2 Mbiri
3 Kenako Solomo anayamba kumanga nyumba ya Yehova+ ku Yerusalemu paphiri la Moriya,+ pamalo amene Yehova anaonekera kwa Davide+ bambo ake. Anamanga nyumbayo pamalo amene Davide anali atakonza, pamalo opunthira mbewu a Orinani+ Muyebusi. 2 Iye anayamba kumanga nyumbayi pa tsiku lachiwiri mʼmwezi wachiwiri, mʼchaka cha 4 cha ufumu wake. 3 Maziko amene Solomo anayala omangira nyumba ya Mulungu woona, mogwirizana ndi muyezo wakale, anali mikono* 60 mulitali ndi mikono 20 mulifupi.+ 4 Khonde lakutsogolo linali mikono 20 mulitali ndipo linkafanana ndi mulifupi mwa nyumbayo. Kuchoka pansi kufika pamwamba, khondelo linali lalitali mikono 20* ndipo mkati mwake anakutamo ndi golide woyenga bwino.+ 5 Nyumba yaikuluyo anaikuta ndi matabwa a mitengo ya junipa,* kenako anaikutanso ndi golide wabwino.+ Atatero, anaikongoletsa ndi matcheni+ ndiponso zithunzi za mitengo yakanjedza zojambula mochita kugoba.+ 6 Anakongoletsanso nyumbayo poikuta ndi miyala yamtengo wapatali.+ Golide+ wakeyo anali wochokera ku Paravaimu. 7 Ndipo matabwa ake akudenga, pamakomo, makoma ndi zitseko za nyumbayo anazikuta ndi golide.+ Pamakoma ake anajambulapo akerubi mochita kugoba.+
8 Kenako iye anapanga chipinda cha Malo Oyera Koposa.+ Mulitali mwake chinali mikono 20 mofanana ndi mulifupi mwa nyumbayo ndipo mulifupi mwake chinali mikono 20. Anachikuta ndi golide wabwino wokwana matalente* 600.+ 9 Golide wa misomali yake anali wolemera masekeli* 50 ndipo zipinda zake zapadenga anazikuta ndi golide.
10 Mʼchipinda cha Malo Oyera Koposa anapangamo zifaniziro ziwiri za akerubi nʼkuzikuta ndi golide.+ 11 Mapiko a akerubiwo+ anali aatali mikono 20. Phiko limodzi la kerubi woyamba linali lalitali mikono 5 ndipo linagunda khoma la chipindacho. Phiko lina linalinso lalitali mikono 5 ndipo linakagunda phiko la kerubi wina. 12 Phiko limodzi la kerubi winayo linali lalitali mikono 5 ndipo linagunda khoma lina la chipindacho. Phiko lina linalinso lalitali mikono 5 ndipo linakagunda phiko la kerubi woyamba uja. 13 Mapiko otambasula a akerubiwo anali aatali mikono 20. Akerubiwo anali ataimirira ndipo nkhope zawo zinayangʼana mkati.*
14 Iye anapanganso katani*+ pogwiritsa ntchito ulusi wabuluu, ubweya wapepo, nsalu yofiira ndi nsalu yabwino kwambiri. Kenako anajambulapo akerubi.+
15 Kutsogolo kwa nyumbayo anamangako zipilala ziwiri+ zazitali mikono 35. Mutu wa chipilala chilichonse unali wautali mikono 5.+ 16 Atatero anapanganso matcheni okhala ngati ovala mʼkhosi nʼkuwaika pamwamba pa zipilalazo ndipo anapanga makangaza* 100 nʼkuwaika kumatcheniwo. 17 Zipilalazo anaziika kutsogolo kwa kachisi, china anachiika kumanja* china kumanzere.* Chipilala chakumanja anachipatsa dzina lakuti Yakini* ndipo chakumanzere anachipatsa dzina lakuti Boazi.*