Salimo 147:2 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 2 Yehova akumanga Yerusalemu.+Akusonkhanitsa pamodzi Aisiraeli amene anapita ku ukapolo.+ Yesaya 56:8 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 8 Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, amene akusonkhanitsa pamodzi Aisiraeli omwe anabalalitsidwa,+ wanena kuti: “Ine ndidzamusonkhanitsira anthu ena kuwonjezera pa anthu ake amene anasonkhanitsidwa kale.”+ Ezekieli 34:12 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 12 Ndidzasamalira nkhosa zanga ngati mʼbusa amene wapeza nkhosa zake zimene zinabalalika ndipo akuzidyetsa.+ Ndidzazipulumutsa mʼmalo onse amene zinabalalikira pa tsiku la mitambo ndi mdima wandiweyani.+ Ezekieli 34:16 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 16 “Nkhosa imene yasowa ndidzaifunafuna,+ imene yasochera ndidzaibweza. Imene yavulala ndidzaimanga povulalapo ndipo imene ili yofooka ndidzailimbitsa, koma yonenepa ndi yamphamvu ndidzaiwononga. Ndidzaipatsa chiweruzo kuti chikhale chakudya chake.” Ezekieli 37:21 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 21 Ndiye uwauze kuti, ‘Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti: “Ine nditenga Aisiraeli kuchokera kwa anthu a mitundu ina kumene anapita. Ndidzawasonkhanitsa pamodzi kuchokera kumbali zonse ndipo ndidzawabweretsa mʼdziko lawo.+ Zefaniya 3:19 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 19 Pa nthawiyo ndidzalanga onse amene akukupondereza,+Ndipo ndidzapulumutsa wotsimphina.+Ndidzasonkhanitsa anthu amene anabalalitsidwa.+ Ndidzachititsa kuti akhale otchuka* komanso azitamandidwa,Mʼdziko lonse limene anachititsidwa manyazi.
8 Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, amene akusonkhanitsa pamodzi Aisiraeli omwe anabalalitsidwa,+ wanena kuti: “Ine ndidzamusonkhanitsira anthu ena kuwonjezera pa anthu ake amene anasonkhanitsidwa kale.”+
12 Ndidzasamalira nkhosa zanga ngati mʼbusa amene wapeza nkhosa zake zimene zinabalalika ndipo akuzidyetsa.+ Ndidzazipulumutsa mʼmalo onse amene zinabalalikira pa tsiku la mitambo ndi mdima wandiweyani.+
16 “Nkhosa imene yasowa ndidzaifunafuna,+ imene yasochera ndidzaibweza. Imene yavulala ndidzaimanga povulalapo ndipo imene ili yofooka ndidzailimbitsa, koma yonenepa ndi yamphamvu ndidzaiwononga. Ndidzaipatsa chiweruzo kuti chikhale chakudya chake.”
21 Ndiye uwauze kuti, ‘Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti: “Ine nditenga Aisiraeli kuchokera kwa anthu a mitundu ina kumene anapita. Ndidzawasonkhanitsa pamodzi kuchokera kumbali zonse ndipo ndidzawabweretsa mʼdziko lawo.+
19 Pa nthawiyo ndidzalanga onse amene akukupondereza,+Ndipo ndidzapulumutsa wotsimphina.+Ndidzasonkhanitsa anthu amene anabalalitsidwa.+ Ndidzachititsa kuti akhale otchuka* komanso azitamandidwa,Mʼdziko lonse limene anachititsidwa manyazi.