-
1 Timoteyo 3:2, 3Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
2 Choncho woyangʼanira ayenera kukhala wopanda chifukwa chomunenezera, mwamuna wa mkazi mmodzi, wosachita zinthu mopitirira malire, woganiza bwino,+ wochita zinthu mwadongosolo, wochereza alendo+ ndiponso wodziwa kuphunzitsa.+ 3 Asakhale munthu womwa mowa mwauchidakwa,+ kapena wankhanza,* koma wololera.+ Asakhalenso wokonda kukangana+ kapena wokonda ndalama.+
-