-
Aefeso 1:13, 14Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
13 Koma inunso munakhala ndi chiyembekezo mwa iye mutamva mawu a choonadi, omwe ndi uthenga wabwino wonena za chipulumutso chanu. Mutakhulupirira, Mulungu anagwiritsa ntchito mzimu woyera umene analonjeza kuti akuikeni chidindo+ ndipo anagwiritsa ntchito Khristu kuti achite zimenezi. 14 Mzimu woyerawo uli ngati chikole chotsimikizira kuti tidzalandira zimene Mulungu watilonjeza.+ Mulungu anachita zimenezi nʼcholinga choti apereke dipo+ kuti anthu ake amasulidwe.+ Zimenezi zidzachititsa kuti atamandidwe komanso kupatsidwa ulemerero.
-