-
Deuteronomo 4:25, 26Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
25 Mukakakhala ndi ana komanso zidzukulu ndipo mukakakhala nthawi yaitali mʼdzikomo, nʼkuchita zinthu zokuwonongetsani popanga chifaniziro chosema+ cha chinthu chilichonse, nʼkuchita choipa pamaso pa Yehova Mulungu wanu, moti nʼkumukhumudwitsa,+ 26 ndikutenga kumwamba ndi dziko lapansi lero monga mboni zokutsutsani, kuti mudzafa mwamsanga mʼdziko limene mukupita kukalitenga mutawoloka Yorodano. Simudzakhala mʼdzikomo kwa nthawi yaitali chifukwa mudzawonongedwa ndithu.+
-