-
Danieli 2:34, 35Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
34 Munapitiriza kuyangʼana mpaka mwala unadulidwa kuphiri koma osati ndi manja a munthu. Mwalawo unamenya chifanizirocho kumapazi ake achitsulo chosakanikirana ndi dongo nʼkuwaphwanya.+ 35 Pa nthawi imeneyo chitsulo, dongo, kopa, siliva ndi golide, zonse zinaphwanyikaphwanyika ndipo zinakhala ngati mankhusu* apamalo opunthirapo mbewu mʼchilimwe. Mphepo inaziuluza moti sizinaonekenso. Koma mwala umene unamenya chifanizirocho unakhala phiri lalikulu ndipo linadzaza dziko lonse lapansi.
-