Mawu a Yehova Ndi Amoyo
Mfundo Zazikulu za M’buku la Oweruza
KODI Yehova amatani anthu ake akam’nyalanyaza n’kuyamba kulambira milungu yonyenga? Nanga amatani ngati anthuwo mobwerezabwereza akukana kumumvera, ndipo akungofuna thandizo lake pamene ali m’mavuto? Kodi zikatero, Yehova amawapulumutsabe? Buku la Oweruza limayankha mafunso amenewa ndi enanso ofunika kwambiri. Bukuli, lomwe linamalizidwa kulembedwa ndi mneneri Samueli cha m’ma 1100 B.C.E., munalembedwa zinthu zomwe zinachitika m’zaka 330 kuchokera pamene Yoswa anamwalira mpaka pa kulongedwa kwa mfumu yoyamba ya Israyeli.
Buku la Oweruza ndi lofunika kwambiri kwa ife popeza kuti ndi mbali ya mawu kapena kuti uthenga wamphamvu wa Mulungu. (Ahebri 4:12) Nkhani zochititsa chidwi za m’bukuli zimatithandiza kuzindikira makhalidwe a Mulungu. Zimene timaphunzira m’nkhani zimenezi zimalimbitsa chikhulupiriro chathu ndi kutithandiza kugwira zolimba “moyo weniweniwo,” umene uli moyo wosatha m’dziko latsopano limene Mulungu walonjeza. (1 Timoteo 6:12, 19; 2 Petro 3:13) Zimene Yehova anachita populumutsa anthu ake zimatipatsa chithunzithunzi cha chipulumutso chachikulu cha m’tsogolo kudzera mwa Mwana wake, Yesu Kristu.
N’CHIFUKWA CHIYANI PANAFUNIKA OWERUZA?
Mafumu a dziko la Kanani atagonjetsedwa motsogoleredwa ndi Yoswa, fuko lililonse la Israyeli linapita komwe kunali cholowa chake ndi kutenga dzikolo. Komabe, Aisrayeliwo analephera kulanda dzikolo kwa eninthakawo. Umenewu unakhala msampha woopsa kwa Israyeli.
Mbadwo umene unakhalapo Yoswa atamwalira, ‘sunam’dziwe Yehova kapena ntchito adaichitira Israyeli.’ (Oweruza 2:10) Komanso anthuwo anayamba kukwatirana ndi Akanani ndiponso kutumikira milungu yawo. Chotero Yehova anapereka Aisrayeli m’manja mwa adani awo. Koma adaniwo atafika powakhaulitsa, ana a Israyeli anafuulira Mulungu woona kuti awathandize. Nkhani ya mndandanda wa oweruza amene Yehova anakhazikitsa kuti apulumutse anthu ake kwa adani awo ikuyamba pamene zinthu zachipembedzo, zachikhalidwe cha anthu, ndiponso zandale zili motere.
Kuyankha Mafunso a M’Malemba:
1:2, 4—N’chifukwa chiyani fuko la Yuda linasankhidwa kukhala loyamba kulandira dziko lomwe analigawira? Kukanakhala kuti zonse zinali bwino, mwayiwu ukanapita kwa fuko la Rubeni, mwana woyamba wa Yakobo. Koma paulosi umene ananena ali pafupi kumwalira, Yakobo ananena kuti zinthu sizidzamuyendera bwino Rubeni, chifukwa chakuti anataya mwayi wake wokhala mwana woyamba kubadwa. Simeoni ndi Levi, amene anachita zinthu mwankhanza, anauzidwa kuti adzamwazika mu Israyeli. (Genesis 49:3-5, 7) Choncho, mwana wotsatira amene akanalandira mwayi umenewu anali Yuda, mwana wachinayi wa Yakobo. Simeoni, amene analowera kumtunda limodzi ndi Yuda, analandira madera aang’onoang’ono amene anali m’malo osiyanasiyana m’kati mwa gawo lalikulu limene Yuda analandira.a—Yoswa 19:9.
1:6, 7—N’chifukwa chiyani mafumu ogonjetsedwa ankawadula zala zazikulu za m’manja ndi za m’mapazi? Munthu woduka zala zazikulu za m’manja ndi za m’mapazi sankathanso kumenya nkhondo. Ngati msilikali alibe zala zazikulu za m’manja angagwire bwanji lupanga kapena mkondo? Ndipo ngati msilikali alibe zala zazikulu za m’mapazi, sangathe kuimirirabe bwinobwino mochirimika.
