Numeri
19 Yehova analankhulanso ndi Mose komanso Aroni kuti: 2 “Ili ndi lamulo limene Yehova wapereka, ‘Uzani Aisiraeli kuti akupatseni ngʼombe yaikazi yofiira, yathanzi komanso yopanda chilema+ yomwe sinamangidwepo goli. 3 Mupereke ngʼombeyo kwa wansembe Eleazara kuti apite nayo kunja kwa msasa, ndipo kumeneko ikaphedwe pamaso pake. 4 Akatero wansembe Eleazara atenge ena mwa magazi a ngʼombeyo ndi chala chake nʼkuwawaza chakutsogolo kwa chihema chokumanako maulendo 7.+ 5 Kenako ngʼombeyo iwotchedwe iyeyo akuona. Awotche chikopa chake, nyama yake, magazi ake, limodzi ndi ndowe zake.+ 6 Wansembeyo atenge mtengo wa mkungudza, kamtengo ka hisope+ ndi ulusi wofiira kwambiri nʼkuziponya pamoto umene akuwotcherapo ngʼombeyo. 7 Akatha, wansembeyo achape zovala zake nʼkusamba* ndi madzi. Pambuyo pake akhoza kulowa mumsasa, koma adzakhala wodetsedwa mpaka madzulo.
8 Munthu amene anawotcha ngʼombeyo achape zovala zake nʼkusamba* ndi madzi, ndipo adzakhala wodetsedwa mpaka madzulo.
9 Ndiyeno munthu amene si wodetsedwa awole phulusa la ngʼombeyo+ nʼkukalisiya pamalo oyera kunja kwa msasawo. Aisiraeli onse azisunga phulusalo kuti aziligwiritsa ntchito pokonza madzi oyeretsera.+ Imeneyi ndi nsembe yamachimo. 10 Munthu amene wawola phulusa la ngʼombeyo azichapa zovala zake ndipo azikhala wodetsedwa mpaka madzulo.
Limeneli ndi lamulo mpaka kalekale kwa Aisiraeli komanso kwa mlendo wokhala pakati pawo.+ 11 Aliyense wokhudza mtembo wa munthu aliyense, azikhala wodetsedwa kwa masiku 7.+ 12 Munthu woteroyo azidziyeretsa ndi madzi oyeretsera aja pa tsiku lachitatu, ndipo pa tsiku la 7 azikhala woyera. Koma akapanda kudziyeretsa pa tsiku lachitatu, sadzakhala woyera pa tsiku la 7. 13 Munthu aliyense amene wakhudza mtembo wa munthu, koma sanadziyeretse, wadetsa chihema cha Yehova.+ Munthu ameneyo aziphedwa kuti asakhalenso pakati pa Isiraeli.+ Iye adakali wodetsedwa chifukwa sanawazidwe madzi oyeretsera.+ Choncho adzakhalabe wodetsedwa.
14 Ngati munthu wafera mutenti, lamulo lake ndi ili: Munthu aliyense amene walowa mutentimo komanso aliyense amene anali mutenti momwemo, adzakhala wodetsedwa kwa masiku 7. 15 Chiwiya chilichonse chosavundikira bwino* ndi chodetsedwa.+ 16 Aliyense amene wakhudza munthu amene waphedwa ndi lupanga kunja kwa msasa, kapena mtembo, fupa la munthu, kapenanso manda, adzakhala wodetsedwa kwa masiku 7.+ 17 Munthu wodetsedwayo amutapireko phulusa la nsembe yamachimo imene inawotchedwa ija. Phulusalo aliike mʼchiwiya nʼkuthiramo madzi akumtsinje. 18 Ndiyeno munthu amene si wodetsedwa+ azitenga kamtengo ka hisope+ nʼkukaviika mʼmadzimo kenako aziwaza tentiyo, ziwiya zonse ndi anthu onse amene anali mutentiyo. Komanso aziwaza munthu amene anakhudza fupa la munthu, munthu amene waphedwa, mtembo kapena manda. 19 Munthu amene si wodetsedwa uja awaze munthu wodetsedwayo madziwo pa tsiku lachitatu komanso pa tsiku la 7.+ Ndipo pa tsiku la 7 lomwelo amuyeretse ku tchimo lake. Kenako amene akuyeretsedwayo achape zovala zake nʼkusamba ndi madzi, ndipo madzulo ake adzakhala woyera.
20 Koma munthu wodetsedwa akapanda kudziyeretsa, aziphedwa kuti asakhalenso mumpingowo,+ chifukwa wadetsa malo opatulika a Yehova. Iye sanawazidwe madzi oyeretsera, choncho ndi wodetsedwa.
21 Limeneli likhale lamulo kwa iwo mpaka kalekale: Munthu amene anawaza madzi oyeretsera,+ azichapa zovala zake. Ndipo munthu amene angakhudze madzi oyeretserawo azikhala wodetsedwa mpaka madzulo. 22 Chinthu chilichonse chimene munthu wodetsedwayo angakhudze, chizikhala chodetsedwa. Komanso munthu amene angakhudze chinthucho, azikhala wodetsedwa mpaka madzulo.’”+