Zekariya
9 Uthenga wokhudza dziko la Hadiraki:
“Uwu ndi uthenga wa Yehova wokhudza dziko la Hadiraki,
Ndipo makamaka ukupita kumzinda wa Damasiko.+
Chifukwa maso a Yehova ali pa anthu,+
Komanso pa mafuko onse a Isiraeli.
2 Uthengawu ukupitanso kwa Hamati+ amene anachita naye malire.
Komanso kwa Turo+ ndi Sidoni+ chifukwa ali ndi nzeru zambiri.+
3 Turo anamanga malo okwera omenyerapo nkhondo.
Anadziunjikira siliva wambiri ngati fumbi,
Ndiponso golide wambiri ngati dothi lamʼmisewu.+
4 Yehova adzamulanda zinthu zake.
Gulu lake lankhondo adzaliponyera mʼnyanja.+
Ndipo iye adzatenthedwa ndi moto.+
5 Asikeloni adzaona zimenezi ndipo adzachita mantha.
Gaza adzamva ululu waukulu.
Izi zidzachitikiranso Ekironi chifukwa amene ankamudalira wachititsidwa manyazi.
Ku Gaza sikudzakhalanso mfumu,
Ndipo ku Asikeloni sikudzakhalanso anthu.+
6 Mwana wochokera mu mtundu wina wa anthu azidzakhala ku Asidodi,
Ndipo ndidzathetsa kunyada kwa Afilisiti.+
7 Ndidzachotsa zinthu zamagazi mʼkamwa mwawo,
Komanso chakudya chonyansa pakati pa mano awo.
Ndipo aliyense amene adzatsale, adzakhala wa Mulungu wathu.
Iye adzakhala ngati mtsogoleri mu Yuda,+
Ndipo Ekironi adzakhala ngati munthu wa Chiyebusi.+
8 Ndidzamanga msasa kunja kwa nyumba yanga kuti ndizidzailondera,+
Moti sipadzakhala munthu wolowa kapena kutuluka.
Aliyense amene ankawagwiritsa ntchito* sadzadutsanso pakati pawo+
Chifukwa ine ndaona ndi maso anga.*
9 Iwe mwana wamkazi wa Ziyoni* sangalala kwambiri.
Fuula mokondwera iwe mwana wamkazi wa Yerusalemu.*
Taona, mfumu yako ikubwera kwa iwe.+
Mfumuyo ndi yolungama ndipo ikubweretsa chipulumutso.*
Ndi yodzichepetsa+ ndipo ikubwera itakwera bulu.
Ikubwera itakwera mwana wamphongo wa bulu.+
10 Ndidzachotsa magaleta ankhondo ku Efuraimu
Ndiponso mahatchi ku Yerusalemu.
Mauta omenyera nkhondo adzachotsedwa.
Mfumuyo idzalalikira uthenga wamtendere kwa anthu a mitundu ina.+
Ulamuliro wake udzayambira kunyanja mpaka kukafika kunyanja ina.
Ndiponso kuchokera ku Mtsinje* mpaka kumalekezero a dziko lapansi.+
11 Koma mkazi iwe, chifukwa cha magazi a pangano limene unapangana ndi ine,
Ndidzatulutsa akaidi ako mʼdzenje lopanda madzi.+
12 Inu akaidi amene muli ndi chiyembekezo, bwererani kumalo a chitetezo champhamvu.+
Lero ndikukuuza kuti,
‘Mkazi iwe, ndidzakupatsa magawo awiri a madalitso.+
13 Ndidzapinda Yuda kuti akhale uta wanga.
Efuraimu ndidzamuika pa uta umenewo ngati muvi.
Ndidzadzutsa ana ako, iwe Ziyoni,
Kuti aukire ana a Girisi.
Ndipo ndidzakusandutsa lupanga la msilikali.’
14 Zidzakhala zoonekeratu kuti Yehova ali ndi anthu ake,
Ndipo muvi wake udzathamanga ngati mphezi.
Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa adzaliza lipenga,+
Ndipo adzapita ndi mphepo yamkuntho yakumʼmwera.
15 Yehova wa magulu ankhondo akumwamba adzateteza anthu ake.
Adani awo adzawaponyera miyala ndi gulaye,* koma iwo adzawagonjetsa.+
Iwo adzasangalala ndipo adzafuula ngati amwa vinyo.
Adzakhala ngati mbale zolowa zodzaza vinyo,
Ndiponso ngati magazi amene athiridwa mʼmakona a guwa lansembe.+
16 Pa tsiku limenelo, Yehova Mulungu adzapulumutsa nkhosa zake,
Zomwe ndi anthu ake.+
Popeza iwo adzakhala ngati miyala yamtengo wapatali yapachisoti chachifumu yomwe ikunyezimira mʼdziko lake.+
Tirigu adzapatsa mphamvu anyamata,
Ndipo vinyo watsopano adzapatsa mphamvu anamwali.”+