Zimene Tikuphunzirapo:
2:10-12. Tiyenera kukhala ndi chizolowezi chophunzira Baibulo nthawi zonse kuti ‘tisaiwale zochita za Yehova.’ (Salmo 103:2) Makolo ayenera kukhomereza choonadi cha Mawu a Mulungu m’mitima ya ana awo.—Deuteronomo 6:6-9.
2:14, 21, 22. Yehova amakhala ndi cholinga polola zinthu zoipa kuchitikira anthu ake osamvera. Amafuna kuti anthuwo alangike, ayengeke, ndi kuthandizidwa kubwerera kwa iye.
YEHOVA AUTSA OWERUZA
Nkhani yochititsa chidwi ya zochita za oweruza ikuyamba ndi ntchito imene Otiniyeli anachita yothetsa ukapolo wa Israyeli wa zaka zisanu ndi zitatu mu ulamuliro wa mfumu ya Mesopotamiya. Pogwiritsa ntchito njira yofunika kulimba mtima kwambiri, Woweruza Ehudi akupha Egiloni, mfumu yonenepa ya Moabu. Samagara yemwe ndi wolimba mtima, akukantha yekhayekha Afilisti 600, pogwiritsa ntchito mtengo wokusira ng’ombe. Baraki ndi asilikali ake opanda zida zokwanira okwana 10,000 akugonjetsa gulu lankhondo lamphamvu kwambiri la Sisera. Iye akuchita izi atalimbikitsidwa ndi Debora, amene ndi mneneri wamkazi, komanso mothandizidwa ndi Yehova. Yehova akupatsa mphamvu Gideoni ndipo akum’thandiza limodzi ndi asilikali ake 300 kugonjetsa Amidyani.
Kudzera mwa Yefita, Yehova akupulumutsa Israyeli kwa a Amoni. Ena mwa amuna 12 amene akuweruza Israyeli, ndi Tola, Yairi, Ibzani, Eloni, ndi Abidoni. Woweruza womalizira pa onse ndi Samsoni, amene akumenyana ndi Afilisti.
Kuyankha Mafunso a M’Malemba:
4:8—N’chifukwa chiyani Baraki anaumirira kuti mneneri Debora apite naye limodzi kunkhondo? Zikuoneka kuti Baraki anaona kuti sangakwanitse kupita yekha kukamenyana ndi gulu lankhondo la Sisera. Mwa kupitira limodzi ndi mneneriyo, iye limodzi ndi asilikali ake akanakhala otsimikiza kuti Mulungu akuwatsogolera, ndi kuwalimbikitsa. Choncho, Baraki sanasonyeze mantha poumirira kuti Debora apite naye limodzi, koma chinali chizindikiro chakuti anali ndi chikhulupiriro champhamvu.
5:20—Kodi nyenyezi zinamenya nkhondo motani kuchokera kumwamba pothandiza Baraki? Baibulo silinena ngati zimenezi zikutanthauza thandizo la angelo, kugwa kwa miyala yochokera kumwamba imene anzeru a Sisera anati inali kulosera tsoka, kapena ngati zikutanthauza ulosi wabodza umene okhulupirira nyenyezi anauza Sisera. Koma n’zosakaikitsa kuti Mulungu anachitapo kanthu.
7:1-3; 8:10—N’chifukwa chiyani Yehova ananena kuti asilikali 32,000 a Gideoni amene anali kukamenyana ndi asilikali 135,000 anali ochuluka kwambiri? Yehova ananena izi chifukwa chakuti iye anali kuthandiza Gideoni ndi asilikali akewo kupambana pankhondoyo. Mulungu sanafune kuti iwo aganize kuti agonjetsa Amidyani chifukwa cha mphamvu zawo.
11:30, 31—Kodi Yefita ankaganiza zopereka nsembe ya munthu pamene ankanena chowinda chake? Yefita sakanakhala n’komwe ndi maganizo amenewo, chifukwa Chilamulo chinati: “Asapezeke mwa inu munthu wakupitiriza mwana wake wamwamuna kapena mwana wake wamkazi ku moto.” (Deuteronomo 18:10) Komabe n’zoona kuti Yefita ankaganiza za munthu osati nyama. Zikuoneka kuti Aisrayeli sankasunga m’nyumba zawo nyama zoyenerera kuperekedwa nsembe. Ndipo nsembe ya nyama sikanachititsa chowindacho kukhala chapadera. Yefita ankadziwa kuti wotuluka m’nyumba mwakemo kudzakumana naye n’kutheka kuti adzakhala mwana wake wamkazi. Womuchingamirayo anayenera kuperekedwa “nsembe yopsereza” m’njira yakuti munthuyo adzatumikira Yehova pa kachisi moyo wake wonse.
