-
1 Samueli 8:11-18Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
11 Iye anawauza kuti: “Munthu amene adzakhale mfumu yanuyo azidzachita izi:+ Azidzatenga ana anu+ kuti azikayenda mʼmagaleta ake+ ndiponso kukwera pamahatchi* ake.+ Ena mwa ana anuwo azidzathamanga patsogolo pa magaleta ake. 12 Adzaika anthu ena kuti akhale atsogoleri a magulu a anthu 1,000+ ndi atsogoleri a magulu a anthu 50.+ Ena azidzalima minda yake,+ kukolola mbewu zake+ ndiponso kupanga zida zake zankhondo ndi zida zogwiritsa ntchito pamagaleta ake.+ 13 Ana anu aakazi adzawatenga kuti azikapanga mafuta onunkhira komanso azikaphika mikate ndi zakudya zina.+ 14 Adzakulandani malo anu abwino kwambiri komanso minda yanu ya mpesa ndi ya maolivi+ nʼkupatsa antchito ake. 15 Adzatenganso gawo limodzi la magawo 10 alionse a zokolola zamʼminda yanu ya mpesa komanso mʼminda ya mbewu zina nʼkuzipereka kwa nduna zake ndi antchito ake. 16 Komanso adzatenga antchito anu aamuna, antchito anu aakazi, abusa anu abwino kwambiri ndi abulu anu kuti azikawagwiritsa ntchito.+ 17 Pa ziweto zanu 10 zilizonse adzatengapo chiweto chimodzi+ ndipo inuyo mudzakhala antchito ake. 18 Tsiku lina mudzalira chifukwa chosankha kukhala ndi mfumu,+ koma Yehova sadzakuyankhani.”
-