-
Mateyu 8:28, 29Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
28 Atafika kutsidya linalo, mʼdera la Agadara, anakumana ndi amuna awiri ogwidwa ndi ziwanda akuchokera mʼmanda.*+ Amunawa anali ochititsa mantha kwambiri moti panalibe aliyense amene ankalimba mtima kudutsa msewu umenewo. 29 Nthawi yomweyo iwo anafuula kuti: “Kodi mukufuna chiyani kwa ife, Mwana wa Mulungu?+ Kodi mwabwera kudzatipatsa chilango+ nthawi yoikidwiratu isanakwane?”+
-