Okhalira Pamodzi mu “Dziko” Lobwezeretsedwa
“Inu mudzatchedwa ansembe a Yehova; anthu adzakuyesani inu atumiki a Mulungu wathu.”—YESAYA 61:6.
1, 2. (a) Kodi mkhalidwe wa otembenuzidwa unali wotani mu Israyeli? (b) Kodi a “khamu lalikulu” asonyeza mzimu wotani m’nthaŵi zamakono?
MU NTHAŴI zakale, pamene Israyeli anali wokhulupirika padziko anachita monga mboni ya ulemerero wa Yehova. (Yesaya 41:8, 9; 43:10) Alendo ambiri anakopeka nakhala olambira Yehova mogwirizana ndi anthu Ake osankhidwa. Kwenikweni, iwo ananena kwa Israyeli zimene Rute ananena kwa Naomi: “Anthu a kwanu ndiwo anthu a kwa inenso, ndi Mulungu wanu ndiye Mulungu wanga.” (Rute 1:16) Iwo anavomereza zofunika za pangano la Chilamulo, amuna anayenera kudulidwa. (Eksodo 12:43-48) Akazi ena anakwatiwa ndi Aisrayeli. Rahabe wa ku Yeriko ndi Rute Mmoabu anakhala makolo achikazi a Yesu Kristu. (Mateyu 1:5) Otembenuka otero anali mbali ya mpingo wa Israyeli.—Deuteronomo 23:7, 8.
2 Lerolino “khamu lalikulu” mofanana ndi otembenuka mu Israyeli lanena kwa otsalira odzozedwa kuti: “Tidzamuka nanu, pakuti tamva kuti Mulungu ali ndi inu.” (Chivumbulutso 7:9; Zekariya 8:23) Amazindikira kuti Akristu odzozedwa ameneŵa ndiwo “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru” wa Yehova, ndipo amagwira nawo ntchito moyandikana kwambiri kwakuti odzozedwawo ndi “nkhosa zina” ali “gulu limodzi, mbusa mmodzi.” (Mateyu 24:45-47; Yohane 10:16) Kodi nchiyani chimene chidzachitika kwa khamu lalikulu pamene abale awo onse odzozedwa alandira mfupo yawo yakumwamba? Iwo sayenera kuwopa. Mu “masiku otsiriza” ano, Yehova wachita makonzedwe kaamba ka nthaŵi imeneyo.—2 Timoteo 3:1.
“Dziko” Lauzimu
3. Kodi “miyamba yatsopano” yoloseredwa ndi Petro nchiyani, ndipo inakhazikitsidwa liti?
3 Makonzedwe akumwamba a kulamulira amene Akristu odzozedwa a 144,000 adzakhala mbali yake analoseredwa ndi mtumwi Petro. Iye anati: “Monga mwa lonjezano lake tiyembekezera miyamba yatsopano, ndi dziko latsopano mmenemo mukhalitsa chilungamo.” (2 Petro 3:13) “Miyamba yatsopano” imeneyi inakhazikitsidwa mu 1914, pamene Kristu anaikidwa pa mpando wachifumu monga Mfumu mu Ufumu wakumwamba. Komano bwanji nanga za “dziko latsopano”?
4. (a) Kodi ndi chochitika chosayembekezereka chotani chimene chinachitika mu 1919? (b) Kodi ‘mtundu wobadwa modzidzimutsa’ unali chiyani ndipo kodi ‘dziko lobadwa’ linali chiyani?
