Deuteronomo
27 Ndiyeno Mose pamodzi ndi akulu a Isiraeli analamula anthuwo kuti: “Muzisunga lamulo lililonse limene ndikukupatsani lero. 2 Ndipo tsiku limene muwoloke Yorodano nʼkulowa mʼdziko limene Yehova Mulungu wanu akukupatsani, mukaimike miyala ikuluikulu nʼkuipanga pulasitala.*+ 3 Kenako mukakawoloka, mukalembe pamiyalapo mawu onse a mʼChilamulo ichi, kuti mulowe mʼdziko limene Yehova Mulungu wanu akukupatsani, dziko loyenda mkaka ndi uchi, mogwirizana ndi zimene Yehova, Mulungu wa makolo anu anakulonjezani.+ 4 Mukawoloka Yorodano, mukaimike miyala imeneyi paphiri la Ebala,+ ndipo mukaipange pulasitala,* mogwirizana ndi zimene ndikukulamulani lero. 5 Komanso mukamangire Yehova Mulungu wanu guwa lansembe kumeneko, guwa lansembe lamiyala. Musakaseme miyalayo ndi chipangizo chilichonse chachitsulo.+ 6 Mukagwiritse ntchito miyala yathunthu pomangira Yehova Mulungu wanu guwa lansembe, ndipo mukapereke nsembe zopsereza kwa Yehova Mulungu wanu paguwalo. 7 Mukapereke nsembe zamgwirizano+ nʼkuzidyera pamenepo,+ ndipo mukasangalale pamaso pa Yehova Mulungu wanu.+ 8 Ndipo mukalembe moonekera bwino pamiyalayo mawu onse a mʼChilamulo chimenechi.”+
9 Kenako Mose komanso ansembe omwe ndi Alevi analankhula ndi Aisiraeli onse kuti: “Aisiraeli inu, khalani chete ndi kumvetsera. Lero mwakhala anthu a Yehova Mulungu wanu.+ 10 Muzimvera mawu a Yehova Mulungu wanu ndi kusunga malamulo+ ndi malangizo ake, amene ndikukupatsani lero.”
11 Tsiku limenelo Mose analamula anthuwo kuti: 12 “Mukawoloka Yorodano, mafuko otsatirawa ndi amene adzaimirire paphiri la Gerizimu+ nʼkudalitsa anthu: Fuko la Simiyoni, Levi, Yuda, Isakara, Yosefe ndi Benjamini. 13 Ndipo mafuko otsatirawa ndi amene adzaimirire paphiri la Ebala+ kuti azidzavomereza matemberero akamadzatchulidwa: Fuko la Rubeni, Gadi, Aseri, Zebuloni, Dani ndi Nafitali. 14 Ndipo Alevi azidzalankhula mokweza kwa anthu onse a mu Isiraeli kuti:+
15 ‘Wotembereredwa ndi munthu aliyense wopanga chifaniziro chosema+ kapena chifaniziro chachitsulo+ nʼkuchibisa.* Chifanizirocho, chomwe ndi ntchito ya manja a mmisiri waluso,* ndi chonyansa kwa Yehova.’+ (Anthu onse azidzayankha kuti, ‘Zikhale momwemo!’*)
16 ‘Wotembereredwa ndi munthu wonyoza bambo ake kapena mayi ake.’+ (Anthu onse azidzayankha kuti, ‘Zikhale momwemo!’)
17 ‘Wotembereredwa ndi munthu wosuntha chizindikiro cha malire a mnzake.’+ (Anthu onse azidzayankha kuti, ‘Zikhale momwemo!’)
18 ‘Wotembereredwa ndi munthu wosocheretsa munthu amene ali ndi vuto losaona.’+ (Anthu onse azidzayankha kuti, ‘Zikhale momwemo!’)
19 ‘Wotembereredwa ndi munthu wopotoza chiweruzo cha mlendo+ amene akukhala pakati panu, mwana wamasiye ndi mkazi wamasiye.’+ (Anthu onse azidzayankha kuti, ‘Zikhale momwemo!’)
20 ‘Wotembereredwa ndi munthu wogona ndi mkazi wa bambo ake, chifukwa wachititsa manyazi bambo akewo.’*+ (Anthu onse azidzayankha kuti, ‘Zikhale momwemo!’)
21 ‘Wotembereredwa ndi munthu wogona ndi nyama iliyonse.’+ (Anthu onse azidzayankha kuti, ‘Zikhale momwemo!’)
22 ‘Wotembereredwa ndi munthu wogona ndi mchemwali wake, mwana wamkazi wa bambo ake kapena mwana wamkazi wa mayi ake.’+ (Anthu onse azidzayankha kuti, ‘Zikhale momwemo!’)
23 ‘Wotembereredwa ndi mwamuna wogona ndi apongozi ake.’+ (Anthu onse azidzayankha kuti, ‘Zikhale momwemo!’)
24 ‘Wotembereredwa ndi munthu wobisalira mnzake nʼkumupha.’+ (Anthu onse azidzayankha kuti, ‘Zikhale momwemo!’)
25 ‘Wotembereredwa ndi munthu wolandira chiphuphu kuti aphe munthu wosalakwa.’+ (Anthu onse azidzayankha kuti, ‘Zikhale momwemo!’)
26 ‘Wotembereredwa ndi munthu amene sadzatsatira mawu a mʼChilamulo ichi ndipo sadzawagwiritsa ntchito.’+ (Anthu onse azidzayankha kuti, ‘Zikhale momwemo!’”)