-
Danieli 7:13, 14Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
13 Ndinapitiriza kuona masomphenya usikuwo ndipo ndinaona winawake wooneka ngati mwana wa munthu+ akubwera mʼmitambo. Iye analoledwa kufika kwa Wamasiku Ambiri+ uja ndipo anamubweretsa pafupi kwambiri ndi Wamasiku Ambiriyo. 14 Kenako anamupatsa ulamuliro,+ ulemu+ ndi ufumu kuti anthu a mitundu yonse komanso anthu olankhula zilankhulo zosiyanasiyana azimutumikira.+ Ulamuliro wake udzakhalapo mpaka kalekale ndipo sudzatha. Ufumu wake sudzawonongedwa.+
-
-
Mateyu 6:9-13Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
9 Koma inu muzipemphera chonchi:+
‘Atate wathu wakumwamba, dzina lanu+ liyeretsedwe.*+ 10 Ufumu wanu ubwere.+ Zofuna zanu+ zichitike padziko lapansi pano ngati mmene zilili kumwamba.+ 11 Mutipatse chakudya chimene* tikufunikira lero.+ 12 Mutikhululukire zolakwa* zathu chifukwa ifenso takhululukira amene atilakwira.*+ 13 Tithandizeni kuti tisagonje tikamayesedwa,*+ koma mutiteteze kwa woipayo.’+
-