Mawu a Yehova Ndi Amoyo
Mfundo Zazikulu za M’buku la Numeri
PAMBUYO potuluka mu Igupto, Aisrayeli analinganizidwa kukhala mtundu woima pawokha. Sipakanapita nthaŵi yaitali kuti aloŵe m’Dziko Lolonjezedwa, koma sizinatero. M’malo mwake anafunika kuyendayenda ‘m’chipululu chachikulu ndi choopsa’ zaka makumi anayi. (Deuteronomo 8:15) Chifukwa chiyani? Mbiri yofotokozedwa m’buku la m’Baibulo la Numeri imatiuza zimene zinachitika. Mbiriyi iyenera kutithandiza kuona kuti kumvera Yehova Mulungu ndi kulemekeza anthu omuimira n’kofunika kwambiri.
Buku la Numeri, limene linalembedwa ndi Mose m’chipululu ndiponso m’zidikha za Moabu, limafotokoza zimene zinachitika m’zaka 38 ndi miyezi 9, kuchokera m’chaka cha 1512 Kristu Asanabwere mpaka m’chaka cha 1473 Kristu Asanabwere. (Numeri 1:1; Deuteronomo 1:3) Nkhani za m’bukuli zili m’zigawo zitatu. Chigawo choyamba chimalongosola zinthu zimene zinachitika pa phiri la Sinai. Chachiŵiri chimafotokoza zimene zinachitika pamene Aisrayeli anali kuyendayenda m’chipululu. Ndipo chigawo chomalizira chili ndi zimene zinachitika m’zidikha za Moabu. Pamene mukuŵerenga nkhaniyi, mwina ndi bwino kusinkhasinkha za mafunso aŵa: ‘Kodi zinthu zimenezi zikundiphunzitsa chiyani? Kodi m’buku limeneli muli mfundo zimene zingandithandize masiku ano?’
PA PHIRI LA SINAI
Woyamba wa kalembera muŵiri wotchulidwa m’buku la Numeri anachitika Aisrayeli akadali m’tsinde mwa phiri la Sinai. Amuna onse a zaka zoyambira pa 20 kupita m’tsogolo, kupatulapo Alevi, analipo 603,550. Mwachionekere, kalemberayu anachitika poganizira zausilikali. N’kutheka kuti anthu onse m’chigono kapena kuti mu msasa, kuphatikizapo akazi, ana, ndi Alevi, analipo opitirira mamiliyoni atatu.
Kalemberayu atatha, Aisrayeli analandira malangizo a mmene aziyendera, anapatsidwa tsatanetsatane wa ntchito za Alevi, ntchito ya pachihema, malamulo okhudza kubindikiritsa munthu, ndi okhudza kuchitirana nsanje komanso malamulo a zowinda za Anaziri. Chaputala 7 chili ndi nkhani ya zinthu zomwe akalonga a mafuko anapereka pa kuperekedwa kwa guwa la nsembe, ndipo chaputala 9 chimafotokoza za mwambo wa Paskha. Anthuŵa anapatsidwanso malangizo okhomera ndi kupasulira msasa.
Kuyankha Mafunso a M’Malemba:
2:1, 2—Kodi ‘zizindikiro’ zimene zinkakhala pakati pa mahema a mbendera [“magulu a mafuko atatuatatu,” NW] m’chipululu zinali chiyani? Baibulo silifotokoza kuti zizindikirozi zinali chiyani. Koma sikuti anthu ankaziona ngati zinthu zopatulika kapena kuti zinali zokhudzana ndi chipembedzo. Zizindikirozi zinkathandiza anthu kudziŵa pamene akukhala mu msasa.
5:27—Kodi akutanthauzanji ponena kuti mkazi amene wachita chigololo ‘adzawonda m’chuuno’? Pa lembali, mawu akuti “m’chuuno” akutanthauza ziŵalo zoberekera. (Genesis 46:26) ‘Kuwonda’ kwa ziŵalo zoberekerazi kukutanthauza kunyala kwa ziŵalozi kuti mkaziyo asathe kukhala ndi pakati.
Zimene Tikuphunzirapo:
6:1-7. Anaziri anafunika kusala vinyo ndi zakumwa zonse zoledzeretsa, zimene zinkafuna kudzimana. Ankafunika kusiya tsitsi lawo kuti likule kwambiri, chomwe chinali chizindikiro cha kugonjera Yehova, mofanana ndi mmene akazi ankakhalira ogonjera kwa amuna kapena atate awo. Anaziri ankafunika kuti asakhale odetsedwa chifukwa chokhudza mtembo, ngakhale mtembo wa mbale wawo. Atumiki a nthaŵi zonse masiku ano amasonyeza mtima wodzipereka pankhani ya kudzimana ndi kugonjera Yehova ndiponso zimene iye wakonza. Ntchito zina zingafune kuti iwo apite ku mayiko akutali ndi kwawo, zimene zingapangitse kuti kukhale kovuta ndipo mwinanso kosatheka kumene kupita kwawo kumaliro a mbale wawo.