Zimene Tikuphunzirapo:
3:10. Zochita zathu zauzimu zingayende bwino, ngati tikudalira mzimu wa Yehova, osati nzeru za anthu.—Salmo 127:1.
3:21. Ehudi anagwiritsa ntchito lupanga lake mwaluso komanso molimba mtima. Tiyenera kuphunzira kukhala aluso pogwiritsa ntchito “lupanga la mzimu, [lomwe ndi] Mawu a Mulungu.” Izi zikutanthauza kuti mu utumiki wathu tiyenera kugwiritsa ntchito Malemba molimba mtima.—Aefeso 6:17; 2 Timoteo 2:15.
6:11-15; 8:1-3, 22, 23. Kudzichepetsa kwa Gideoni kukutiphunzitsa zinthu zitatu zofunika: (1) Tikapatsidwa mwayi wa utumiki, tiyenera kuganizira mmene tingakwaniritsire utumikiwo m’malo mongoganizira za kutchuka kapena ulemu womwe tingapeze chifukwa cha utumikiwo. (2) Tikamachita zinthu ndi anthu okonda mikangano, n’chinthu chanzeru kwambiri kukhala odzichepetsa. (3) Kudzichepetsa kumatithandiza kupewa kukhala ndi mtima womangofuna malo apamwamba.
6:17-22, 36-40. Nafenso tiyenera kukhala osamala ndipo ‘tisamakhulupirire mawu alionse ouziridwa.’ M’malo mwake, tiyenera ‘kuyesa mawu ouziridwawo kuona ngati achokera kwa Mulungu.’ (1 Yohane 4:1, NW) Pofuna kutsimikizira kuti uphungu umene akufuna kupereka ukuchokera m’Mawu a Mulungu basi, mkulu wachikristu watsopano angachite bwino kufunsa munthu wina amene wakhala mkulu kwa nthawi yaitali.
6:25-27. Gideoni anali wosamala kuti asakwiyitse chisawawa anthu amene anali kutsutsana nawo. Polalikira uthenga wabwino, tiyenera kusamala kuti tisakhumudwitse ena mosayenerera chifukwa cha mmene tikulankhulira.
7:6. Pankhani yotumikira Yehova, tiyenera kukhala atcheru ndi ogalamuka, ngati amuna 300 a Gideoni.
9:8-15. N’kupusatu kwambiri kuchita zinthu modzikuza n’kukhala ndi mtima wofuna maudindo apamwamba kapena kukhala ndi mphamvu zolamulira!
11:35-37. Chitsanzo chabwino cha Yefita mosakayikira chinathandiza kwambiri mwana wake wamkazi kukhala ndi chikhulupiriro cholimba ndiponso kukhala ndi mtima wodzimana. Masiku ano makolo angawasonyeze ana awo chitsanzo choterocho.
11:40. Munthu amene akusonyeza mtima wofunitsitsa kutumikira Yehova amalimbikitsidwa tikamuyamikira.
13:8. Pophunzitsa ana awo, makolo ayenera kupemphera kwa Yehova kuti awatsogolere ndipo ayenera kumvera malangizo ake.—2 Timoteo 3:16.
14:16, 17; 16:16. Kukonda kulira ndiponso kudandaula pofuna kuti munthu akuchitireni zinazake kungathe kuwononga ubwenzi wanu ndi munthuyo.—Miyambo 19:13; 21:19.
MILANDU INA YA MU ISRAYELI
M’chigawo chomaliza cha buku la Oweruza muli nkhani ziwiri zikuluzikulu. Yoyamba ndi ya munthu wina dzina lake Mika, amene anaimika fano m’nyumba mwake ndi kulemba ntchito Mlevi kuti akhale ngati wansembe wake. Fuko la Dani litawononga mzinda wa Laisi, kapena kuti Lesemu, linamanga mzinda wawowawo ndi kuupatsa dzina lakuti Dani. Pogwiritsa ntchito fano la Mika ndi wansembe wake uja, iwo anayambitsa kulambira kwa mtundu wina mu Dani. Zikuoneka kuti mzinda wa Laisi anaulanda Yoswa asanamwalire.—Yoswa 19:47.
Nkhani yaikulu yachiwiri inachitika pasanapite nthawi yaitali kuchokera pamene Yoswa anamwalira. Amuna ambirimbiri a mumzinda wa Gibeya wa fuko la Benjamini anagwiririra mkazi. Tchimo limeneli linangotsala pang’ono kufafanizitsa mtundu wonse wa Benjamini moti amuna 600 okha ndi amene anapulumuka. Koma panakonzedwa njira ina yowathandiza kupeza akazi oti awakwatire, ndipo chiwerengero chawo chinawonjezeka. Podzafika nthawi imene Davide anali kulamulira, fuko lawo linali ndi anthu opita kunkhondo pafupifupi 60,000.—1 Mbiri 7:6-11.
