1 Mbiri
29 Mfumu Davide anauza mpingo wonse kuti: “Solomo mwana wanga, amene Mulungu wamusankha,+ ndi wamngʼono ndipo sadziwa zambiri.+ Ntchitoyi ndi yaikulu chifukwa si kachisi* wa munthu koma wa Yehova Mulungu.+ 2 Ine ndayesetsa mwakhama kukonzekera nyumba ya Mulungu wanga. Ndapereka golide wodzapangira zinthu zagolide, siliva wodzapangira zinthu zasiliva, kopa* wodzapangira zinthu zakopa, zitsulo zodzapangira zinthu zachitsulo+ ndi matabwa+ odzapangira zinthu zamatabwa. Ndaperekanso miyala ya onekisi, miyala yomanga ndi simenti, miyala yokongoletsera, miyala yamtengo wapatali yamitundu yonse ndiponso miyala yambiri ya alabasitala. 3 Komanso chifukwa chakuti ndikusangalala ndi nyumba ya Mulungu wanga,+ kuwonjezera pa zonse zimene ndakonzekera zokhudza nyumba yopatulikayo, ndikupereka kunyumba ya Mulungu wanga chuma changa+ chomwe ndi golide ndi siliva. 4 Ndikupereka matalente* 3,000 a golide wa ku Ofiri,+ matalente 7,000 a siliva woyengedwa bwino wodzakutira makoma a nyumba, 5 golide wodzapangira zinthu zagolide, siliva wodzapangira zinthu zasiliva ndi siliva woti amisiri adzagwiritse ntchito. Tsopano ndani lero wakonzeka kupereka mphatso kwa Yehova?”+
6 Choncho akalonga a nyumba za makolo, akalonga a mafuko a Aisiraeli, atsogoleri a magulu a anthu 1,000 ndi a magulu a anthu 100+ ndiponso atsogoleri oyangʼanira ntchito za mfumu,+ anabwera nʼkuyamba kupereka zinthu mwa kufuna kwawo. 7 Iwo anapereka golide wokwana matalente 5,000, madariki* 10,000, siliva wokwana matalente 10,000, kopa wokwana matalente 18,000 ndi zitsulo zokwana matalente 100,000. Anapereka zonsezi kuti zigwire ntchito panyumba ya Mulungu woona. 8 Munthu aliyense amene anali ndi miyala yamtengo wapatali anaipereka ku chuma chapanyumba ya Yehova, chomwe Yehiela+ mbadwa ya Gerisoni+ ankayangʼanira. 9 Anthuwo anasangalala chifukwa cha nsembe zaufulu zimene anapereka, chifukwa anapereka nsembezo kwa Yehova ndi mtima wonse.+ Nayenso Mfumu Davide anasangalala kwambiri.
10 Kenako Davide anatamanda Yehova pamaso pa mpingo wonse kuti: “Mutamandidwe inu Yehova Mulungu wa Isiraeli atate wathu, kuyambira kalekale mpaka kalekale. 11 Inu Yehova, ukulu,+ mphamvu,+ kukongola, ulemerero ndi ulemu+ ndi zanu, chifukwa zinthu zonse zakumwamba ndi zapadziko lapansi ndi zanu.+ Ufumu ndi wanu, inu Yehova.+ Ndinu Wokwezeka ndiponso ndinu mutu pa onse. 12 Chuma ndi ulemerero zimachokera kwa inu.+ Inu mumalamulira chilichonse.+ Mʼdzanja lanu muli mphamvu+ ndi nyonga+ ndipo dzanja lanu limatha kukweza+ ndiponso kupereka mphamvu kwa onse.+ 13 Tsopano inu Mulungu wathu, tikukuyamikani ndi kutamanda dzina lanu lokongola.
