-
Levitiko 6:20, 21Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
20 “Iyi ndi nsembe imene Aroni ndi ana ake ayenera kupereka kwa Yehova pa tsiku limene akudzozedwa:+ ufa wosalala wokwana gawo limodzi mwa magawo 10 a muyezo wa efa*+ uzikhala nsembe yambewu+ yoperekedwa nthawi zonse. Hafu ya ufawo azipereka mʼmamawa ndipo hafu inayo madzulo. 21 Nsembeyo izikhala yophika ndi mafuta mʼchiwaya.+ Izikhala yosakaniza bwino ndi mafuta. Uzipereka mitanda yophika ya nsembe yambewu monga kafungo kosangalatsa* kwa Yehova.
-