4 Mu 1919, Yehova anatulutsa otsalira odzozedwa mu ukapolo wa Babulo Wamkulu. (Chivumbulutso 18:4) Kwa atsogoleri a Dziko Lachikristu, chochitika chamwadzidzidzi chimenechi sanachiyembekezere konse. Ponena za icho, Baibulo limati: “Ndani anamva kanthu kotereko? Ndani anaona zinthu zoterezo? Kodi dziko lidzabadwa tsiku limodzi? Kodi mtundu udzabadwa modzidzimutsa?” (Yesaya 66:8) Pamene mpingo wa odzozedwa unakhalapo mwadzidzidzi pamaso pa mitundu monga anthu omasulidwa, unalidi mtundu ‘wobadwa modzidzimutsa.’ Komabe, kodi “dziko” limenelo linali chiyani? M’lingaliro lina, linali mkhalidwe wauzimu wolingana ndi dziko la Israyeli wakale. Linali dera la ntchito loperekedwa ku “mtundu” wobadwa chatsopanowo, malo kumene maulosi a Paradaiso wa m’buku la Yesaya akukwaniritsidwa mwauzimu m’nthaŵi yamakono. (Yesaya 32:16-20; 35:1-7; yerekezerani ndi Ahebri 12:12-14.) Kulikonse kumene Mkristu angakhale m’thupi, iyeyo ali mu “dziko” limenelo.
5. Kodi ndi maziko otani amene anakhalapo mu 1919? Fotokozani.
5 Kodi zimenezi zili nchiyani ndi “dziko latsopano” loloseredwa ndi Petro? Chabwino, “mtundu” watsopano umenewo, wobadwa mu 1919 mu “dziko” lobwezeretsedwa, unali kudzakula kukhala gulu la padziko lonse lopangidwa ndi olambira Yehova odzozedwa ndi osadzozedwa. Gulu limeneli lidzapulumuka Armagedo kuloŵa m’dziko latsopano la Mulungu. Mwa njira imeneyi mtundu umenewo ungaonedwe kukhala maziko a chitaganya cha anthu olungama, dziko lapansi latsopano, chimene chidzakhalako pambuyo pa kuwonongedwa kwa dziko la Satana.a Pofika pakati pa ma 1930, odzozedwa, monga kagulu, anali atasonkhanitsidwa m’dziko lobwezeretsedwa. Chiyambire pamenepo, kusonkhanitsidwa kwa khamu lalikulu la nkhosa zina limene lerolino lafika pafupifupi pa mamiliyoni asanu, kwapatsidwa chisamaliro chachikulu. (Chivumbulutso 14:15, 16) Kodi anthu achulukitsitsa mu “dziko” limenelo? Ayi, malire ake akhoza kukuzidwa monga momwe kukufunikira. (Yesaya 26:15) Ndithudi, kuli kokondweretsa kuona chiŵerengero chake cha anthu chikukula pamene otsalira odzozedwa akudzaza “dziko” limenelo ndi “zipatso”—chakudya chauzimu chopatsa thanzi ndi chopereka nyonga. (Yesaya 27:6) Koma kodi a nkhosa zina ameneŵa ali ndi malo otani mu “dziko” lobwezeretsedwa la anthu a Mulungu?
Alendo Okangalika mu ‘Dzikolo’
6. Kodi alendo akhala okangalika motani mu “dziko” la anthu a Mulungu?
6 Monga momwe otembenuka okhala m’dziko la Israyeli anagonjera ku Chilamulo cha Mose, ndimo mmenenso khamu lalikulu lokhala mu “dziko” lobwezeretsedwa lerolino limasonyezera kumvera malamulo a Yehova. Pokhala ophunzitsidwa ndi abale awo odzozedwa, amapeŵa kulambira konyenga kwa mtundu uliwonse ndipo amaona mwazi kukhala wopatulika. (Machitidwe 15:19, 20; Agalatiya 5:19, 20; Akolose 3:5) Amakonda Yehova ndi mtima wawo wonse, nzeru zawo zonse, moyo wawo wonse, ndi mphamvu zawo zonse ndipo amakonda mnansi wawo monga iwo eni. (Mateyu 22:37; Yakobo 2:8) Mu Israyeli wakale otembenuka anathandiza kumanga kachisi wa Solomo ndipo anachirikiza kubwezeretsa kulambira koona. (1 Mbiri 22:2; 2 Mbiri 15:8-14; 30:25) Lerolino, a khamu lalikulu amakhalanso ndi phande m’ntchito zomanga. Mwachitsanzo, iwo amathandiza kupanga mipingo ndi madera, osaphatikizapo ntchito zomanga zakuthupi, monga Nyumba Zaufumu, Nyumba za Misonkhano, ndi nyumba za nthambi.
