-
Deuteronomo 24:14, 15Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
14 Musamabere mwachinyengo waganyu yemwe ndi wovutika ndiponso wosauka, kaya akhale mmodzi wa abale anu kapena mlendo amene akukhala mʼdziko lanu, amene ali mʼmizinda yanu.*+ 15 Muzimupatsa malipiro ake tsiku lomwelo dzuwa lisanalowe,+ chifukwa iye ndi wosauka ndipo akudalira malipiro ake omwewo kuti akhale ndi moyo. Mukapanda kutero adzafuula kwa Yehova chifukwa cha zimene inuyo mwamuchitira ndipo mudzapezeka kuti mwachimwa.+
-