Ekisodo
18 Ndiyeno Yetero, wansembe wa ku Midiyani, apongozi ake a Mose,+ anamva zonse zimene Mulungu anachitira Mose ndi anthu ake Aisiraeli komanso mmene Yehova anawatulutsira ku Iguputo.+ 2 Kenako Yetero apongozi ake a Mose, anatenga Zipora, mkazi wa Mose, amene Mose anali atamutumiza kwawo. 3 Anatenganso ana aamuna awiri a Zipora.+ Mwana wina, Mose anamupatsa dzina lakuti Gerisomu,*+ ndipo anati: “Chifukwa ndakhala mlendo mʼdziko lachilendo.” 4 Mwana winayo anamupatsa dzina lakuti Eliezere,* ndipo anati: “Mulungu wa atate anga ndi amene amandithandiza, chifukwa anandipulumutsa kwa Farao amene ankafuna kundipha.”+
5 Choncho Yetero, apongozi ake a Mose, limodzi ndi ana aamuna a Mose ndi mkazi wake, anapita kwa Mose mʼchipululu, kuphiri la Mulungu woona, kumene anamanga msasa.+ 6 Ndiyeno anatumiza uthenga kwa Mose kuti: “Ine Yetero, mpongozi wako,+ ndikubwera limodzi ndi mkazi wako ndi ana ako awiri.” 7 Nthawi yomweyo Mose anatuluka kukachingamira apongozi ake, ndipo anagwada nʼkuwerama, kenako anawakisa.* Iwo analonjerana, atatero anapita kukalowa mutenti.
8 Mose anafotokozera apongozi akewo zonse zimene Yehova anachitira Farao ndi Iguputo pofuna kuthandiza Isiraeli.+ Anawafotokozera mavuto onse amene anakumana nawo mʼnjira+ komanso mmene Yehova anawapulumutsira. 9 Yetero anasangalala kwambiri atamva zabwino zonse zimene Yehova anachitira Aisiraeli powapulumutsa ku Iguputo.* 10 Ndiyeno Yetero anati: “Yehova atamandike, amene anakupulumutsani ku Iguputo ndiponso kwa Farao, amenenso analanditsa anthuwa kwa Aiguputo omwe ankawazunza. 11 Tsopano ndadziwa kuti Yehova ndi wamkulu kuposa milungu ina yonse,+ chifukwa cha zimene anachitira anthu amene ankachita zinthu modzikuza pamaso pa anthu ake.” 12 Kenako Yetero, apongozi ake a Mose, anabweretsa nsembe yopsereza ndi nsembe zina kwa Mulungu. Ndipo Aroni ndi akulu onse a Isiraeli anabwera nʼkudyera limodzi chakudya ndi apongozi ake a Mose, pamaso pa Mulungu woona.
13 Tsiku lotsatira, Mose anakhala pansi monga mwa masiku onse kuti atumikire anthu monga woweruza, ndipo anthu ankaima pamaso pa Mose kuyambira mʼmawa mpaka madzulo. 14 Apongozi a Mose ataona zonse zimene iye ankachitira anthuwo anati: “Kodi anthuwa ukuchita nawo chiyani? Nʼchifukwa chiyani wangokhala wekha ndipo anthu onsewa aima pamaso pako kuyambira mʼmawa mpaka madzulo?” 15 Mose anayankha apongozi akewo kuti: “Chifukwa anthuwa akumabwera kwa ine kuti adzamve malangizo a Mulungu. 16 Akakhala ndi mlandu pakati pawo akumabwera nawo kwa ine, ndipo ndikumaweruza nʼkuwauza chigamulo cha Mulungu woona ndi malamulo ake.”+
17 Ndiyeno apongozi a Mose anamuuza kuti: “Zimene ukuchitazi si zabwino. 18 Ndithu iwe ndi anthu amene uli nawowa mutopa nazo zimenezi, chifukwa ntchito imeneyi ndi yaikulu kwambiri ndipo sungathe kuigwira wekha. 19 Tsopano mvera zimene ndikufuna kukuuza. Ndikupatsa malangizo ndipo Mulungu adzakhala nawe.+ Iweyo uzilankhula ndi Mulungu woona mʼmalo mwa anthuwa+ komanso uzipititsa milandu kwa Mulungu woona.+ 20 Ndipo uziwaphunzitsa za malangizo ndi malamulo+ komanso kuwauza njira imene ayenera kuyendamo ndi ntchito imene ayenera kugwira. 21 Pakati pa anthuwa, usankhepo amuna oyenerera,+ oopa Mulungu, okhulupirika, odana ndi kupeza phindu mwachinyengo.+ Amenewa uwaike kuti akhale atsogoleri a anthuwa, ndipo pakhale atsogoleri a magulu a anthu 1,000, atsogoleri a magulu a anthu 100, atsogoleri a magulu a anthu 50 ndi atsogoleri a magulu a anthu 10.+ 22 Pakakhala mlandu uliwonse atsogoleri amenewa aziweruza anthuwo. Mlandu ukakhala wovuta azibwera nawo kwa iwe,+ koma mlandu uliwonse waungʼono, aziweruza. Uwalole amunawa kuti azikuthandiza kuchita zimenezi, kuti udzichepetsere ntchito.+ 23 Ukachita zimenezi, ndipo ngati zikugwirizana ndi zimene Mulungu akufuna, pamenepo udzaikwanitsa ntchitoyi komanso anthuwa adzabwerera kwawo akusangalala.”
24 Nthawi yomweyo Mose anamvera zimene apongozi ake anamuuza ndipo anachita zonse zimene ananena. 25 Mose anasankha amuna oyenerera mu Isiraeli monse kuti akhale atsogoleri a anthu. Anasankha atsogoleri a magulu a anthu 1,000, atsogoleri a magulu a anthu 100, atsogoleri a magulu a anthu 50 ndi atsogoleri a magulu a anthu 10. 26 Choncho iwo ankaweruza anthuwo pakakhala mlandu. Mlandu wovuta ankapita nawo kwa Mose,+ koma mlandu uliwonse waungʼono ankauweruza. 27 Kenako Mose anatsanzikana ndi apongozi ake+ ndipo iwo anabwerera kwawo.