Mateyu 20:26, 27 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 26 Sizikuyenera kukhala choncho pakati panu.+ Koma aliyense amene akufuna kuti akhale wamkulu pakati panu akuyenera kukhala mtumiki wanu+ 27 ndipo amene akufuna kuti akhale woyamba pakati panu akuyenera kukhala kapolo wanu.+ Luka 9:48 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 48 Ndiyeno anawauza kuti: “Aliyense amene walandira mwana wamngʼono ngati uyu mʼdzina langa walandiranso ine. Ndipo aliyense amene walandira ine walandiranso amene anandituma.+ Chifukwa aliyense amene amachita zinthu ngati mwana wamngʼono pakati panu ndi amene ali wamkulu.”+ Luka 22:26 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 26 Inu musakhale otero.+ Koma amene ali wamkulu kwambiri pa nonsenu akhale ngati wamngʼono+ kwambiri pa nonsenu, ndipo amene ali mtsogoleri akhale ngati wotumikira. Aroma 12:10 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 10 Pokonda abale, muzikhala ndi chikondi chenicheni. Pa nkhani yosonyezana ulemu, muziyamba ndi inuyo.+ 1 Petulo 5:5 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 5 Chimodzimodzinso inu achinyamata, muzigonjera amuna achikulire.*+ Komanso nonsenu muzichitirana zinthu modzichepetsa* chifukwa Mulungu sasangalala ndi anthu odzikuza. Koma anthu odzichepetsa amawasonyeza kukoma mtima kwake kwakukulu.+
26 Sizikuyenera kukhala choncho pakati panu.+ Koma aliyense amene akufuna kuti akhale wamkulu pakati panu akuyenera kukhala mtumiki wanu+ 27 ndipo amene akufuna kuti akhale woyamba pakati panu akuyenera kukhala kapolo wanu.+
48 Ndiyeno anawauza kuti: “Aliyense amene walandira mwana wamngʼono ngati uyu mʼdzina langa walandiranso ine. Ndipo aliyense amene walandira ine walandiranso amene anandituma.+ Chifukwa aliyense amene amachita zinthu ngati mwana wamngʼono pakati panu ndi amene ali wamkulu.”+
26 Inu musakhale otero.+ Koma amene ali wamkulu kwambiri pa nonsenu akhale ngati wamngʼono+ kwambiri pa nonsenu, ndipo amene ali mtsogoleri akhale ngati wotumikira.
10 Pokonda abale, muzikhala ndi chikondi chenicheni. Pa nkhani yosonyezana ulemu, muziyamba ndi inuyo.+
5 Chimodzimodzinso inu achinyamata, muzigonjera amuna achikulire.*+ Komanso nonsenu muzichitirana zinthu modzichepetsa* chifukwa Mulungu sasangalala ndi anthu odzikuza. Koma anthu odzichepetsa amawasonyeza kukoma mtima kwake kwakukulu.+