2 Mbiri
36 Kenako anthu amʼdzikolo anatenga Yehoahazi+ mwana wa Yosiya nʼkumuika kukhala mfumu ku Yerusalemu mʼmalo mwa bambo ake.+ 2 Yehoahazi anayamba kulamulira ali ndi zaka 23 ndipo analamulira miyezi itatu ku Yerusalemu. 3 Koma mfumu ya Iguputo inamuchotsa pa udindo wake ku Yerusalemu, nʼkulamula anthu amʼdzikolo kuti aipatse matalente* 100 a siliva ndi talente imodzi ya golide.+ 4 Kenako, mfumu ya Iguputo inaika Eliyakimu, mʼbale wake wa Yehoahazi, kukhala mfumu ya Yuda ndi Yerusalemu ndipo inamusintha dzina kuti akhale Yehoyakimu. Koma Neko+ anatenga Yehoahazi, mʼbale wake wa Eliyakimu, nʼkupita naye ku Iguputo.+
5 Yehoyakimu+ anayamba kulamulira ali ndi zaka 25 ndipo analamulira zaka 11 ku Yerusalemu. Iye anapitiriza kuchita zoipa pamaso pa Yehova Mulungu wake.+ 6 Kenako Nebukadinezara+ mfumu ya Babulo anabwera kudzamʼmanga ndi zomangira ziwiri zakopa* nʼkupita naye ku Babulo.+ 7 Nebukadinezara anatenga ziwiya zina za mʼnyumba ya Yehova nʼkupita nazo ku Babulo ndipo anakaziika mʼnyumba yake yachifumu.+ 8 Nkhani zina zokhudza Yehoyakimu, zonyansa zimene anachita ndiponso zoipa zimene zinapezeka zokhudza iyeyo, zinalembedwa mʼBuku la Mafumu a Isiraeli ndi Yuda. Kenako mwana wake Yehoyakini anakhala mfumu mʼmalo mwake.+
9 Yehoyakini+ anayamba kulamulira ali ndi zaka 18 ndipo analamulira miyezi itatu ndi masiku 10 ku Yerusalemu. Iye ankachita zoipa pamaso pa Yehova.+ 10 Chakumayambiriro kwa chaka, Mfumu Nebukadinezara inatuma asilikali ake omwe anakamutenga nʼkubwera naye ku Babulo+ limodzi ndi zinthu zabwino zamʼnyumba ya Yehova.+ Komanso Nebukadinezara anasankha Zedekiya, yemwe anali mʼbale wa bambo ake a Yehoyakini, kuti akhale mfumu ya Yuda ndi Yerusalemu.+
11 Zedekiya+ anayamba kulamulira ali ndi zaka 21 ndipo analamulira zaka 11 ku Yerusalemu.+ 12 Iye anapitiriza kuchita zoipa pamaso pa Yehova Mulungu wake. Ndipo sanadzichepetse pamaso pa mneneri Yeremiya+ yemwe ankalankhula molamulidwa ndi Yehova. 13 Kuwonjezera pamenepo, Zedekiya anagalukira Mfumu Nebukadinezara+ yomwe inamulumbiritsa mʼdzina la Mulungu. Zedekiya anapitiriza kukhala wosamva komanso kuumitsa mtima wake ndipo anakana kubwerera kwa Yehova Mulungu wa Isiraeli. 14 Anthu ndi atsogoleri onse a ansembe anali osakhulupirika ngakhale pangʼono ndipo ankachita zonyansa zonse zimene anthu a mitundu ina ankachita. Iwo anaipitsa nyumba ya Yehova+ imene iye anaiyeretsa ku Yerusalemu.
15 Yehova Mulungu wa makolo awo anapitiriza kuwachenjeza kudzera mwa atumiki ake. Ankawachenjeza mobwerezabwereza chifukwa ankamvera chisoni anthu akewo ndiponso malo ake okhala. 16 Koma iwo anapitiriza kunyoza atumiki a Mulungu woona,+ kunyoza mawu ake+ ndiponso kuseka aneneri ake.+ Iwo anafika poti panalibenso chiyembekezo choti angathe kuchiritsidwa. Kenako Yehova anawakwiyira kwambiri nʼkuwalanga.+
17 Choncho anawabweretsera mfumu ya Akasidi+ yomwe inapha anyamata awo ndi lupanga+ mʼnyumba yopatulika.+ Sinamvere chisoni mnyamata kapena namwali, wachikulire kapena wodwala.+ Mulungu anapereka zonse mʼmanja mwake.+ 18 Mfumuyo inatenga ziwiya zonse, zazikulu ndi zazingʼono, zamʼnyumba ya Mulungu woona. Inatenganso chuma cha mʼnyumba ya Yehova, chuma cha mfumu ndi cha akalonga ake. Inatenga chilichonse nʼkupita nacho ku Babulo.+ 19 Inatentha nyumba ya Mulungu woona,+ kugwetsa mpanda wa Yerusalemu,+ kutentha nyumba zonse zokhala ndi mipanda yolimba kwambiri ndiponso zinthu zonse zamtengo wapatali.+ 20 Nebukadinezara anatenga anthu amene sanaphedwe ndi lupanga+ nʼkupita nawo ku Babulo. Anthuwo anakhala antchito ake+ ndiponso a ana ake mpaka pamene ufumu wa Perisiya unayamba kulamulira.+ 21 Zimenezi zinachitika pokwaniritsa mawu a Yehova amene ananena kudzera mwa Yeremiya,+ mpaka pamene dzikolo linalipira masabata ake.+ Masiku onse amene dzikolo linali bwinja linkasunga sabata mpaka zinakwana zaka 70.+
22 Mʼchaka choyamba cha Koresi+ mfumu ya Perisiya, pokwaniritsa mawu a Yehova amene analankhula kudzera mwa Yeremiya,+ Yehova analimbikitsa Koresi mfumu ya Perisiya kuti alengeze mu ufumu wake wonse, zomwenso iye analemba mʼmakalata,+ kuti: 23 “Koresi mfumu ya Perisiya wanena kuti, ‘Yehova Mulungu wakumwamba wandipatsa maufumu onse apadziko lapansi.+ Iye wandituma kuti ndimumangire nyumba ku Yerusalemu mʼdziko la Yuda.+ Aliyense amene ali pakati panu mwa anthu onse amene amamutumikira, Yehova Mulungu wake akhale naye ndipo apite.’”+