Ezara
5 Mneneri Hagai+ ndi mneneri Zekariya+ mdzukulu wa Ido,+ analosera kwa Ayuda a ku Yuda ndi ku Yerusalemu mʼdzina la Mulungu wa Isiraeli yemwe anali nawo. 2 Pa nthawi imeneyi ndi pamene Zerubabele+ mwana wa Salatiyeli ndi Yesuwa+ mwana wa Yehozadaki anayamba kumanganso nyumba ya Mulungu+ yomwe inali ku Yerusalemu. Aneneri a Mulungu anali nawo limodzi ndipo ankawathandiza.+ 3 Pa nthawi imeneyo Tatenai bwanamkubwa wa kutsidya lina la Mtsinje,* Setara-bozenai ndi anzawo anabwera kwa Ayudawo nʼkuwafunsa kuti: “Kodi ndi ndani wakulamulani kuti mumange nyumbayi komanso kumaliza ntchitoyi?”* 4 Anawafunsanso kuti: “Kodi anthu amene akumanga nyumba imeneyi mayina awo ndi ndani?” 5 Mulungu ankayangʼanira* akulu a Ayuda+ ndipo anthuwo sanawasiyitse ntchitoyo mpaka pamene analemba kalata yokhudza nkhaniyo nʼkuitumiza kwa Dariyo ndiponso pamene kalata yoyankha nkhaniyi inabwera.
6 Izi nʼzimene zinali mʼkalata imene Tatenai bwanamkubwa wa kutsidya lina la Mtsinje, Setara-bozenai ndi anzake ndiponso abwanamkubwa aangʼono amene anali kutsidya lina la Mtsinje, anatumiza kwa mfumu Dariyo. 7 Anatumiza uthenga kwa iye ndipo analemba kuti:
“Kwa Mfumu Dariyo:
Mtendere ukhale nanu. 8 Inu mfumu dziwani kuti ife tinapita kuchigawo cha Yuda kunyumba ya Mulungu wamkulu. Kumeneko takapeza kuti nyumbayo akuimanga ndi miyala yochita kugubuduza ndiponso akuika matabwa mʼmakoma ake. Iwo akugwira ntchitoyo mwakhama ndipo ikuyenda bwino. 9 Ndiyeno tinafunsa akuluakulu awo kuti: ‘Kodi ndi ndani wakulamulani kuti mumange nyumbayi komanso kumaliza ntchitoyi?’*+ 10 Tinawafunsanso mayina awo kuti tikuuzeni nʼcholinga choti tilembe mayina a anthu amene akuwatsogolera.
11 Iwo anatiyankha kuti: ‘Ndife atumiki a Mulungu wakumwamba ndi dziko lapansi. Tikumanganso nyumba imene inamangidwa zaka zambiri zapitazo, imene mfumu yaikulu ya Isiraeli inamanga nʼkuimaliza.+ 12 Koma chifukwa chakuti makolo athu anakwiyitsa Mulungu wakumwamba,+ iye anawapereka mʼmanja mwa Nebukadinezara+ mfumu ya Babulo Mkasidi, yemwe anagwetsa nyumbayi+ nʼkutenga anthu kupita nawo ku ukapolo ku Babulo.+ 13 Koma mʼchaka choyamba cha Koresi mfumu ya Babulo, mfumu Koresi inaika lamulo loti nyumba ya Mulunguyi imangidwenso.+ 14 Komanso, mfumu Koresi inachotsa mʼkachisi wa ku Babulo ziwiya zagolide ndi zasiliva zimene Nebukadinezara anazitenga mʼkachisi wa Mulungu yemwe anali ku Yerusalemu, nʼkupita nazo kukachisi wa ku Babuloyo.+ Ndiyeno anazipereka kwa munthu wina dzina lake Sezibazara,*+ amene Koresi anamusankha kuti akhale bwanamkubwa.+ 15 Koresiyo anamuuza kuti: “Tenga ziwiyazi, ukaziike mʼkachisi amene ali ku Yerusalemu. Ukaonetsetse kuti nyumba ya Mulungu yamangidwanso pamalo ake.”+ 16 Sezibazarayo atabwera anamanga maziko a nyumba ya Mulungu+ yomwe ili ku Yerusalemu. Kuyambira nthawi imeneyo mpaka pano nyumbayi ikumangidwabe ndipo sinamalizidwe.’+
17 Tsopano ngati inu mfumu mukuona kuti nʼkoyenera, uzani anthu kuti afufuze mʼnyumba ya chuma cha mfumu imene ili ku Babuloko. Muwauze kuti aone ngati mfumu Koresi inaikadi lamulo loti nyumba ya Mulungu yomwe ili ku Yerusalemu+ imangidwenso. Kenako inu mfumu mutitumizire chigamulo chanu pa nkhani imeneyi.”