Ekisodo
4 Koma Mose anayankha kuti: “Bwanji ngati sakandikhulupirira komanso kumvera mawu anga?+ Chifukwatu adzanena kuti, ‘Yehova sanaonekere kwa iwe.’” 2 Kenako Yehova anamufunsa kuti: “Chili mʼdzanja lakocho nʼchiyani?” Mose anayankha kuti: “Ndodo.” 3 Ndiyeno iye anati: “Iponye pansi.” Iye anaiponya pansi ndipo inasanduka njoka.+ Zitatero Mose anayamba kuthawa. 4 Ndiyeno Yehova anauza Mose kuti: “Igwire kumchira.” Choncho Mose anaigwira ndipo inasandukanso ndodo mʼdzanja lake. 5 Kenako Mulungu anati: “Ukachite zimenezi kuti akakhulupirire kuti Yehova Mulungu wa makolo awo, Mulungu wa Abulahamu, Mulungu wa Isaki ndi Mulungu wa Yakobo,+ anaonekera kwa iwe.”+
6 Yehova anamuuzanso kuti: “Lowetsa dzanja lako mʼmalaya, pachifuwa.” Choncho Mose analowetsa dzanja lake mʼmalaya. Koma atalitulutsa, anaona kuti dzanja lakelo lachita khate ndipo likuoneka loyera kwambiri.+ 7 Ndiyeno Mulungu anati: “Lowetsanso dzanja lako mʼmalayamo.” Choncho analowetsanso dzanja lake mʼmalaya. Atalitulutsa anaona kuti lakhalanso bwino ngati poyamba. 8 Mulungu anamuuza kuti: “Ngati sakakukhulupirira kapena kulabadira chizindikiro choyamba, akakhulupirira chizindikiro chachiwirichi.+ 9 Komabe ngati sakakhulupirira zizindikiro ziwirizi nʼkumvera mawu ako, ukatenge madzi amumtsinje wa Nailo nʼkuwathira panthaka youma. Ndipo madzi amene ukatenge mumtsinje wa Nailowo adzasanduka magazi panthakapo.”+
10 Ndiyeno Mose anauza Yehova kuti: “Pepani Yehova, ine kulankhula kumandivuta kuyambira kalekale. Komanso panopa pamene mukulankhula ndi ine mtumiki wanu, ndikulankhula movutikira* chifukwa ndine wa lilime lolemera.”+ 11 Pamenepo Yehova anamuuza kuti: “Anapatsa munthu pakamwa ndi ndani, kapena ndi ndani amene ali ndi mphamvu zopangitsa munthu kukhala wosalankhula, wogontha, woona kapena wosaona? Kodi si ine, Yehova? 12 Choncho pita, ndipo ukamakalankhula ine ndidzakhala nawe* ndipo ndidzakuuza zoti unene.”+ 13 Koma Mose anati: “Pepani Yehova, chonde, tumizani wina aliyense amene mukufuna kumutumiza.” 14 Zitatero, Yehova anakwiyira kwambiri Mose ndipo anati: “Kodi si paja Aroni+ Mlevi uja ndi mʼbale wako? Ndikudziwa kuti amalankhula bwino kwambiri. Ndiponso, iye ali mʼnjira kudzakuchingamira. Akakuona, adzakondwera kwambiri mumtima mwake.+ 15 Choncho ukalankhule naye ndi kumuuza zoti akanene.+ Ineyo ndidzakhala ndi iwe pamodzi ndi iye mukamakalankhula+ ndipo ndidzakuuzani zochita. 16 Iyeyo ndi amene azikalankhula kwa anthu mʼmalo mwa iwe. Choncho adzakhala wokulankhulira, ndipo iwe udzakhala ngati Mulungu kwa iye.+ 17 Ndodo iyi izikakhala mʼdzanja lako ndipo uzikaigwiritsa ntchito pochita zizindikiro.”+
18 Choncho Mose anapita kwa Yetero apongozi ake+ nʼkuwauza kuti: “Ndikufuna kupita kwa abale anga ku Iguputo kuti ndikaone ngati adakali moyo.” Choncho, Yetero anayankha Mose kuti: “Pita mu mtendere.” 19 Ndiyeno Yehova anamuuza Mose ali ku Midiyani kuti: “Nyamuka, bwerera ku Iguputo, chifukwa onse amene ankafuna kukupha* anafa.”+
20 Kenako Mose anatenga mkazi wake ndi ana ake nʼkuwakweza pabulu, ndipo anayamba ulendo wobwerera ku Iguputo. Komanso Mose anatenga ndodo ya Mulungu woona mʼdzanja lake. 21 Yehova anauzanso Mose kuti: “Ukakafika ku Iguputo ukaonetsetse kuti wachita pamaso pa Farao, zodabwitsa zonse zimene ndakupatsa mphamvu kuti ukachite.+ Koma ine ndidzamulola kuti aumitse mtima wake,+ moti sadzalola anthu anga kuchoka.+ 22 Ukauze Farao kuti, ‘Yehova wanena kuti: “Isiraeli ndi mwana wanga wamwamuna, mwana wanga woyamba kubadwa.+ 23 Ndikukuuza kuti, Lola mwana wanga apite kuti akanditumikire. Koma ngati ukukana kumulola kuti apite, ndidzapha mwana wako wamwamuna, mwana wako woyamba kubadwa.”’”+
24 Ndiyeno ali pa ulendowo, atafika pamalo oti agone, Yehova+ anakumana naye ndipo ankafuna kumupha.+ 25 Zitatero, Zipora+ anatenga mwala wakuthwa* nʼkumudula mwana wakeyo. Ndipo khungu analidulalo analiponya pansi ndipo linakhudza mapazi ake. Kenako ananena kuti: “Popeza ndinu mkwati wa magazi kwa ine.” 26 Atatero, Mulungu anamusiya. Pamenepo Zipora anati, “mkwati wa magazi,” chifukwa cha mdulidwewo.
27 Kenako Yehova anauza Aroni kuti: “Pita kuchipululu kukachingamira Mose.”+ Choncho Aroni ananyamuka ndipo anakumana ndi Mose paphiri la Mulungu woona,+ ndipo anamulonjera nʼkumukisa.* 28 Atakumana, Mose anauza Aroni mawu onse a Yehova, yemwe anamutuma.+ Anamuuzanso zizindikiro zonse zimene anamulamula kuti achite.+ 29 Kenako Mose ndi Aroni anapita kukasonkhanitsa akulu onse a Aisiraeli.+ 30 Aroni anawauza mawu onse amene Yehova anauza Mose, ndipo Mose anachita zizindikiro+ pamaso pa anthuwo. 31 Zitatero anthuwo anakhulupirira+ Mose. Atamva kuti Yehova akufuna kuthandiza Aisiraeli+ komanso kuti waona mavuto amene akukumana nawo,+ anagwada nʼkuwerama mpaka nkhope zawo pansi.