Numeri
35 Yehova anapitiriza kulankhula ndi Mose mʼchipululu cha Mowabu ku Yeriko, pafupi ndi mtsinje wa Yorodano+ kuti: 2 “Lamula Aisiraeli kuti pacholowa chawo cha malo, akapereke kwa Alevi mizinda yokhalamo.+ Akaperekenso kwa Aleviwo malo odyetserako ziweto ozungulira mizindayo.+ 3 Aleviwo azikakhala mʼmizindayo, ndipo malo odyetserako ziwetowo akakhala a ziweto zawo, katundu wawo ndi nyama zawo zonse. 4 Malo odyetserako ziweto a mizinda imene mukapereke kwa Aleviwo, akakhale mamita 445* kuchokera pampanda wa mzindawo kuzungulira mzinda wonse. 5 Mukayeze kunja kwa mzinda, mamita 890 kumbali yakumʼmawa, mamita 890 kumbali yakumʼmwera, mamita 890 kumbali yakumadzulo, ndi mamita 890 kumbali yakumpoto, kuzungulira mzinda. Amenewa akakhale malo odyetserako ziweto kwa anthu amʼmizindayo.
6 Mukapereke kwa Alevi mizinda 6 yoti munthu amene wapha mnzake azikathawirako. Kuwonjezera pa mizindayi, mukapereke kwa Aleviwo mizinda ina 42.+ 7 Mizinda yonse imene mukapereke kwa Alevi ikakwane 48. Mizindayi mukawapatse limodzi ndi malo ake odyetserako ziweto.+ 8 Mizinda imene mukawapatseyo ikachokere pa cholowa cha Aisiraeli.+ Pa fuko lalikulu mukatenge mizinda yambiri, ndipo pa fuko lalingʼono mukatenge yochepa.+ Fuko lililonse likapereke ina ya mizinda yake kwa Alevi mogwirizana ndi cholowa chimene akalandire.”
9 Yehova anapitiriza kulankhula ndi Mose kuti: 10 “Lankhula ndi Aisiraeli, uwauze kuti, ‘Muwoloka Yorodano kupita kudziko la Kanani.+ 11 Mukasankhe mizinda yoyenerera kwa inu, kuti ikakhale mizinda yanu yothawirako. Munthu amene wapha mnzake mwangozi azikathawira kumeneko.+ 12 Mizindayo ikakhale malo amene munthu wopha mnzake, amene akuthawa wobwezera magazi+ azikathawirako, kuti amene wapha mnzakeyo asaphedwe mpaka mlandu wake utaweruzidwa pamaso pa oweruza.+ 13 Mizinda yothawirako 6 imene mukaperekeyo, izikagwira ntchito imeneyi. 14 Mupereke mizinda itatu tsidya lino la Yorodano,+ ndiponso mukapereke mizinda itatu tsidya linalo, mʼdziko la Kanani.+ Imeneyi ikakhala mizinda yothawirako. 15 Mizinda 6 imeneyi ikakhale kothawirako Aisiraeli, mlendo+ komanso munthu aliyense amene akukhala pakati pawo, aliyense amene wapha munthu mwangozi.+
16 Koma ngati munthu wamenya mnzake ndi chitsulo nʼkufa, ameneyo ndi wopha munthu. Ndipo wopha munthuyo ayenera kuphedwa ndithu.+ 17 Ngati wagenda mnzake ndi mwala woti ungaphe munthu, mnzakeyo nʼkufa, ameneyo ndi wopha munthu. Ndipo wopha munthuyo aphedwe ndithu. 18 Ngati wamenya mnzake ndi mtengo woti ungaphe munthu, mnzakeyo nʼkufa, ameneyo ndi wopha munthu. Wopha munthuyo aphedwe ndithu.
19 Wobwezera magazi ndi amene ayenera kupha munthu amene wapha mnzakeyo. Akadzangomupeza, wobwezera magaziyo adzamuphe. 20 Ngati munthu wafa wina atamukankha chifukwa chodana naye, kapena ngati wafa wina atamugenda ndi chinachake ndi zolinga zoipa,*+ 21 kapenanso wafa wina atamumenya ndi dzanja lake chifukwa chodana naye, amene wapha mnzakeyo aphedwe ndithu. Iye ndi wopha munthu. Wobwezera magazi aphe wopha munthuyo akangomupeza.
22 Koma ngati wamukankha mwangozi, osati chifukwa choti amadana naye, kapena ngati wamugenda ndi chinachake mwangozi, osati ndi zolinga zoipa,*+ 23 kapena ngati samamuona ndipo wamugwetsera mwala, mnzakeyo nʼkufa, koma sanali mdani wake komanso analibe cholinga choti amuvulaze, 24 oweruza aweruze pakati pa wopha mnzakeyo ndi woyenera kubwezera magaziyo, mogwirizana ndi malamulo amenewa.+ 25 Kenako oweruzawo azipulumutsa wopha munthuyo mʼmanja mwa wobwezera magazi, ndipo amubwezere kumzinda wothawirako kumene anathawira. Iye ayenera kukhala mumzindamo mpaka mkulu wa ansembe amene anadzozedwa ndi mafuta opatulika adzamwalire.+
26 Koma wopha munthuyo akatuluka kunja kwa malire a mzinda wothawirako kumene anathawira, 27 wobwezera magazi nʼkumupeza kunja kwa malire a mzinda wothawirako nʼkumupha, wobwezera magaziyo alibe mlandu wa magazi. 28 Wopha munthuyo ayenera kukhala mumzinda wothawirako mpaka mkulu wa ansembe atamwalira. Pambuyo pa imfa ya mkulu wa ansembe, wopha munthuyo akhoza kubwerera kumalo a cholowa chake.+ 29 Amenewa adzakhale malamulo anu oweruzira milandu mʼmibadwo yanu yonse kulikonse kumene mukakhale.
30 Aliyense amene wapha munthu aziphedwa+ pambuyo poti mboni zatsimikizira.+ Koma munthu sakuyenera kuphedwa ngati pali umboni woperekedwa ndi munthu mmodzi yekha. 31 Musamalandire dipo lowombolera moyo wa munthu amene wapha mnzake, chifukwa ndi woyenera kuphedwa. Aphedwe ndithu ameneyo.+ 32 Komanso musamalandire dipo lowombolera munthu amene anathawira kumzinda wothawirako, nʼcholinga choti aloledwe kubwerera kwawo mkulu wa ansembe asanamwalire.
33 Musamadetse dziko limene mukukhalamo, chifukwa magazi ndi amene amadetsa dziko.+ Ndipo dziko limene ladetsedwa ndi magazi silingayeretsedwe ndi china chilichonse, kupatulapo magazi a munthu amene anakhetsa magaziyo.+ 34 Musamadetse dziko limene mukukhalamo, limene inenso ndikukhalamo, chifukwa ine Yehova ndikukhala pakati pa Aisiraeli.’”+