7. Kodi nchiyani chimene chinachitika mu Yerusalemu wa pambuyo pa ukapolo pamene panalibe Alevi okwanira kuchita utumiki wa pakachisi?
7 Mu 537 B.C.E., pamene Israyeli anabwerako ku undende wa ku Babulo, anayamba kulinganiza utumiki pamalo a kachisi womangidwansoyo. Komabe, Alevi amene anabwerako anali ochepa. Chotero, Anetini—alendo okhala m’dzikolo odulidwa amene poyamba anali othandiza Alevi—anapatsidwa mathayo owonjezereka mu utumiki wa pakachisi. Komabe, iwo sanali ofanana ndi ansembe odzozedwa a mu mzera wa Aroni.b—Ezara 7:24; 8:15-20; Nehemiya 3:22-26.
8, 9. Kodi nkhosa zina zakhala motani ndi mbali yaikulu ya ntchito yopereka utumiki wapatulika mkati mwa masiku otsiriza?
8 Lerolino Akristu odzozedwa atsatira njira imeneyi. Pamene “nthaŵi yachitsiriziro” yapitiriza, otsalira a odzozedwa acheperachepera mu “dziko” la anthu a Mulungu. (Danieli 12:9; Chivumbulutso 12:17) Chifukwa cha zimenezi, khamu lalikulu tsopano likuchita yochuluka ya ntchito ya kupereka “utumiki wopatulika.” (Chivumbulutso 7:15, NW) Potsatira utsogoleri wa abale awo odzozedwa, “[amapereka] chiperekere nsembe yakuyamika Mulungu, ndiyo chipatso cha milomo yovomereza dzina lake.” Iwo ‘samaiŵala kuchitira chokoma ndi kugaŵira ena,’ akumadziŵa kuti “nsembe zotere Mulungu akondwera nazo.”—Ahebri 13:15, 16.
9 Ndiponso, popeza kuti khamu lalikulu likuwonjezereka ndi zikwi mazana ambiri chaka chilichonse, pali kufunika kwa uyang’aniro kowonjezereka. Panthaŵi ina umenewu unachitidwa ndi Akristu odzozedwa okha. Tsopano, uyang’aniro wa mipingo yochuluka, ndiponso madera, zigawo, ndi nthambi, waikiziridwa m’manja mwa nkhosa zina chifukwa cha kusoŵako. Mu 1992 angapo a ameneŵa anapatsidwa mwaŵi wa kukhala pa misonkhano ya makomiti a Bungwe Lolamulira ndi kutumikira monga othandiza osapanga zigamulo. Chikhalirechobe, a nkhosa zinawo ali okhulupirikabe kwa Akristu anzawo odzozedwawo ndipo kuwachirikiza monga kapolo wokhulupirika ndi wanzeru wa Yehova amakuona kukhala mwaŵi.—Mateyu 25:34-40.
“Ngati Shehe”
10, 11. Potsatira chitsanzo cha Afilisti ena, kodi ndimotani mmene ena amene kale anali adani a anthu a Mulungu asinthira mitima? Ndi chotulukapo chotani?
10 Njira imene kapolo wokhulupirika ndi wanzeru wagwiritsirira ntchito nkhosa zina m’malo athayo inaloseredwa pa Zekariya 9:6, 7. Pamenepo timaŵerenga kuti: “Ndidzawononga kudzikuza kwa Afilisti. Ndipo ndidzachotsa mwazi wake m’kamwa mwake, ndi zonyansa zake pakati pa mano ake; momwemo iyenso adzakhala wotsalira wa Mulungu wathu, ndipo adzakhala ngati [shehe, NW] m’Yuda, ndi Ekroni ngati Myebusi.”c Afilisti anali adani enieni a anthu a Yehova, monga momwe dziko la Satana lilili lerolino. (1 Yohane 5:19) Monga momwe potsirizira pake Afilisti anawonongedwera monga mtundu, nalonso dzikoli, pamodzi ndi mbali zake za chipembedzo, zandale, ndi zamalonda, lidzakumana posachedwapa ndi mkwiyo wa Yehova wowononga.—Chivumbulutso 18:21; 19:19-21.
