-
1 Mbiri 22:14Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
14 Ndayesetsa mwakhama kusonkhanitsa golide womangira nyumba ya Yehova wokwana matalente* 100,000 ndi siliva wokwana matalente 1 miliyoni. Koma nʼzosatheka kuyeza kulemera kwa kopa ndi zitsulo+ chifukwa nʼzochuluka kwambiri. Ndasonkhanitsanso matabwa ndi miyala+ pokonzekera, koma udzawonjezerapo zina.
-
-
2 Mbiri 4:18-22Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
18 Solomo anapanga ziwiya zimenezi zambiri. Kopayo sanadziwike kulemera kwake.+
19 Solomo anapanga zinthu zonse+ zapanyumba ya Mulungu woona. Anapanga guwa lansembe lagolide,+ matebulo+ oikapo mkate wachionetsero+ 20 ndi zoikapo nyale ndi nyale zake zagolide woyenga bwino,+ zoti aziziyatsa pafupi ndi mʼchipinda chamkati mogwirizana ndi malamulo ake. 21 Anapanganso maluwa agolide, nyale zagolide ndi zopanira zagolide zozimitsira nyale ndipo golide wake anali woyengedwa bwino kwambiri. 22 Komanso anapanga zozimitsira nyale, mbale zolowa, makapu ndi zopalira moto. Zonsezi zinali zagolide woyenga bwino. Anapanganso khomo lolowera mʼnyumbayo, zitseko zamkati za Chipinda Choyera Koposa+ ndi zitseko za nyumbayo. Zonsezi zinali zagolide.+
-