-
2 Samueli 24:18-23Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
18 Kenako Gadi anapita kwa Davide tsiku lomwelo nʼkukamuuza kuti: “Pitani mukamangire Yehova guwa lansembe pamalo opunthira mbewu a Arauna wa Chiyebusi.”+ 19 Choncho Davide anapitadi mogwirizana ndi mawu a Gadi komanso mogwirizana ndi zimene Yehova analamula. 20 Arauna atasuzumira panja anaona mfumu ndi atumiki ake akubwera. Nthawi yomweyo Arauna anatuluka nʼkugwada pamaso pa mfumu ndipo anawerama mpaka nkhope yake kufika pansi. 21 Arauna anafunsa kuti: “Nʼchifukwa chiyani inu mbuyanga mfumu mwabwera kwa ine mtumiki wanu?” Davide anayankha kuti: “Ndabwera kudzagula malo ako opunthira mbewu. Ndikufuna kumangira Yehova guwa lansembe, kuti mliri umene uli pakati pa anthuwu uthe.”+ 22 Koma Arauna anauza Davide kuti: “Mbuyanga mfumu, tengani malowo ndipo mupereke chilichonse chimene mukuona kuti nʼchabwino. Ngʼombe iyi ikhale nsembe yopsereza ndipo chopunthira ndi zipangizo zinazi zikhale nkhuni. 23 Ine Arauna ndikukupatsani zonsezi mfumu.” Kenako Arauna anauza mfumu kuti: “Yehova Mulungu wanu asonyeze kuti akusangalala nanu.”
-