11 Komabe, malinga ndi mawu a Zekariya, Afilisti ena anatembenuka mtima, ndipo zimenezi zinachitira chithunzi kuti anthu ena a m’dziko lerolino sadzapitiriza kukhala paudani ndi Yehova. Adzaleka kupembedza mafano ndi miyambo yake yonyansa ndi nsembe zake zonyansazo ndi kuyeretsedwa pamaso pa Yehova. M’tsiku lathu lino “Afilisti” okonzeka otero akupezeka m’khamu lalikulu.
12. M’nthaŵi zamakono, kodi ndimotani mmene “Ekroni” wakhalira “ngati Myebusi”?
12 Malinga ndi ulosiwo, mzinda waukulu wa Afilisti wa Ekroni udzakhala “ngati Myebusi.” Nawonso Ayebusi panthaŵi ina anali adani a Israyeli. Yerusalemu anali m’manja mwawo kufikira pamene Davide anamulanda. Komabe, ena a awo amene anapulumuka pankhondo ndi Israyeli mwachionekere anakhala otembenuka. Anatumikira m’dziko la Israyeli monga akapolo ndipo analidi ndi mwaŵi wa kugwira ntchito yomanga kachisi. (2 Samueli 5:4-9; 2 Mbiri 8:1-18) Lerolino, “Aekroni” amene amatembenuka kudzalambira Yehova alinso ndi mwaŵi wambiri wa utumiki mu “dziko” loyang’aniridwa ndi kapolo wokhulupirika ndi wanzeru.
13. Kodi ashehe anali ayani m’nthaŵi zakale?
13 Zekariya akunena kuti Mfilisti adzakhala ngati shehe mu Yuda. Liwu Lachihebri lakuti ʼal·luphʹ, pamene litembenuzidwa kuti “shehe,” limatanthauza “mtsogoleri wa chikwi” (kapena, “chiliarch”). Anali malo apamwamba kwambiri. Mtundu woyambirira wa Edomu mwachionekere unali ndi a shehe 13 okha. (Genesis 36:15-19) Liwulo “shehe” silimagwiritsiridwa ntchito kaŵirikaŵiri polankhula za Israyeli, koma mawu akuti “mkulu (kapena, kalonga) wa zikwi” amapezeka kwambiri. Pamene Mose anaitana oimira mtundu wa Israyeli, anapempha “akulu a zikwizo za Israyeli.”d Ameneŵa analipo 12, amene mwachionekere anali pansi pa Mose. (Numeri 1:4-16) Mofananamo, m’gulu la nkhondo, akalonga a zikwi anali achiŵiri kwa kazembe wankhondo kapena kwa mfumu.—2 Samueli 18:1, 2; 2 Mbiri 25:5.
14. Kodi ndimotani mmene “Mfilisti” wakhalira ngati shehe lerolino?
14 Zekariya sanalosere kuti Mfilisti wolapa kwenikweni adzakhala shehe mu Israyeli. Zimenezo sizikanakhala zoyenera, popeza kuti sanali Mwisrayeli weniweni. Koma iye adzakhala ngati shehe, akumakhala m’malo aulamuliro wofanana ndi wa shehe. Ndipo ndimo mmene zakhalira. Pamene otsalira a Akristu odzozedwa akuchepa m’chiŵerengero ndipo ambiri a awo amene akalipobe ali okalamba, a nkhosa zina ophunzitsidwa bwino amathandizira popereŵera, titero kunena kwake. Iwo samafuna kulanda malo abale awo odzozedwawo. Koma kapolo wokhulupirika ndi wanzeru amawapatsa ulamuliro pamene kuli kofunika mu “dziko” limenelo kotero kuti gulu la Mulungu lipitebe patsogolo m’njira yadongosolo. Mchitidwe wapang’onopang’ono wotero ukuonedwa mu ulosi winanso.
Ansembe ndi Alimi
15. (a) M’kukwaniritsidwa kwa Yesaya 61:5, 6, kodi ndani amene ali “ansembe a Yehova,” ndipo ndi liti pamene amatumikira m’malo ameneŵa m’lingaliro lokwanira? (b) Kodi ndani amene ali “alendo” amene amachita ntchito yaulimi ya Israyeli, ndipo—m’lingaliro lauzimu—kodi ntchitoyi imaphatikizaponji?
