Machitidwe a Atumwi
9 Koma Saulo anapitiriza kuopseza ophunzira a Ambuye+ komanso ankafunitsitsa kuwapha. Choncho anapita kwa mkulu wa ansembe 2 kukapempha makalata a chilolezo kuti apite nawo kumasunagoge a ku Damasiko. Anapempha makalatawo kuti akakapeza wina aliyense wotsatira Njirayo,*+ mwamuna kapena mkazi, akamumange nʼkubwera naye ku Yerusalemu.
3 Ali pa ulendo wakewo, atatsala pangʼono kufika ku Damasiko, mwadzidzidzi anangoona kuwala kochokera kumwamba kutamuzungulira.+ 4 Zitatero anagwa pansi ndipo anamva mawu akuti: “Saulo, Saulo, nʼchifukwa chiyani ukundizunza?” 5 Iye anafunsa kuti: “Mbuyanga, ndinu ndani kodi?” Anamuyankha kuti: “Ndine Yesu,+ amene ukumuzunza.+ 6 Nyamuka, ulowe mumzindawo, ndipo ukauzidwa zoyenera kuchita.” 7 Anthu amene anali naye limodzi pa ulendowo, anangoima kusowa chonena. Iwo anamva ndithu kuti munthu akulankhula, koma sanaone aliyense.+ 8 Kenako Saulo anaimirira, koma ngakhale kuti ankayangʼana, sankaona chilichonse. Choncho anamugwira dzanja nʼkumulondolera ku Damasiko. 9 Saulo anakhala masiku atatu asakuona+ ndipo sanadye kapena kumwa chilichonse.
10 Ku Damasiko kunali wophunzira wina dzina lake Hananiya.+ Ndiyeno Ambuye analankhula naye mʼmasomphenya kuti: “Hananiya!” Iye anayankha kuti: “Ine Ambuye.” 11 Kenako Ambuyewo anamuuza kuti: “Nyamuka upite ku Msewu Wowongoka. Ukakafika panyumba ya Yudasi, ukafunse za munthu wina dzina lake Saulo, wa ku Tariso.+ Iyeyo akupemphera, 12 ndipo mʼmasomphenya waona munthu dzina lake Hananiya atafika nʼkumugwira pamutu* kuti ayambenso kuona.”+ 13 Koma Hananiya anayankha kuti: “Ambuye, ndamva kwa anthu ambiri za munthu ameneyu. Ndamva zoipa zonse zimene anachitira oyera anu ku Yerusalemu. 14 Ndipo panopa ansembe aakulu amupatsa mphamvu kuti amange onse oitana pa dzina lanu.”+ 15 Koma Ambuye anamuuza kuti: “Pita, chifukwa munthu ameneyu ndi chiwiya changa+ chosankhidwa chotengera dzina langa kupita nalo kwa anthu a mitundu ina+ komanso kwa mafumu+ ndi Aisiraeli. 16 Popeza ndidzamuonetsa bwinobwino mavuto onse amene adzakumane nawo chifukwa cha dzina langa.”+
17 Choncho Hananiya anapita nʼkukalowa mʼnyumbamo. Ndiyeno anamugwira pamutu* nʼkunena kuti: “Mʼbale wanga Saulo, Ambuye Yesu amene anaonekera kwa iwe pamsewu umene unadzera, wandituma. Wandituma kwa iwe kuti uyambenso kuona komanso udzazidwe ndi mzimu woyera.”+ 18 Nthawi yomweyo tinthu tooneka ngati mamba a nsomba tinagwa kuchokera mʼmaso mwa Saulo ndipo anayambanso kuona. Kenako anapita kukabatizidwa. 19 Atadya chakudya anapezanso mphamvu.
