-
Maliko 6:47-51Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
47 Kunja kutada, ngalawa ija inali ili pakati pa nyanja, koma iye anali yekha kumtunda.+ 48 Ataona ophunzirawo akupalasa movutika chifukwa cholimbana ndi mphepo yamphamvu, iye anawalondola akuyenda panyanja. Uwu unali mʼbandakucha pafupifupi pa ulonda wa 4.* Koma ophunzirawo ankaona ngati akufuna kuwapitirira. 49 Atamuona akuyenda panyanjapo ophunzirawo anaganiza kuti: “Amenewa ndi masomphenya ndithu!” Ndipo anafuula mokweza. 50 Anachita zimenezi chifukwa onsewo anamuona ndipo anachita mantha. Koma nthawi yomweyo iye anawauza kuti: “Mtima mʼmalo, ndine. Musachite mantha.”+ 51 Ndiyeno Yesu anakwera nawo mʼngalawamo ndipo mphepoyo inaleka. Ataona zimenezi anadabwa kwambiri.
-