Kuyankha Mafunso a M’Malemba:
17:6; 21:25—Ngati ‘aliyense ankachita chom’komera pamaso pake,’ kodi zimenezi zinalimbikitsa chisokonezo? Ayi, chifukwa Yehova anaika dongosolo loyenera lotsogolera anthu ake. Anawapatsa Chilamulo ndi ansembe kuti awaphunzitse kuyenda m’njira yake. Pogwiritsa ntchito Urimu ndi Tumimu, mkulu wa ansembe ankatha kufunsira nzeru kwa Mulungu pa nkhani zofunika. (Eksodo 28:30) Komanso mzinda uliwonse unali ndi akulu amene ankatha kupereka malangizo abwino kwambiri. Mwisrayeli akagwiritsa ntchito zinthu zimenezi, ankakhala ndi chikumbumtima chomuthandiza kuchita zinthu zabwino. Akamachita “chom’komera pamaso pake” m’njira imeneyi, zotsatira zake zinali zabwino. Koma munthu akanyalanyaza Chilamulo n’kungochita zomukomera iyeyo pankhani ya makhalidwe ndi kulambira, mapeto ake ankagwa nazo m’mavuto.
20:17-48—N’chifukwa chiyani Yehova analola kuti fuko la Benjamini ligonjetse mitundu inayo kawiri, ngakhale kuti fuko limeneli linafunika kulangidwa? Polola kuti mafuko okhulupirikawo agonje kwambiri poyambirira, Yehova ankafuna kuwayesa mafukowo kuti aone ngati analidi otsimikiza mtima kuchotseratu kuipa konse mu Israyeli.
Zimene Tikuphunzirapo:
19:14, 15. Posafuna kuchereza alendo zinaoneka kuti anthu a ku Gibeya sanali anthu a khalidwe labwino. Akristu akulimbikitsidwa ‘kuchereza alendo.’—Aroma 12:13.
M’tsogolomu Muli Chipulumutso
Posachedwapa, Ufumu wa Mulungu womwe uli m’manja mwa Kristu Yesu udzawononga dziko loipali ndi kupulumutsa anthu oongoka mtima ndi angwiro. (Miyambo 2:21, 22; Danieli 2:44) Nthawiyo, ‘adani ake onse, a Yehova, adzatayika momwemo. Koma iwo omukonda adzakhala ngati dzuwa lotuluka mu mphamvu yake.’ (Oweruza 5:31) Tiyeni tisonyeze kuti tili m’gulu la anthu okonda Yehova potsatira zimene taphunzira m’buku la Oweruza.
Mfundo yaikulu yomwe taona mobwerezabwereza m’nkhani za Oweruza n’njakuti: Kumvera Yehova kumadzetsa madalitso osaneneka, koma kusamumvera kumalowetsa munthu m’mavuto oopsa. (Deuteronomo 11:26-28) Ndiyetu m’pofunika kuti tikhale ‘omvera ndi mtima’ wonse zofuna za Mulungu zimene iye watidziwitsa.—Aroma 6:17; 1 Yohane 2:17.
[Mawu a M’munsi]
a Alevi sanalandire cholowa chilichonse m’Dziko Lolonjezedwa. Anangolandira midzi 48 imene inali m’malo osiyanasiyana m’dziko lonse la Israyeli.
[Mapu patsamba 25]
(Onani m’magazini yeniyeni kuti mumvetse izi)
“Yehova anautsa oweruza, amene anawapulumutsa m’dzanja la iwo akuwafunkha.”—Oweruza 2:16
OWERUZA
1. Otiniyeli (Fuko la Manase)
2. Ehudi (Fuko la Yuda)
3. Samagara (Fuko la Yuda)
4. Baraki (Fuko la Nafitali)
5. Gideoni (Fuko la Isakara)
6. Tola (Fuko la Manase)
7. Yairi (Fuko la Manase)
8. Yefita (Fuko la Gadi)
9. Ibzani (Fuko la Aseri)
10. Eloni (Fuko la Zebuloni)
11. Abidoni (Fuko la Efraimu)
12. Samsoni (Fuko la Yuda)
DANI
MANASE
NAFITALI
ASERI
ZEBULONI
ISAKARA
MANASE
GADI
EFRAIMU
DANI
BENJAMINI
RUBENI
YUDA
[Chithunzi patsamba 26]
Kodi mwaphunzira zotani pa mfundo yoti Baraki anaumirira kuti Debora apite nawo kunkhondo?