-
1 Mafumu 2:8, 9Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
8 Ndiye palinso Simeyi wa ku Bahurimu, mwana wa Gera wa fuko la Benjamini. Iyeyu anandilankhula mawu onyoza kwambiri+ tsiku limene ndinkapita ku Mahanaimu.+ Koma atabwera kudzakumana nane pa Yorodano, ndinamulumbirira pamaso pa Yehova kuti: ‘Sindidzakupha ndi lupanga.’+ 9 Iweyo usangomusiya, umulange,+ poti ndiwe munthu wanzeru ndipo ukudziwa zimene uyenera kumuchita. Uchite zoti imvi zake zipite ku Manda* zili ndi magazi.”+
-