2 Mbiri
4 Ndiyeno anapanga guwa lansembe lakopa.*+ Guwalo linali lalikulu mikono 20 mulitali, mikono 20 mulifupi ndipo kuchokera pansi kufika pamwamba linali lalitali mikono 10.
2 Kenako iye anapanga thanki yosungira madzi.*+ Thankiyo inali yozungulira ndipo inali mikono 10 kuchokera mbali ina kufika ina, kuyeza modutsa pakati. Thankiyo inali yaitali mikono 5 ndipo kuzungulira thanki yonseyo inali mikono 30.+ 3 Kuzungulira mʼkhosi mwake monse munali zokongoletsera zooneka ngati zipanda.+ Pamalo alionse otalika mkono umodzi ankaikapo zokongoletsera 10. Zokongoletsera zooneka ngati zipandazo zinalipo mizere iwiri ndipo anaziumbira kumodzi ndi thankiyo. 4 Thankiyo anaikhazika pangʼombe zamphongo 12.+ Ngʼombe zitatu zinayangʼana kumpoto, zitatu zinayangʼana kumadzulo, zitatu zinayangʼana kumʼmwera ndipo zitatu zinayangʼana kumʼmawa. Thankiyo inali pamwamba pa ngʼombezo ndipo mbuyo zonse za ngʼombezo zinaloza pakati. 5 Kuchindikala kwa thankiyo kunali chikhatho* chimodzi. Milomo yake inali ngati kukamwa kwa mphika kapena ngati maluwa. Muthankiyo munkalowa madzi okwana mitsuko* 3,000.
6 Iye anapanganso mabeseni 10 ndipo anaika mabeseni 5 kumanja, mabeseni 5 kumanzere.+ Mʼmabeseniwo ankatsukiramo zinthu zimene ankagwiritsa ntchito popereka nsembe yopsereza.+ Koma ansembe ankasamba madzi a muthanki ija.+
7 Kenako anapanga zoikapo nyale 10 zagolide+ mogwirizana ndi zomwe anauzidwa+ nʼkuziika mʼkachisi. Anaika 5 kumanja, 5 kumanzere.+
8 Iye anapanganso matebulo 10 nʼkuwaika mʼkachisi. Anaika 5 kumanja, 5 kumanzere+ ndipo anapanganso mbale zolowa 100 zagolide.
9 Ndiyeno anapanga bwalo+ la ansembe+ ndi bwalo lalikulu* komanso zitseko za bwalo lalikululo.+ Zitsekozo anazikuta ndi kopa. 10 Thanki ija anaiika kumanja, kumʼmwera chakumʼmawa.+
11 Hiramu anapanganso ndowa, mafosholo ndi mbale zolowa.+
Choncho iye anamaliza ntchito imene ankagwirira Mfumu Solomo panyumba ya Mulungu woona.+ 12 Pa ntchitoyi anapanga zipilala ziwiri,+ mitu ya zipilala yooneka ngati mbale zolowa imene anaiika pamwamba pazipilala ziwirizo komanso maukonde awiri+ okutira mitu iwiri imene inali pazipilalazo. 13 Anapanganso makangaza 400+ oika pamaukonde awiri aja ndipo panali mizere iwiri ya makangaza* pa ukonde uliwonse. Makangazawo anali okutira mitu iwiri yooneka ngati mbale zolowa imene inali pazipilala ziwiri zija.+ 14 Anapanganso zotengera 10, mabeseni 10 oika pazotengerazo,+ 15 thanki imodzi, ngʼombe zamphongo 12 zokhala pansi pa thankiyo,+ 16 ndowa, mafosholo, mafoloko+ ndi ziwiya zina zonse. Hiramu-abivu+ anapanga zinthu zimenezi ndi kopa wonyezimira kuti Mfumu Solomo aziike mʼnyumba ya Yehova. 17 Mfumuyo inaumba zinthu zimenezi mʼchikombole chochindikala chadongo mʼchigawo cha Yorodano, pakati pa Sukoti+ ndi Zereda. 18 Solomo anapanga ziwiya zimenezi zambiri. Kopayo sanadziwike kulemera kwake.+
19 Solomo anapanga zinthu zonse+ zapanyumba ya Mulungu woona. Anapanga guwa lansembe lagolide,+ matebulo+ oikapo mkate wachionetsero+ 20 ndi zoikapo nyale ndi nyale zake zagolide woyenga bwino,+ zoti aziziyatsa pafupi ndi mʼchipinda chamkati mogwirizana ndi malamulo ake. 21 Anapanganso maluwa agolide, nyale zagolide ndi zopanira zagolide zozimitsira nyale ndipo golide wake anali woyengedwa bwino kwambiri. 22 Komanso anapanga zozimitsira nyale, mbale zolowa, makapu ndi zopalira moto. Zonsezi zinali zagolide woyenga bwino. Anapanganso khomo lolowera mʼnyumbayo, zitseko zamkati za Chipinda Choyera Koposa+ ndi zitseko za nyumbayo. Zonsezi zinali zagolide.+