Ekisodo
39 Ndiyeno anapanga zovala zolukidwa bwino zoti azivala potumikira mʼmalo oyera. Zovalazo anazipanga pogwiritsa ntchito ulusi wabuluu, ubweya wa nkhosa wapepo ndi ulusi wofiira kwambiri.+ Anapanga zovala zopatulika za Aroni+ mogwirizana ndi zimene Yehova analamula Mose.
2 Anapanga efodi+ wopeta ndi golide, ulusi wabuluu, ubweya wa nkhosa wapepo, ulusi wofiira kwambiri ndi ulusi wopota wabwino kwambiri. 3 Anasula golide kukhala wopyapyala kwambiri, ndipo anamulezaleza kukhala ngati tizingwe kuti apetere limodzi ndi ulusi wabuluu, ubweya wa nkhosa wapepo, ulusi wofiira kwambiri ndi ulusi wabwino kwambiri. 4 Anapanganso nsalu ziwiri zamʼmapewa nʼkuzilumikiza ku efodiyo. Anazilumikiza kutsogolo ndi kumbuyo kwake. 5 Lamba* woluka womangira efodi amene anamulumikiza ku efodiyo+ anali wopangidwa ndi nsalu ya efodi yomweyo. Anali wagolide, ulusi wabuluu, ubweya wa nkhosa wapepo, ulusi wofiira kwambiri ndi ulusi wopota wabwino kwambiri, mogwirizana ndi zimene Yehova analamula Mose.
6 Ndiyeno anaika miyala ya onekisi mʼzoikamo zagolide. Pamiyalayo analembapo mayina a ana a Isiraeli mochita kugoba ngati mmene amagobera chidindo.+ 7 Ndipo miyalayo anailowetsa pansalu zamʼmapewa za efodi kuti ikhale miyala yachikumbutso kwa ana a Isiraeli,+ mogwirizana ndi zimene Yehova analamula Mose. 8 Kenako anapanga chovala pachifuwa+ ndipo anachipanga mwaluso mofanana ndi efodi. Anachipanga ndi golide, ulusi wabuluu, ubweya wa nkhosa wapepo, ulusi wofiira kwambiri ndi ulusi wopota wabwino kwambiri.+ 9 Akachipinda pakati chinali chofanana mbali zonse 4. Chovala pachifuwacho anachipanga kuti akachipinda pakati, mulitali mwake chizikhala masentimita 22* ndiponso mulifupi mwake masentimita 22. 10 Ndiyeno pachovala pachifuwacho anaikapo mizere 4 ya miyala. Mzere woyamba unali ndi miyala ya rube, topazi ndi emarodi. 11 Mzere wachiwiri unali ndi miyala ya nofeki, safiro ndi yasipi. 12 Mzere wachitatu unali ndi miyala ya lesemu,* agate ndi ametusito. 13 Ndipo mzere wa 4 unali ndi miyala ya kulusolito, onekisi ndi yade. Anaiika mʼzoikamo zake zagolide. 14 Miyalayo anaiika mogwirizana ndi mayina a ana 12 a Isiraeli. Mwala uliwonse analembapo mochita kugoba ngati mmene amagobera chidindo ndipo mwala uliwonse unali ndi dzina limodzi mwa mayina a mafuko 12.
15 Ndipo pachovala pachifuwa anapangapo matcheni agolide woyenga bwino, okhala ngati zingwe zopota.+ 16 Anapanganso zoikamo miyala ziwiri zagolide ndi mphete ziwiri zagolide, ndipo anaika mphete ziwirizo mʼmakona awiri a chovala pachifuwacho. 17 Kenako analowetsa zingwe ziwiri zagolide zija mumphete ziwiri zamʼmakona a chovala pachifuwa. 18 Ndipo analowetsa zingwe ziwirizo pa zoikamo miyala ziwiri. Kenako anaika zoikamo miyala ziwirizo pansalu zamʼmapewa za efodi chakutsogolo. 19 Atatero anapanga mphete ziwiri zagolide nʼkuziika mʼmakona awiri a chovala pachifuwa kumbali yamkati yokhudzana ndi efodi.+ 20 Ndiyeno anapanga mphete zina ziwiri zagolide nʼkuziika kutsogolo kwa efodi, mʼmunsi mwa nsalu ziwiri zamʼmapewa, pafupi ndi polumikizira, pamwamba pa malo amene lamba* woluka walumikizana ndi efodi. 21 Atatero anamanga chovala pachifuwacho ndi chingwe chabuluu. Chingwe chimenecho chinalowa mumphete za chovala pachifuwa komanso mphete za efodi. Zimenezi zinkathandiza kuti chovala pachifuwacho chisamasunthe koma chizikhala pamwamba pa lamba* woluka wa efodi, mogwirizana ndi zimene Yehova analamula Mose.