15 Yesaya 61:5, 6 amati: “Alendo adzaimirira ndi kudyetsa magulu ako, ndi anthu akunja adzakhala olima ako, ndi kukukonzera minda yamphesa. Koma inu mudzatchedwa ansembe a Yehova; anthu adzakuyesani inu atumiki a Mulungu wathu; inu mudzadya chuma cha amitundu, nimudzaloŵa mu ulemerero wawo.” Lerolino, “ansembe a Yehova” ndiwo Akristu odzozedwa. M’lingaliro lonse lokwanira, iwo adzatumikira monga “ansembe a Yehova . . . atumiki a Mulungu wathu,” mu Ufumu wakumwamba. (Chivumbulutso 4:9-11) Kodi ndani amene ali “alendo” okhala ndi thayo la ntchito yaulimi? Ameneŵa ndiwo a nkhosa zina, amene akukhala mu “dziko” la Israyeli wa Mulungu. Kodi nchiyani chimene chili kudyetsa, kulima, ndi kukonzera minda yamphesa imene aikiziridwa? M’lingaliro lofunika kwambiri lauzimu, ntchito zimenezi nzokhudza kuthandiza, kuphunzitsa, ndi kututa anthu.—Yesaya 5:7; Mateyu 9:37, 38; 1 Akorinto 3:9; 1 Petro 5:2.
16. Kodi ndani amene potsirizira pake adzachita ntchito yonse mu “dziko” la anthu a Mulungu?
16 Pakali pano, chiŵerengero chochepa cha Aisrayeli auzimu chidakali pa dziko lapansi chikumakhala ndi phande m’kudyetsa, kulima, ndi kukonzera minda yamphesa kwauzimu. Pamene potsirizira pake mpingo wa odzozedwa wonse ugwirizana ndi Kristu, ntchito yonseyi idzasiyidwa m’manja mwa nkhosa zina. Ngakhale uyang’aniro wakuthupi wa “dziko” limenelo panthaŵiyo udzakhala m’manja mwa nkhosa zina zoyenera, zimene m’buku la Ezekieli zimafotokozedwa kukhala gulu la akalonga.—Ezekieli, machaputala 45, 46.e
“Dziko” Likhalitsa
17. Kodi ndi makonzedwe otani amene Yehova wakhala akulinganiza m’masiku ano otsiriza?
17 Inde, khamu lalikulu siliyenera kuwopa! Yehova walipangira makonzedwe okwanira. Chochitika chofunika kwambiri pa dziko lapansi mkati mwa masiku otsiriza ano chakhala cha kusonkhanitsa ndi kusindikiza chizindikiro odzozedwa. (Chivumbulutso 7:3) Komabe, poona kuti zimenezi zikuchitidwa, Yehova wagwirizanitsa nkhosa zina ndi iwo m’dziko lauzimu lobwezeretsedwa. Mmenemo iwo adyetsedwa mwauzimu ndi kuphunzitsidwa kakhalidwe Kachikritu. Ndiponso, aphunzitsidwa bwino kuchita utumiki wopatulika, kuphatikizapo uyang’aniro. Pa zimenezi iwo akuthokoza kwambiri Yehova ndi abale awo odzozedwa.
18. Kodi ndi pa zochitika zotani pamene nkhosa zina zidzapyola zili zokhulupirika mu “dziko” la Israyeli wauzimu?
18 Pamene Gogi wa ku Magogi aukira anthu a Mulungu kotsiriza, nkhosa zina zidzachirimika limodzi ndi otsalira odzozedwa mu “dziko la midzi yopanda malinga.” Nkhosa zina zidzakhalabe mu “dziko” limenelo, pamene zidzapulumuka chiwonongeko cha mitundu ndi kuloŵa m’dziko latsopano la Mulungu. (Ezekieli 38:11; 39:12, 13; Danieli 12:1; Chivumbulutso 7:9, 14) Mwa kukhalabe okhulupirika, iwo sadzachoka konse m’malo awo osangalatsawo.—Yesaya 11:9.
