Oweruza
17 Panali mwamuna wina wakudera lamapiri la Efuraimu,+ dzina lake Mika. 2 Iye anauza mayi ake kuti: “Ndalama zanu zasiliva zokwana 1,100 zimene zinasowa zija, ndipo munatemberera munthu amene anazibayo ine ndikumva, zili ndi ine. Ndine amene ndinatenga.” Atatero mayi akewo anati: “Yehova akudalitse mwana wanga.” 3 Choncho anabweza ndalama zasiliva zokwana 1,100 zija kwa mayi ake. Koma mayi akewo anati: “Ndalamazi ndizipereka kwa Yehova kuti zikhale zopatulika. Ndikufuna kuti iweyo ugwiritse ntchito ndalamazi kukapangitsa chifaniziro chosema ndiponso chifaniziro chachitsulo.+ Choncho ndikukupatsa ndalamazi.”
4 Mika atabweza ndalamazo kwa mayi ake, mayi akewo anatenga ndalama zasiliva 200 nʼkuzipereka kwa wosula siliva. Wosula silivayo anapanga zifaniziro ziwiri. Zifanizirozi anaziika mʼnyumba ya Mika. 5 Mika anali ndi nyumba ya milungu ndipo anapanga efodi+ ndi aterafi,*+ komanso anapatsa mmodzi mwa ana ake udindo woti akhale wansembe wake.+ 6 Pa nthawiyo mu Isiraeli munalibe mfumu.+ Aliyense ankangochita zimene akuona kuti nʼzoyenera.+
7 Ndiyeno ku Betelehemu+ wa ku Yuda kunali mnyamata wina, wamʼbanja la Yuda. Iye anali Mlevi+ ndipo anakhala kumeneko kwakanthawi. 8 Mnyamata ameneyu anachoka mumzinda wa Betelehemu wa ku Yuda, kuti akapeze malo okhala. Ali pa ulendowu, anafika mʼdera lamapiri la Efuraimu, kunyumba ya Mika.+ 9 Ndiyeno Mika anamʼfunsa kuti: “Wachokera kuti?” Iye anayankha kuti: “Ndine Mlevi, ndachokera ku Betelehemu wa ku Yuda ndipo ndikufufuza malo okhala.” 10 Atatero Mika anamuuza kuti: “Bwanji uzikhala ndi ine ndipo ukhale mlangizi* komanso wansembe wanga? Ndizikupatsa ndalama zasiliva 10 pa chaka, zovala komanso chakudya.” Atatero Mleviyo analowa mʼnyumba. 11 Choncho Mleviyo anavomera kukhala ndi Mika ndipo ankakhala ngati mmodzi wa ana ake. 12 Kuwonjezera pamenepo, Mika anapatsa Mleviyo udindo woti akhale wansembe wake+ ndipo ankakhala mʼnyumba ya Mikayo. 13 Kenako Mika anati: “Tsopano ndadziwa kuti Yehova azindichitira zabwino, chifukwa wansembe wanga ndi Mlevi.”