8:25, 26. Anthu achikulire anali kulamulidwa kupuma pa ntchito yomwe mwalamulo ankafunika kugwira. Ankachita izi pofuna kuonetsetsa kuti pali amuna oyenerera ogwira ntchito za Alevi, ndiponso poganizira msinkhu wa anthu achikulirewo. Komabe ankatha kudzipereka kuti athandize Alevi ena. Ngakhale kuti masiku ano palibe nthaŵi yopuma pa ntchito yolengeza Ufumu, mfundo ya lamuloli ikutipatsa phunziro lofunika kwambiri. Ngati Mkristu sangakwanitse kugwira ntchito zina chifukwa cha ukalamba, iye angathe kugwira ntchito zina zimene angazikwanitse.
KUYENDAYENDA M’CHIPULULU
Mtambo wokhala pamwamba pa chihema utakwera, Aisrayeli anayamba ulendo umene anakaloŵa nawo m’zidikha za Moabu patatha zaka 38 ndi mwezi umodzi kapena iŵiri. Mungapindule kwambiri kutsatira njira yawo pa mapu amene ali patsamba 9 la kabuku kakuti ‘Onani Dziko Lokoma,’ kofalitsidwa ndi Mboni za Yehova.
Paulendo wopita ku Kadesi, m’chipululu cha Parana, panabuka madandaulo atatu. Dandaulo loyamba linatha Yehova atatumiza moto kuti unyeketse ena mwa anthuwo. Kenako Aisrayeli anadandaula kuti akufuna nyama, ndipo Yehova anawapatsa zinziri. Kudandaula za Mose komwe Miriamu ndi Aroni anachita kunachititsa kuti Miriamu agwidwe khate kwa kanthaŵi.
Atamanga mahema awo pa Kadesi, Mose anatuma anthu 12 kuti akazonde Dziko Lolonjezedwa. Anthuŵa anabwerako patatha masiku 40. Pokhulupirira lipoti loipa lokhudza dzikolo limene anthu khumi mwa anthu okazonda dzikowo anafotokoza, anthu anafuna kuponya miyala Mose ndi Aroni, pamodzi ndi Yoswa ndi Kalebi, azondi okhulupirikawo. Yehova anaganiza zokantha anthuwo ndi milili, koma Mose anachonderera kuti asatero, ndipo Mulungu anafotokoza kuti anthuwo akhala akuyendayenda m’chipululu zaka 40, mpaka anthu onse amene anaŵerengedwa pa kalembera uja atatha kufa.
Yehova anaperekanso malangizo ena. Kora ndi anthu ena anapandukira Mose ndi Aroni, koma opandukawo ena anawonongedwa ndi moto pamene ena anamezedwa ndi nthaka. Tsiku lotsatira anthu onse anali kung’ung’udza motsutsana ndi Mose ndi Aroni. Chifukwa cha zimenezi, anthu 14,700 anafa ndi mliri wochoka kwa Yehova. Pofuna kudziŵitsa anthu kuti ndi ndani amene wam’sankha kukhala mkulu wa ansembe, Mulungu anachititsa ndodo ya Aroni kuphuka. Kenako Yehova anapereka malamulo enanso a ntchito za Alevi ndiponso malamulo okhudza kuyeretsa anthu. Kugwiritsira ntchito phulusa la ng’ombe yamsoti yofiira kunkaimira kuyeretsedwa kwa anthu mwa nsembe ya Yesu.—Ahebri 9:13, 14.
Ana a Israyeli anapitanso ku Kadesi, komwe Miriamu anamwalirira. Anthu anadandaulanso ndi Mose ndi Aroni. Kodi chifukwa chake chinali chiyani? Kusoŵa kwa madzi. Chifukwa chakuti Mose ndi Aroni analephera kuyeretsa dzina la Yehova pamene anali kupatsa anthuwo madzi mozizwitsa, iwo anataya mwayi wokaloŵa m’Dziko Lolonjezedwa. Aisrayeli anachoka pa Kadesi, ndipo Aroni anamwalirira pa phiri la Hori. Pamene anali kuyenda mozungulira Edomu, Aisrayeli analema ndipo analankhulira Mulungu ndi Mose zinthu zoipa. Motero Yehova anatumiza njoka zaululu kuti ziwalange. Apanso, Mose anachonderera Mulungu, ndipo Mulungu anamuuza kuti apange njoka yamkuwa ndi kuiika pamtengo kuti anthu amene alumidwa azichira akaiyang’ana. Njokayo inali kuimira kupachikidwa kwa Yesu Kristu kuti anthufe tipindule mpaka muyaya. (Yohane 3:14, 15) Israyeli anagonjetsa mafumu a Aamori, omwe ndi Sihoni ndi Ogi, ndi kuwalanda mayiko awo.
