Esitere
2 Kenako mkwiyo wa Mfumu Ahasiwero+ utachepa, anakumbukira zimene Vasiti anachita,+ komanso chilango chimene anapatsidwa.+ 2 Ndiyeno atumiki a mfumu anati: “Pakhale anthu oti akufufuzireni inu mfumu anamwali okongola. 3 Ndiyeno inu mfumu musankhe anthu mʼzigawo zonse za ufumu wanu.+ Anthuwo asonkhanitse anamwali okongola kunyumba ya mfumu ya ku Susani* yokhala ndi mpanda wolimba kwambiri ndipo azikhala mʼnyumba ya akazi. Atsikanawa aziyangʼaniridwa ndi Hegai,+ munthu wofulidwa wa mfumu amene amayangʼanira akazi. Ndipo kumeneko atsikanawo azikawapaka mafuta okongoletsa. 4 Mtsikana amene mfumu idzasangalale naye kwambiri adzakhala mfumukazi mʼmalo mwa Vasiti.”+ Mawu amenewa anasangalatsa mfumu ndipo inachitadi zomwezo.
5 Panali munthu wina, Myuda, amene ankakhala kunyumba ya mfumu ya ku Susani*+ yokhala ndi mpanda wolimba kwambiri. Dzina lake anali Moredikayi.+ Moredikayi anali mwana wa Yairi, Yairi anali mwana wa Simeyi ndipo Simeyi anali mwana wa Kisi wa fuko la Benjamini.+ 6 Moredikayi ndi anthu ena anatengedwa ku Yerusalemu kupita ku ukapolo pamodzi ndi Yekoniya*+ mfumu ya Yuda, amene Nebukadinezara mfumu ya Babulo anamutenga kupita naye ku ukapolo. 7 Moredikayi ndi amene ankalera Hadasa,* amene ndi Esitere, mwana wa achimwene awo a bambo ake,+ chifukwa analibe bambo kapena mayi. Mtsikanayu anali wooneka bwino ndiponso wokongola kwambiri. Bambo ndi mayi a mtsikanayu atamwalira, Moredikayi anamʼtenga nʼkumakhala naye ngati mwana wake. 8 Ndiyeno anthu atalengeza mawu a mfumu ndiponso lamulo lake, komanso atasonkhanitsa atsikana ambiri kunyumba ya mfumu ku Susani* kuti Hegai aziwayangʼanira,+ Esitere nayenso anatengedwa kupita kunyumba ya mfumuyo kuti azikayangʼaniridwa ndi Hegai amene ankayangʼanira akazi.
9 Hegai anasangalala naye mtsikanayu moti ankamukomera mtima.* Choncho nthawi yomweyo anakonza za mafuta okongoletsa oti azipakidwa+ komanso chakudya choti azipatsidwa. Anamupatsanso atsikana 7 amene anachita kuwasankha kuchokera kunyumba ya mfumu. Kenako anamusamutsa pamodzi ndi atsikanawo nʼkuwapatsa malo abwino kwambiri mʼnyumba ya akaziyo. 10 Esitere sananene za mtundu wa anthu ake+ kapena za abale ake, chifukwa Moredikayi+ anali atamulangiza kuti asauze aliyense.+ 11 Tsiku lililonse Moredikayi ankadutsa kutsogolo kwa bwalo la nyumba ya akazi kuti adziwe ngati Esitere ali bwino komanso zimene zikumuchitikira.
12 Mtsikana aliyense ankakhala ndi nthawi yake yokaonekera kwa Mfumu Ahasiwero akamaliza kumuchitira zonse zimene amayenera kuwachitira akazi pa miyezi 12. Atsikanawo ankawapaka mafuta a mule*+ miyezi 6 kenako nʼkuwapakanso mafuta a basamu+ pamodzi ndi mafuta enanso okongoletsa miyezi inanso 6. Akachita zimenezi ankakhala kuti amaliza dongosolo lonse lowakongoletsera. 13 Akatero mtsikana aliyense ankapita kwa mfumu. Akamachoka kunyumba ya akazi kupita kunyumba ya mfumu, ankamupatsa chilichonse chimene wapempha. 14 Mtsikanayo ankapita kwa mfumu madzulo nʼkubwerako mʼmawa ndipo ankapita kunyumba yachiwiri ya akazi, imene Sasigazi ankayangʼanira. Sasigazi anali munthu wofulidwa wa mfumu+ yemwe ankayangʼanira akazi aangʼono* a mfumu. Mtsikanayo sankapitanso kwa mfumu pokhapokha ngati mfumuyo yasangalala naye ndipo yamuitanitsa pomutchula dzina.+
15 Esitere anali mwana wa Abihaili, mchimwene wawo wa bambo ake a Moredikayi. Moredikayi anamutenga nʼkumakhala naye ngati mwana wake.+ Ndiyeno nthawi yoti Esitere akaonekere kwa mfumu itakwana, sanapemphe kalikonse kupatulapo zimene Hegai anamuuza. Hegai anali munthu wofulidwa wa mfumu amenenso ankayangʼanira akazi. (Pa nthawi yonseyi aliyense womuona Esitere ankamukonda.) 16 Esitere anapita naye kunyumba yachifumu ya Mfumu Ahasiwero mʼmwezi wa 10 umene ndi mwezi wa Tebeti,* mʼchaka cha 7+ cha ulamuliro wa mfumuyi. 17 Ndiyeno mfumu inakonda kwambiri Esitere kuposa akazi ena onse, moti inasangalala naye ndipo inaona kuti ndi wabwino* kuposa anamwali ena onse. Choncho mfumu inamuveka duku lachifumu kumutu kwake nʼkumuika kukhala mfumukazi+ mʼmalo mwa Vasiti.+ 18 Kenako mfumu inakonzera akalonga ake ndi atumiki ake onse phwando lalikulu, phwando la Esitere. Ndiyeno mfumu inamasula akaidi amʼzigawo zake zonse, ndipo inayamba kupereka mphatso mogwirizana ndi chuma chimene mfumuyo inali nacho.
19 Pamene anamwali*+ anasonkhanitsidwa kachiwiri, Moredikayi anali atakhala pansi kugeti la mfumu. 20 Esitere sananene zokhudza abale ake ndiponso anthu a mtundu wake,+ mogwirizana ndi zimene Moredikayi anamulangiza. Esitere ankachita zimene Moredikayi wanena ngati mmene ankachitira pa nthawi imene ankakhala naye.+
21 Mʼmasiku amenewo, pamene Moredikayi ankakhala pageti la mfumu, Bigitana ndi Teresi, omwe anali nduna ziwiri zapanyumba ya mfumu, omwenso anali alonda apakhomo, anakwiya ndipo anakonza zoti aphe Mfumu Ahasiwero. 22 Koma Moredikayi anamva zimenezi ndipo nthawi yomweyo anauza Mfumukazi Esitere. Kenako Esitere anakalankhula ndi mfumu mʼmalo mwa Moredikayi.* 23 Choncho nkhaniyi inafufuzidwa ndipo zinadziwika kuti inali yoona, moti Bigitana ndi Teresi anapachikidwa pamtengo. Zimenezi zinalembedwa pamaso pa mfumu mʼbuku la mbiri ya masiku amenewo.+