-
Mateyu 14:24-33Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
24 Pa nthawiyi nʼkuti ngalawa ija itapita kutali* pakati pa madzi, ndipo inkakankhidwa mwamphamvu ndi mafunde chifukwa ankalimbana ndi mphepo yamphamvu. 25 Koma pa ulonda wa 4* mʼbandakucha, iye anafika kwa ophunzirawo akuyenda pamwamba pa madzi. 26 Ophunzirawo atamuona akuyenda panyanjapo, anachita mantha nʼkunena kuti: “Amenewa ndi masomphenya ndithu!” Ndipo anafuula mwamantha. 27 Koma nthawi yomweyo Yesu anawauza kuti: “Mtima mʼmalo, ndine. Musachite mantha.”+ 28 Ndiyeno Petulo anayankha kuti: “Ambuye, ngati ndinudi ndiuzeni ndiyende pamadzipa ndibwere kuli inuko.” 29 Iye anamuuza kuti: “Bwera!” Choncho Petulo anatsika mʼngalawamo nʼkuyenda pamadzi kupita kumene kunali Yesu. 30 Koma ataona mphepo yamkuntho, anachita mantha. Atayamba kumira anafuula kuti: “Ambuye, ndipulumutseni!” 31 Nthawi yomweyo Yesu anatambasula dzanja lake nʼkumugwira ndipo anamuuza kuti: “Wachikhulupiriro chochepa iwe, nʼchifukwa chiyani wakayikira?”+ 32 Atakwera mʼngalawa, mphepo yamkuntho ija inasiya. 33 Pamenepo amene anali mʼngalawamo anamugwadira nʼkunena kuti: “Ndinudi Mwana wa Mulungu.”
-
-
Yohane 6:16-21Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
16 Chakumadzulo ndithu, ophunzira ake anapita kunyanja.+ 17 Iwo anakwera ngalawa nʼkuyamba kuwoloka nyanja kulowera ku Kaperenao. Pa nthawiyi nʼkuti mdima utagwa ndipo Yesu anali asanabwerebe kwa iwo.+ 18 Komanso nyanja inayamba kuchita mafunde chifukwa kunkawomba mphepo yamphamvu.+ 19 Koma atapalasa makilomita pafupifupi 5 kapena 6,* anaona Yesu akuyenda panyanja kuyandikira ngalawayo ndipo iwo anachita mantha. 20 Koma Yesu anawauza kuti: “Ndine, musachite mantha!”+ 21 Kenako anamulola kuti akwere mʼngalawa yawo, ndipo nthawi yomweyo ngalawa ija inakafika kumtunda kumene ankapita.+
-