Kuyankha Mafunso a M’Malemba:
12:1—Kodi n’chifukwa chiyani Miriamu ndi Aroni anadandaula za Mose? Zikuoneka kuti chifukwa chenicheni chimene iwo anadandaulira chinali chakuti Miriamu ankafuna kukhala ndi mphamvu zambiri. N’kutheka kuti, mkazi wa Mose, Zipora, atabwera kuchipululu kudzakhala ndi Mose, Miriamu anayamba kuopa kuti sazionedwanso monga mayi wolemekezeka kwambiri.—Eksodo 18:1-5.
12:9-11—N’chifukwa chiyani Miriamu yekha ndiye anagwidwa khate? Mwachionekere, ndi iye amene anayambitsa kudandaula n’kuumiriza Aroni kuti athandizane naye. Aroni anasonyeza mtima wabwino poulula kulakwa kwake.
21:14, 15—Kodi buku limene alitchula apa n’chiyani? Malemba amatchula mabuku osiyanasiyana amene anthu olemba Baibulo anawagwiritsira ntchito monga gwero la zimene analemba. (Yoswa 10:12, 13; 1 Mafumu 11:41; 14:19, 29) Limodzi mwa mabuku ameneŵa linali “buku la Nkhondo za Yehova.” Bukuli linkafotokoza nkhondo zimene anthu a Yehova anamenya.
Zimene Tikuphunzirapo:
11:27-29. Mose anapereka chitsanzo chabwino kwambiri cha zimene tiyenera kuchita ena akalandira ntchito yapadera mu utumiki wa Yehova. Mose anasangalala pamene Elidadi ndi Medadi anayamba kunenera m’malo mowachitira nsanje pofuna kuti iye yekha azipatsidwa ulemu.
12:2, 9, 10; 16:1-3, 12-14, 31-35, 41, 46-50. Yehova amayembekezera kuti anthu amene amamulambira azilemekeza udindo woperekedwa ndi Mulungu.
14:24. Chinthu chofunika kwambiri chotithandiza kukana kuchita zinthu zoipa zimene dziko likutikakamiza kuchita ndicho kukhala ndi “mzimu wina,” kapena kuti maganizo ena. Tiyenera kukhala ndi maganizo osiyana ndi a anthu a m’dzikoli.
15:37-41. Cholinga cha mphonje zapadera zimene zinkakhala pa zovala za Aisrayeli chinali kuwakumbutsa kuti iwo ndi anthu opatulidwa kuti alambire Mulungu ndi kumvera malamulo ake. Kodi nafenso sitiyenera kutsatira miyezo ya Mulungu pamoyo wathu ndi kuoneka kuti ndife anthu osiyana ndi dzikoli?
M’ZIDIKHA ZA MOABU
Amoabu anachita nawo mantha kwambiri ana a Israyeli atamanga mahema awo m’zidikha za Moabu. Motero, Mfumu Balaki ya Moabu, inaitanitsa Balamu kuti akatemberere Aisrayeliwo. Koma Yehova anakakamiza Balamu kuti awadalitse. Motero, anatenga akazi achimoabu ndiponso achimidyani kuti akope amuna achiisrayeli ndi kuchita nawo zachisembwere ndi kulambira mafano. Chotsatirapo chake chinali chakuti Yehova anapha anthu 24,000 amene anachita zolakwa zimenezi. Mliriwu unasiya Pinehasi atasonyeza kuti sangalekerere mchitidwe woukira Yehova.
