo 10 a muyezo wa efa,* wothira mafuta oyenga bwino kwambiri okwana gawo limodzi mwa magawo 4 a muyezo wa hini,* ndi gawo limodzi mwa magawo 4 a vinyo wa nsembe yachakumwa. 41 Uzipereka mwana wa nkhosa wachiwiri madzulo kuli kachisisira.* Uzimupereka pamodzi ndi nsembe yambewu komanso nsembe yachakumwa ngati mmene unachitira mʼmawa. Uzipereke kuti zikhale kafungo kosangalatsa,* nsembe yowotcha pamoto yoperekedwa kwa Yehova.
-
-
Numeri 28:4, 5Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
4 Mwana wa nkhosa mmodzi wamphongo muzimupereka nsembe mʼmamawa. Ndipo mwana wa nkhosa wamphongo winayo, muzimupereka nsembe madzulo kuli kachisisira.*+ 5 Muzipereka nsembezi limodzi ndi ufa wosalala wokwana gawo limodzi mwa magawo 10 a muyezo wa efa,* kuti ikhale nsembe yambewu. Ufawo muziuthira mafuta oyenga bwino kwambiri okwana gawo limodzi mwa magawo 4 a muyezo wa hini.*+
-