19, 20. (a) M’dziko latsopano, kodi ndi uyang’aniro waukulu wotani umene nzika za mu “dziko” limenelo zidzakhala nawo? (b) Kodi tikuyembekezeranji ndi chidwi chachikulu?
19 Israyeli wakale analamuliridwa ndi mafumu aumunthu ndipo anali ndi ansembe Achilevi. M’dziko latsopano, Akristu adzakhala ndi uyang’aniro waukulu koposa. Pansi pa Yehova Mulungu, iwo adzakhala ogonjera kwa Mkulu wa Ansembe ndi Mfumu, Yesu Kristu, ndi kwa ansembe ndi mafumu anzake a 144,000—amene ena a iwo anali kuwadziŵa monga abale ndi alongo awo Achikristu pa dziko lapansi. (Chivumbulutso 21:1) Nzika zokhulupirika za m’dziko lauzimulo zidzakhala pa dziko lapansi lobwezeretsedwa ku paradaiso weniweni, zikumakondwera ndi madalitso ochiritsa operekedwa kudzera mu Yerusalemu Watsopano.—Yesaya 32:1; Chivumbulutso 21:2; 22:1, 2.
20 Pamene galeta lakumwamba la Yehova laulemerero likupita patsogolo mosaletseka kuti likwaniritse zifuno zake, tonsefe tikuyembekezera ndi chidwi chachikulu kudzakwaniritsa gawo lathu. (Ezekieli 1:1-28) Pamene zifuno zimenezo zikwaniritsidwa, lingalirani za chisangalalo chimene chidzakhalapo pa kuyeretsedwa kwa Yehova kwa chipambano! Panthaŵiyo nyimbo yaikulu yolembedwa pa Chivumbulutso 5:13 idzaimbidwa ndi zolengedwa zonse: “Kwa Iye wakukhala pa mpando wachifumu, ndi kwa Mwanawankhosa zikhale chiyamiko, ndi ulemu, ndi ulemerero, ndi ufumu, kufikira nthaŵi za nthaŵi”! Kaya malo athu adzakhala kumwamba kapena pa dziko lapansi, kodi sitikulakalaka kudzakhalapo, tikumagwirizana ndi ena m’nyimbo yaulemerero yachitamando imeneyo?
[Mawu a M’munsi]
a Onani “New Heavens and a New Earth,” lofalitsidwa mu 1953 ndi Watchtower Bible and Tract Society of New York, Inc., masamba 322-3.
b Ngati mufuna malongosoledwe onse, onani nkhani yakuti “‘Opatsidwa’ Ali Mphatso ya Yehova” m’kope la Nsanja ya Olonda la April 15, 1992.
c Onani Paradise Restored to Mankind—By Theocracy!, lofalitsidwa mu 1972 ndi Watchtower Bible and Tract Society of New York, Inc., masamba 264-9.
d Chihebri: raʼ·shehʹ ʼal·phehʹ Yis·ra·ʼelʹ, lotembenuzidwa kuti khi·liʹar·khoi Is·ra·elʹ (“chiliarchs of Israel”) mu Septuagint.
e Onani “The Nations Shall Know That I Am Jehovah”—How?, lofalitsidwa mu 1971 ndi Watchtower Bible and Tract Society of New York, Inc., masamba 401-7.
Kodi Mungayankhe Motani?
◻ Kodi ndi “dziko” lotani limene linabwezeretsedwa mu 1919, ndipo linadzazidwa motani ndi nzika zake?
◻ Kodi nkhosa zina zapatsidwa motani mathayo owonjezereka mu “dziko” la anthu a Mulungu obwezeretsedwa?
◻ Kodi ziŵalo za khamu lalikulu zili “ngati Myebusi” m’njira yotani? zili “ngati shehe m’Yuda” motani?
◻ Kodi nkhosa zina zokhulupirika zidzakhala mu “dziko” limenelo kwautali wotani?
[Chithunzi patsamba 23]
Mfilisti wamakono adzakhala “ngati shehe m’Yuda”
[Zithunzi patsamba 24]
Odzozedwa ndi nkhosa zina amatumikira pamodzi m’dziko lauzimu