14 Ndine ndani ine ndipo anthu anga ndani kuti tithe kupereka nsembe zaufulu ngati zimenezi? Chifukwa chilichonse nʼchochokera kwa inu ndipo tapereka kwa inu zochokera mʼdzanja lanu. 15 Ifetu ndife alendo pamaso panu, komanso okhala mʼdziko la eni ngati mmene analili makolo athu onse.+ Masiku athu padziko lapansi ali ngati mthunzi+ ndipo ndife osakhalitsa. 16 Inu Yehova Mulungu wathu, chuma chonse chimene takonzekera kuti tikumangireni nyumba ya dzina lanu loyera nʼchochokera mʼdzanja lanu ndipo zonse ndi zanu. 17 Inu Mulungu wanga, ine ndikudziwa bwino kuti mumafufuza mitima+ ndiponso kuti mumakonda anthu okhulupirika.+ Ineyo ndapereka zinthu zonsezi mwakufuna kwanga komanso ndi mtima wopanda chinyengo. Ndasangalala kwambiri kuona anthu anu ali apawa, akupereka zopereka zawo mwakufuna kwawo. 18 Inu Yehova Mulungu wa Abulahamu, Isaki ndi Isiraeli makolo athu, thandizani anthu anuwa kuti akhale ndi mtima wodzipereka woterewu mpaka kalekale ndiponso kuti azikutumikirani ndi mtima wawo wonse.+ 19 Mupatse Solomo mwana wanga mtima wathunthu+ kuti asunge malamulo anu,+ zikumbutso zanu komanso kuti achite zinthu zonsezi nʼkumanga kachisi* amene zipangizo zake ndakonzeratu.”+
20 Kenako Davide anauza mpingo wonse kuti: “Tsopano tamandani Yehova Mulungu wanu!” Choncho anthu onsewo anayamba kutamanda Yehova Mulungu wa makolo awo ndipo anagwadira Yehova ndi mfumu nʼkuwerama mpaka nkhope zawo kufika pansi. 21 Anthuwo anayamba kupereka nsembe kwa Yehova ndipo anapereka nsembe zopsereza+ kwa Yehova mpaka tsiku lotsatira. Anapereka ngʼombe zamphongo zazingʼono 1,000, nkhosa zamphongo 1,000, ana a nkhosa amphongo 1,000 ndi nsembe zake zachakumwa.+ Iwo anapereka nsembe zambirimbiri za Aisiraeli onse.+ 22 Pa tsikulo, iwo anadya ndi kumwa mosangalala kwambiri+ pamaso pa Yehova. Kachiwirinso, anaveka Solomo mwana wa Davide ufumu ndipo anamudzoza pamaso pa Yehova kukhala mtsogoleri.+ Anadzozanso Zadoki kukhala wansembe.+ 23 Choncho, Solomo anakhala pampando wachifumu wa Yehova+ monga mfumu mʼmalo mwa Davide bambo ake ndipo zinthu zinkamuyendera bwino. Aisiraeli onse ankamumvera. 24 Akalonga onse,+ asilikali amphamvu+ ndiponso ana onse a Mfumu Davide,+ ankagonjera Solomo mfumu. 25 Yehova anakweza kwambiri Solomo pamaso pa Aisiraeli onse nʼkumupatsa ulemu waukulu wachifumu kuposa mfumu ina iliyonse imene inalamulira Isiraeli iye asanakhale mfumu.+
26 Choncho Davide mwana wa Jese analamulira Isiraeli yense. 27 Nthawi yonse imene iye analamulira Isiraeli inali zaka 40. Ku Heburoni analamulira zaka 7+ ndipo ku Yerusalemu analamulira zaka 33.+ 28 Kenako iye anamwalira ali wokalamba,+ atakhala ndi moyo wautali, chuma ndiponso ulemerero. Ndiyeno mwana wake Solomo anakhala mfumu mʼmalo mwake.+ 29 Nkhani zokhudza Mfumu Davide, kuyambira pachiyambi mpaka kumapeto, zikupezeka mʼzinthu zimene analemba Samueli wamasomphenya,* mneneri Natani+ ndiponso Gadi+ wamasomphenya. 30 Analembanso nkhani zonse zokhudza ufumu wake, mphamvu zake, zinthu zimene zinachitika pa moyo wake ndiponso zomwe zinachitikira Aisiraeli onse ndi maufumu onse owazungulira.