Kalembera wachiŵiri anasonyeza kuti, kupatulapo Yoswa ndi Kalebe, panalibenso wina aliyense mwa anthu amene anaŵerengedwa nawo pa kalembera woyamba uja amene panthaŵiyi anali moyo. Yoswa anaikidwa kukhala woloŵa m’malo mwa Mose. Aisrayeli analandira malangizo operekera zopereka zosiyanasiyana ndiponso a nkhani yopanga chowinda. Aisrayeli anabwezera chilango kwa Amidyani. Mafuko a Rubeni, Gadi, ndi fuko logaŵika pakati la Manase anakhazikika kum’maŵa kwa mtsinje wa Yordano. Aisrayeli anapatsidwa malangizo a mmene awolokere Yordano ndi kulanda dziko. Ndipo malire a dzikolo anafotokozedwa mwatsatanetsatane. Choloŵa anafunika kuchigaŵa pochita maere. Alevi anapatsidwa midzi 48, ndipo 6 mwa midziyo inali midzi yopulumukirako.
Kuyankha Mafunso a M’Malemba:
22:20-22—Kodi n’chifukwa chiyani Yehova anakwiyira Balamu? Yehova anali atauza mneneri Balamu kuti asatemberere Aisrayeli. (Numeri 22:12) Komabe, mneneriyu anatengana ndi amuna a Balaki ali ndi malingaliro okatemberera Israyeli. Balamu ankafuna kusangalatsa mfumu ya Amoabu ndi kulipiridwa ndi mfumuyi. (2 Petro 2:15, 16; Yuda 11) Ngakhale pamene Balamu anakakamizidwa kudalitsa Aisrayeli m’malo mowatemberera, iye anafunabe kusangalatsa mfumuyo mwa kupereka maganizo oti akazi olambira Baala akope amuna achiisrayeli. (Numeri 31:15, 16) Motero Mulungu anakwiya ndi Balamu chifukwa cha dyera lake limene linamuchititsa zachinyengo.
30:6-8—Kodi mwamuna wachikristu angafafanize zowinda za mkazi wake? Nkhani ya zowinda masiku ano imakhala pakati pa Yehova ndi wolambira aliyense payekha. Mwachitsanzo, kudzipatulira kwa Yehova ndi chowinda chimene munthu amapanga payekha. (Agalatiya 6:5) Mwamuna alibe mphamvu yofafaniza chowinda choterocho. Komabe, mkazi ayenera kuonetsetsa kuti asawinde kuchita zinthu zotsutsana ndi Mawu a Mulungu kapena ntchito zake kwa mwamuna wake.
Zimene Tikuphunzirapo:
25:11. Pinehasi anatisonyezatu chitsanzo chabwino kwambiri chokhala munthu wachangu pa kulambira Yehova! Kodi chikhumbo chakuti mpingo ukhale woyera sichiyenera kutilimbikitsa kuuza akulu achikristu tchimo lililonse la chisembwere limene ifeyo tikulidziŵa?
35:9-29. Mfundo yakuti wopha munthu mwangozi azisiya nyumba yake n’kuthaŵira ku mudzi wopulumukirako ndi kukhalako kanthaŵi ikutiphunzitsa kuti moyo ndi wopatulika ndipo tikufunika kuulemekeza.
35:33. Dziko loipitsidwa ndi mwazi wa anthu osalakwa lingatetezeredwe kokha ndi mwazi wa anthu omwe anakhetsa mwazi wa osalakwawo. Ndiyetu m’poyenera kuti Yehova adzayambe wawononga oipa asanasinthe dziko kukhala paradaiso!—Miyambo 2:21, 22; Danieli 2:44.
Mawu a Mulungu Ali ndi Mphamvu
Tiyenera kulemekeza Yehova ndiponso anthu amene apatsidwa maudindo pakati pa anthu ake. Buku la Numeri limaimveketsa bwino mfundo imeneyi. Ilitu ndi phunziro lalikulu lothandiza kuti mumpingo masiku ano mukhale mtendere ndi umodzi!
Zochitika zimene zafotokozedwa m’buku la Numeri zimasonyeza mmene zilili zosavuta kuti anthu amene amanyalanyaza zinthu zauzimu achite choipa, monga kung’ung’udza, chisembwere, ndi kulambira mafano. Zitsanzo ndiponso mfundo zina zimene tikuphunzira m’buku la m’Baibulo limeneli zingagwiritsidwe ntchito pa nkhani ya zosoŵa za pampingo pa Msonkhano wa Utumiki m’mipingo ya Mboni za Yehova. Zoonadi, “mawu a Mulungu ali amoyo, ndi ochitachita” m’moyo mwathu.—Ahebri 4:12.
[Chithunzi pamasamba 24, 25]
Pogwiritsa ntchito mtambo wozizwitsa womwe unkakhala pamwamba pa chihema, Yehova anali kulamulira Aisrayeli kuti amange msasa ndiponso kuti aupasule
[Zithunzi patsamba 26]
Yehova ndi woyenera kumumvera ndiponso iye amatiyembekezera kulemekeza anthu omuimira