Iye anakhala ndi ophunzira ku Damasiko kwa masiku angapo.+ 20 Nthawi yomweyo anayamba kulalikira za Yesu mʼmasunagoge, kuti ameneyu ndi Mwana wa Mulungu. 21 Koma anthu onse amene anamumva akulankhula, anadabwa kwambiri ndipo ankanena kuti: “Kodi munthu uyu si uja ankazunza anthu a ku Yerusalemu oitana pa dzina limeneli?+ Kodi chimene anabwerera kuno si kudzagwira anthu nʼkupita nawo kwa ansembe aakulu?”+ 22 Komabe Saulo anapitiriza kukhala ndi mphamvu zambiri ndipo ankathetsa nzeru Ayuda a ku Damasiko powafotokozera mfundo zomveka zotsimikizira kuti Yesu ndi Khristu.+
23 Patapita masiku ambiri, Ayudawo anakonza chiwembu choti amuphe.+ 24 Koma Saulo anadziwa za chiwembucho. Iwo ankayangʼananso mosamala mʼmageti masana onse ndiponso usiku kuti amuphe. 25 Choncho usiku, ophunzira ake anamuika mʼdengu nʼkumutulutsira pawindo la mpanda nʼkumutsitsira kunja.+
26 Atafika ku Yerusalemu+ anayesetsa kuti agwirizane ndi ophunzira kumeneko. Koma onse ankamuopa, chifukwa sankakhulupirira kuti ndi wophunzira. 27 Choncho Baranaba+ anamuthandiza popita naye kwa atumwi. Ndipo anawafotokozera mwatsatanetsatane mmene Saulo anaonera Ambuye+ amene analankhula naye pamsewu. Anawafotokozeranso mmene Saulo analankhulira molimba mtima ku Damasiko mʼdzina la Yesu.+ 28 Zitatero anapitiriza kukhala nawo nʼkumayenda momasuka mu Yerusalemu, ndipo ankalankhula molimba mtima mʼdzina la Ambuye. 29 Iye ankalankhulana ndiponso kutsutsana ndi Ayuda olankhula Chigiriki. Koma iwo anayamba kufufuza njira yoti amuphere.+ 30 Abale atazindikira zimenezi, anapita naye ku Kaisareya nʼkumutumiza ku Tariso.+
31 Ndiyeno mpingo ku Yudeya konse, ku Galileya ndi ku Samariya+ unayamba kukhala pamtendere ndipo unali wolimba. Chifukwa choti ophunzira ankaopa Yehova* komanso ankalimbikitsidwa ndi mzimu woyera,+ mpingowo unkakulirakulira.
32 Pamene Petulo ankayenda mʼdera lonselo, anafikanso kwa oyera amene ankakhala ku Luda.+ 33 Kumeneko anapeza munthu wina dzina lake Eneya, yemwe anakhala chigonere pabedi lake kwa zaka 8 chifukwa anali wakufa ziwalo. 34 Ndiyeno Petulo anamuuza kuti: “Eneya, Yesu Khristu akukuchiritsa.+ Dzuka ndipo ukonze pabedi lakolo.”+ Nthawi yomweyo anadzuka. 35 Anthu onse a ku Luda ndiponso kuchigwa cha Sharoni atamuona, anayamba kukhulupirira Ambuye.
36 Ku Yopa kunali wophunzira wina dzina lake Tabita, dzina limene limamasuliridwa kuti Dorika.* Tabita ankachita zinthu zambiri zabwino ndiponso ankapatsa ena mphatso zambiri zachifundo. 37 Ndiyeno mʼmasiku amenewo iye anadwala ndipo anamwalira. Choncho anamusambitsa nʼkukamugoneka mʼchipinda chamʼmwamba. 38 Popeza kuti Luda anali pafupi ndi Yopa, ophunzirawo atamva kuti Petulo ali mumzindawu, anatuma anthu awiri kukamupempha kuti: “Chonde mubwere kwathu mwamsanga.” 39 Petulo atamva zimenezi, ananyamuka nʼkupita nawo limodzi. Atafika, anamutenga nʼkupita naye mʼchipinda chamʼmwamba chija. Akazi onse amasiye anabwera kwa iye akulira ndipo ankamuonetsa zovala zambiri ndiponso mikanjo imene Dorika ankasoka pamene anali nawo. 40 Petulo anauza anthu onse kuti atuluke,+ ndiyeno anagwada nʼkupemphera. Kenako anatembenuka nʼkuyangʼana mtembowo nʼkunena kuti: “Tabita, dzuka!” Ndiyeno mayiyo anatsegula maso ndipo ataona Petulo, anadzuka nʼkukhala tsonga.+ 41 Petulo anamugwira dzanja nʼkumuimiritsa. Atatero anaitana oyerawo komanso akazi amasiye aja, ndipo onse anaona kuti Tabita ali moyo.+ 42 Izi zinadziwika ku Yopa konse ndipo anthu ambiri anakhulupirira Ambuye.+ 43 Petulo anakhalabe ku Yopa kwa masiku angapo ndipo ankakhala kwa munthu wina wofufuta zikopa, dzina lake Simoni.+