22 Ndiyeno anapanga malaya odula manja ovala mkati mwa efodi. Anapangidwa ndi woomba nsalu ndipo anawapanga ndi ulusi wabuluu wokhawokha.+ 23 Malaya odula manjawo anali otsegula pamwamba pake, pakatikati. Anali otsegula ngati chovala chakunkhondo cha mamba achitsulo. Potsegulapo panali popenderera mʼmphepete mwake kuti pasangʼambike. 24 Kenako, mumpendero wamʼmunsi wa malaya odula manjawo anapangamo zinthu zooneka ngati makangaza za ulusi wabuluu, ubweya wa nkhosa wapepo ndi ulusi wofiira kwambiri wopota pamodzi. 25 Anapanganso mabelu agolide woyenga bwino nʼkuwaika pakati pa makangaza, kuzungulira mpendero wamʼmunsi wa malaya odula manjawo. 26 Anaika belu kenako khangaza,* belu kenako khangaza, kuzungulira mpendero wamʼmunsi mwa malaya odula manja. Malayawo ankavala potumikira, mogwirizana ndi zimene Yehova analamula Mose.
27 Kenako anawomba nsalu ya ulusi wabwino kwambiri nʼkupangira mikanjo ya Aroni ndi ana ake.+ 28 Anapanganso nduwira+ ya nsalu yabwino kwambiri, mipango yokongola yokulunga kumutu+ ya nsalu zabwino kwambiri ndi makabudula a nsalu*+ za ulusi wopota wabwino kwambiri. 29 Anapanganso lamba wapamimba ndi ulusi wopota wabwino kwambiri, ulusi wabuluu, ubweya wa nkhosa wapepo ndi ulusi wofiira kwambiri, mogwirizana ndi zimene Yehova analamula Mose.
30 Atatero anapanga kachitsulo konyezimira kagolide woyenga bwino, chizindikiro chopatulika cha kudzipereka. Analembapo mawu akuti: “Yehova ndi Woyera.” Mawuwa anawalemba mochita kugoba ngati mmene amagobera chidindo.+ 31 Analowetsa chingwe chopangidwa ndi ulusi wabuluu mʼkachitsuloko kuti akamangirire panduwirayo, mogwirizana ndi zimene Yehova analamula Mose.
32 Choncho ntchito yonse ya chihema, kapena kuti chihema chokumanako, inatha ndipo Aisiraeli anachita zonse zimene Yehova analamula Mose.+ Anachitadi zomwezo.
33 Kenako anabweretsa kwa Mose chihema+ ndi zipangizo zake zonse, nsalu yake yophimba pamwamba,+ ngowe zake,+ mafelemu ake,+ ndodo zake+ zonyamulira, zipilala zake ndi zitsulo zoika pansi.+ 34 Anabweretsanso chophimba chihemacho cha zikopa za nkhosa zonyika mu utoto wofiira,+ chophimba chinanso chapamwamba pake cha chikopa cha akatumbu, katani,+ 35 likasa la Umboni, ndodo zake zonyamulira,+ chivundikiro chake,+ 36 tebulo, ziwiya zake zonse+ ndi mkate wachionetsero. 37 Anabweretsanso choikapo nyale chagolide woyenga bwino, nyale zake+ zondandalikidwa bwino, ziwiya zonse za choikapo nyalecho,+ mafuta a nyale,+ 38 guwa lansembe+ lagolide, mafuta odzozera,+ zofukiza zonunkhira,+ nsalu yotchinga+ pakhomo la chihemacho, 39 guwa lansembe lakopa,+ sefa wake wa zitsulo zakopa, ndodo zake zonyamulira,+ ziwiya zonse+ zogwiritsa ntchito paguwalo, beseni losambira ndi choikapo chake.+ 40 Anabweretsanso nsalu zotchingira bwalo, zipilala ndi zitsulo zokhazikapo zipilalazo,+ nsalu yotchinga+ pakhomo la bwalo, zikhomo za bwalo ndi zingwe zake,+ ziwiya zonse zogwiritsa ntchito pa utumiki wapachihema, kapena kuti chihema chokumanako, 41 zovala zolukidwa bwino zoti azivala potumikira mʼmalo opatulika, zovala zopatulika za Aroni wansembe+ ndi zovala za ana ake zoti azivala potumikira monga ansembe.
42 Aisiraeli anagwira ntchito yonse motsatira zonse zimene Yehova analamula Mose.+ 43 Mose atayendera ntchito yonse, anaona kuti achita zonse mogwirizana ndi zimene Yehova analamula, ndipo Mose anawadalitsa.