Levitiko 18:5 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 5 Muzisunga malamulo anga ndi zigamulo zanga. Aliyense amene akuchita zimenezi adzakhala ndi moyo chifukwa cha malamulo ndi zigamulo zimenezo.+ Ine ndine Yehova. Deuteronomo 5:16 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 16 Muzilemekeza bambo anu ndi mayi anu+ mogwirizana ndi zimene Yehova Mulungu wanu anakulamulani, kuti mukhale ndi moyo nthawi yaitali komanso kuti zinthu zikuyendereni bwino mʼdziko limene Yehova Mulungu wanu akukupatsani.+ Yesaya 55:3 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 3 Tcherani khutu lanu ndipo mubwere kwa ine.+ Mverani ndipo mudzapitiriza kukhala ndi moyo,Ndithu ine ndidzachita nanu pangano limene lidzakhalepo mpaka kalekale+Lokhudza chikondi chokhulupirika chimene ndinalonjeza Davide. Lonjezo limeneli ndi lodalirika.+ Yohane 12:50 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 50 Ndipo ndikudziwa kuti lamulo lake ndi lothandiza anthu kudzapeza moyo wosatha.+ Choncho zimene ndimalankhula, ndimazilankhula mogwirizana ndi zimene Atate andiuza.”+
5 Muzisunga malamulo anga ndi zigamulo zanga. Aliyense amene akuchita zimenezi adzakhala ndi moyo chifukwa cha malamulo ndi zigamulo zimenezo.+ Ine ndine Yehova.
16 Muzilemekeza bambo anu ndi mayi anu+ mogwirizana ndi zimene Yehova Mulungu wanu anakulamulani, kuti mukhale ndi moyo nthawi yaitali komanso kuti zinthu zikuyendereni bwino mʼdziko limene Yehova Mulungu wanu akukupatsani.+
3 Tcherani khutu lanu ndipo mubwere kwa ine.+ Mverani ndipo mudzapitiriza kukhala ndi moyo,Ndithu ine ndidzachita nanu pangano limene lidzakhalepo mpaka kalekale+Lokhudza chikondi chokhulupirika chimene ndinalonjeza Davide. Lonjezo limeneli ndi lodalirika.+
50 Ndipo ndikudziwa kuti lamulo lake ndi lothandiza anthu kudzapeza moyo wosatha.+ Choncho zimene ndimalankhula, ndimazilankhula mogwirizana ndi zimene Atate andiuza.”+