1 Samueli
8 Samueli atakalamba, anaika ana ake aamuna kuti akhale oweruza mu Isiraeli. 2 Mwana wake woyamba anali Yoweli, ndipo wachiwiri anali Abiya.+ Iwo anali oweruza ku Beere-seba. 3 Ana akewa sanatsatire chitsanzo chake. Iwo ankakonda kupeza phindu mwachinyengo,+ kulandira ziphuphu+ ndiponso kupotoza chilungamo.+
4 Patapita nthawi, akulu onse a mu Isiraeli anasonkhana pamodzi nʼkupita kwa Samueli ku Rama. 5 Iwo anamuuza kuti: “Inuyo mwakalamba, koma ana anu sakutsatira chitsanzo chanu. Ndiye mutisankhire mfumu yoti izitiweruza ngati mitundu ina yonse.”+ 6 Koma Samueli sanasangalale atamuuza kuti: “Mutipatse mfumu yoti izitiweruza.” Kenako Samueli anapemphera kwa Yehova. 7 Yehova anauza Samueli kuti: “Mvera zonse zimene anthuwo akuuza, chifukwatu sanakane iwe koma akana ine kuti ndikhale mfumu yawo.+ 8 Zimene akuchitazi ndi zimene akhala akuchita kuyambira tsiku limene ndinawatulutsa ku Iguputo mpaka pano. Akhala akundisiya+ nʼkumatumikira milungu ina+ ndipo nʼzimenenso akuchitira iweyo. 9 Choncho mvera zimene akuuzazo. Koma uwachenjeze mwamphamvu, ndipo uwauze zimene munthu amene akufuna kuti akhale mfumu yawoyo azidzafuna kwa iwo.”
10 Samueli anafotokozera anthu amene ankamupempha kuti awapatse mfumuwo zonse zimene Yehova ananena. 11 Iye anawauza kuti: “Munthu amene adzakhale mfumu yanuyo azidzachita izi:+ Azidzatenga ana anu+ kuti azikayenda mʼmagaleta ake+ ndiponso kukwera pamahatchi* ake.+ Ena mwa ana anuwo azidzathamanga patsogolo pa magaleta ake. 12 Adzaika anthu ena kuti akhale atsogoleri a magulu a anthu 1,000+ ndi atsogoleri a magulu a anthu 50.+ Ena azidzalima minda yake,+ kukolola mbewu zake+ ndiponso kupanga zida zake zankhondo ndi zida zogwiritsa ntchito pamagaleta ake.+ 13 Ana anu aakazi adzawatenga kuti azikapanga mafuta onunkhira komanso azikaphika mikate ndi zakudya zina.+ 14 Adzakulandani malo anu abwino kwambiri komanso minda yanu ya mpesa ndi ya maolivi+ nʼkupatsa antchito ake. 15 Adzatenganso gawo limodzi la magawo 10 alionse a zokolola zamʼminda yanu ya mpesa komanso mʼminda ya mbewu zina nʼkuzipereka kwa nduna zake ndi antchito ake. 16 Komanso adzatenga antchito anu aamuna, antchito anu aakazi, abusa anu abwino kwambiri ndi abulu anu kuti azikawagwiritsa ntchito.+ 17 Pa ziweto zanu 10 zilizonse adzatengapo chiweto chimodzi+ ndipo inuyo mudzakhala antchito ake. 18 Tsiku lina mudzalira chifukwa chosankha kukhala ndi mfumu,+ koma Yehova sadzakuyankhani.”
19 Koma anthuwo anakana kumvera zomwe Samueli anawauza. Iwo anati: “Ayi. Ife tikufuna mfumu basi. 20 Zikatero tikhala ngati mitundu ina yonse, ndipo mfumu yathuyo ndi imene izitiweruza ndiponso kutitsogolera pokamenya nkhondo.” 21 Samueli atamva zimene anthuwo ananena, anafotokozera Yehova zonsezo. 22 Yehova anauza Samueli kuti: “Mvera zimene anenazo ndipo asankhire mfumu yoti iziwalamulira.”+ Kenako Samueli anauza Aisiraeliwo kuti: “Aliyense apite kumzinda wakwawo.”