Levitiko
18 Yehova anapitiriza kulankhula ndi Mose kuti: 2 “Uza Aisiraeli kuti, ‘Ine ndine Yehova Mulungu wanu.+ 3 Musamachite zinthu zimene anthu a ku Iguputo kumene munkakhala amachita, komanso musamachite zinthu zimene anthu amʼdziko la Kanani limene ndikukupititsani amachita.+ Ndipo musamakatsatire malamulo awo. 4 Muzisunga zigamulo zanga komanso muzitsatira malamulo anga.+ Ine ndine Yehova Mulungu wanu. 5 Muzisunga malamulo anga ndi zigamulo zanga. Aliyense amene akuchita zimenezi adzakhala ndi moyo chifukwa cha malamulo ndi zigamulo zimenezo.+ Ine ndine Yehova.
6 Mwamuna aliyense pakati panu asayandikire wachibale wake aliyense kuti agone naye.*+ Ine ndine Yehova. 7 Usagone ndi bambo ako komanso usagone ndi mayi ako. Amenewo ndi mayi ako ndipo usagone nawo.
8 Usagone ndi mkazi wa bambo ako,+ chifukwa kuchita zimenezo nʼkuchititsa manyazi bambo ako.*
9 Usagone ndi mchemwali wako, kaya ndi mwana wamkazi wa bambo ako kapena mwana wamkazi wa mayi ako. Kaya munabadwira mʼbanja limodzi kapena anabadwira mʼbanja lina.+
10 Usagone ndi mwana wamkazi wa mwana wako wamwamuna kapena mwana wamkazi wa mwana wako wamkazi, chifukwa kumeneko nʼkudzichititsa manyazi.
11 Usagone ndi mwana wamkazi wa mkazi wa bambo ako, mwana wa bambo ako, chifukwa ameneyo ndi mchemwali wako.
12 Usagone ndi mchemwali wa bambo ako. Ameneyo ndi wachibale wa bambo ako.+
13 Usagone ndi mchemwali wa mayi ako, chifukwa ndi wachibale wa mayi ako.
14 Usachititse manyazi mchimwene wa bambo ako* mwa kugona ndi mkazi wake, chifukwa amenewo ndi mayi ako.+
15 Usagone ndi mpongozi wako wamkazi.+ Iye ndi mkazi wa mwana wako, choncho usagone naye.
16 Usagone ndi mkazi wa mchimwene wako,+ chifukwa kumeneko nʼkuchititsa manyazi* mchimwene wako.
17 Usagone ndi mkazi limodzi ndi mwana wake wamkazi.+ Usatenge mwana wamkazi wa mwana wamwamuna wa mkazi wakoyo komanso mwana wamkazi wa mwana wake wamkazi kuti ugone naye. Limeneli ndi khalidwe lonyansa* chifukwa amenewa ndi achibale a mkazi wako.
18 Ukakwatira mkazi usakwatirenso mchemwali wake kuti akhale mkazi wako wachiwiri,+ nʼkumagona naye mchemwali wakeyo ali moyo.
19 Usayandikire mkazi kuti ugone naye pa nthawi imene akusamba chifukwa ndi wodetsedwa.+
20 Usagone ndi mkazi wa mnzako nʼkukhala wodetsedwa.+
21 Usalole kuti aliyense mwa ana ako aperekedwe* kwa Moleki.+ Usanyoze dzina la Mulungu wako mwa njira imeneyi.+ Ine ndine Yehova.
22 Usagone ndi mwamuna ngati mmene umagonera ndi mkazi.+ Zimenezi nʼzonyansa.
23 Mwamuna asamagone ndi nyama nʼkukhala wodetsedwa, ndipo mkazi asamadzipereke kwa nyama kuti agone nayo.+ Kuchita zimenezi nʼkosemphana ndi chibadwa.
24 Musamadzidetse ndi chilichonse cha zinthu zimenezi, chifukwa mitundu imene ndikuithamangitsa pamaso panu yadzidetsa ndi makhalidwe onyansawa.+ 25 Nʼchifukwa chake dzikolo ndi lodetsedwa, ndipo ndidzalilanga chifukwa cha zolakwa zake moti dzikolo lidzalavula anthu ake kunja.+ 26 Koma inu muzisunga malamulo anga ndi zigamulo zanga.+ Ndipo aliyense wa inu, kaya ndi nzika kapena mlendo wokhala pakati panu, asamachite chilichonse cha zinthu zonyansa zimenezi.+ 27 Chifukwa anthu amene ankakhala mʼdzikolo inu musanafike ankachita zinthu zonyansa zimenezi,+ ndipo panopa dzikolo ndi lodetsedwa. 28 Mukapewa kuchita zimenezi, dziko silidzakulavulani chifukwa cholidetsa ngati mmene lidzalavulire mitundu imene ikukhalamo inu musanafike. 29 Aliyense wa inu akadzachita chilichonse cha zinthu zonyansazi, adzaphedwa kuti asadzakhalenso pakati pa anthu ake. 30 Choncho muzisunga malamulo anga popewa kuchita miyambo yonyansa iliyonse imene anthu akhala akuchita inu musanafike,+ kuti musadzidetse ndi miyamboyo. Ine ndine Yehova Mulungu wanu.’”